Kasambidwe Ka Sunnah-Gawo 4

14. Onetsetsani kuti madzi akufika pena paliponse pathupi lanu, nthawi ina iliyonse mukadzithira madzi dzinyureni ndicholinga chofuna kuonetsetsa kuti madziwo alowa pakhungu lonse, ngakhale kutangotsala malo ochepetsetsa kwambiri osathiridwa madzi, kusamba (kwa fardh) sikudzatheka, pamene mukusambitsa thupi, sambitsani kutsogolo kwake kenako kumbuyo.[1]

عن علي رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال من ترك موضع شعرة من جنابة لم يغسلها فعل بها كذا وكذا من النار قال علي فمن ثم عاديت رأسي ثلاثا وكان يجز شعره (سنن أبي داود، الرقم: ٢٤٩)

Sayyiduna Ali radhiyallahu anhu akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, yemwe ali ndi janabah (akufunikira kusamba kokakamizidwa) nasiya kagawo kamodzi kosafikira madzi pathupi lake ngakhale katakhala kamulingo watsitsi limodzi, malo amenewo adzapatsidwa chilango chakuti chakuti, “nchifukwa chake sindimakonda kusunga tsitsi.’’ Zanenedwa kuti Aliy (radhiyallahu anhu) ankameta tsitsi (poopa kuti malo ena ake angatsale osafikiridwa madzi akamasamba pasapezeke tsitsi louma zomwe zingapangitse kuti kusamba kusakwanile).[2]

15. Musaononge madzi mukamasamba, pasagwiritsidwe ntchito madzi ochuluka, madzi ochepanso omwe sangakwanire kusamba asagwiritsidwe ntchito.

عن عبد الله بن محمد بن عقيل بن أبي طالب عن أبيه عن جده رضي الله عنهم قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم يجزئ من الوضوء مد ومن الغسل صاع فقال رجل لا يجزئنا فقال قد كان يجزئ من هو خير منك وأكثر شعرا يعني النبي صلى الله عليه وسلم (سنن ابن ماجة، الرقم: ٢٧٠)[3]

Sayyiduna Aqeel bin Abi Taalib (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, madzi okwana mudd imodzi ndi okwanira kupangira wudhu, ndipo sa’a imodzi yamadzi ndiyokwanira kusamba. “pakunva zimenezimunthu wina adati, madzi oterowo sangakwanire kusamba’’  Sayyiduna Aqeel (radhiyallah anhu) adanchenjeza munthu uja nati,’’ (madzi oterewo) ankamukwanira yemwe anali opambana kuposa iweyo ndipo anali nditsitsi lochuluka kuposa iweyo (ankatanthauza Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ’mudd ndi sa’a ndimitundu yamilingo yoyesera.

16. Musayankhule kapena kuimba ndikukambirana nkhani zina pamene mukusamba.[4]

17. Musatenge nthawi yaitali kubafa, makamaka ngati bafalo ndilogwiritsidwa ntchito ndi anthu ambiri.[5]

18. Musanyasitse kubafa nditsitsi lamalo obisika.[6]

19. Ganiziraninso ena mukamagwiritsa ntchito madzi otentha. Musagwiritse ntchito madzi ochuluka moti ena omwe angabwere pambuyo panu asapeze madzi okwanira otentha.[7]

20. Pamapeto posamba ndibwino kulisiya thupi lanu (osapukuta) kuti liume lokha. Koma ngati mwakakamizika kuti mudzipukute ndithaulo, m udzaloredwa kutero.[8]

21. Fulumirani kubisa thupi lanu mukamaliza kusamba.[9]

22. Musakodzere kubafa.[10]


[1] يفيض الماء على (شقه الأيمن) مقدمه ثم مؤخره (ثم) بعد فراغه منه جميعه يفيضه على شقه (الأيسر) كذلك (تحفة المحتاج ١/٢٩٦)

[2] سكت الحافظ عن هذا الحديث في الفصل الثاني من هداية الرواة (١/٢٣٥) فالحديث حسن عنده

[3] قال البوصيري في الزوائد (١/٩٩): إسناده ضعيف لضعف حبان ويزيد

لهذا الحديث شاهد من حديث ابن عباس قال قال رجل كم يكفيني للوضوء قال مد قال كم يكفيني للغسل قال صاع قال فقال الرجل لا يكفيني فقال لا أم لك قد كفى من هو خير منك رسول الله صلى الله عليه وسلم رواه أحمد والبزار والطبراني في الكبير ورجاله ثقات (مجمع الزوائد الرقم: ١٠٩٩)

[4] كذا يسن … وترك نفض وتنشف واستعانة وتكلم لغير عذر (تحفة المحتاج ١/٢٩٧)

[5] اتفق أصحابنا وغيرهم على ذم الإسراف في الماء في الوضوء والغسل وقال البخاري في صحيحه كره أهل العلم الإسراف فيه والمشهور أنه مكروه كراهة تنزيه وقال البغوي والمتولي حرام (المجموع شرح المهذب ٢/١٥٢)

[6] يحرم الانتفاع بشعر الآدمي وسائر أجزائه لكرامته بل يدفن شعره وظفره وسائر أجزائه (المجموع شرح المهذب ٣/١٠٣)

[7] عن عبد الله بن عمرو رضي الله عنهما عن النبي صلى الله عليه وسلم قال المسلم من سلم المسلمون من لسانه ويده والمهاجر من هجر ما نهى الله عنه (صحيح البخاري، الرقم: ١٠)

[8] كذا يسن … وترك نفض وتنشف (تحفة المحتاج ١/٢٩٧)

[9] عن زرعة بن مسلم بن جرهد الأسلمي عن جده جرهد قال مر النبي صلى الله عليه وسلم بجرهد في المسجد وقد انكشف فخذه فقال إن الفخذ عورة هذا حديث حسن ما أرى إسناده بمتصل (سنن الترمذي، الرقم: ٢٧٩٥)

[10] عن عبد الله بن مغفل أن النبي صلى الله عليه وسلم نهى أن يبول الرجل في مستحمه وقال إن عامة الوسواس منه (سنن الترمذي، الرقم: ٢١)

Check Also

Kasambidwe Ka Sunnah Gawo 2

5. Yambani ndi kuwerenga Bismillah mukamasamba, ndikupanga niya yoti mukuchotsa hadathil akbar (unve waukulu).

6. Sambitsani zikhatho zanu katatu.