Kuyesedwa Kwa Durood Pa Mlingo Wokwanira

عن أبي هريرة رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم من سره أن يكتال بالمكيال الأوفى إذا صلى علينا أهل البيت فليقل اللهم صل على محمد النبي الأمي وأزواجه أمهات المؤمنين وذريته وأهل بيته كما صليت على آل إبراهيم إنك حميد مجيد (سنن أبي داود، الرقم: ٩٨٢، وسكت عليه هو والمنذري في مختصره، الرقم: ٩٨١)

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, amene akufuna kuti Durood yake ikaikidwe pa sikelo ndikukalemera kwambiri kuti munthu akalandire mphotho yochuluka akatiwerengera Durood adzichulukitsa kuwerenga Durood iyi:

اَللّٰهُمَّ صَلِّ عَلٰى مُحَمَّدٍ النَّبِيِّ الْأُمِّيِّ وَأَزْوَاجِهِ أُمَّهَاتِ الْمُؤْمِنِيْنَ وَذُرِّيَّتِهِ وَأَهْلِ بَيْتِهِ كَمَا صَلَّيْتَ عَلٰى آلِ إِبْرَاهِيْمَ إِنَّكَ حَمِيْدٌ مَجِيْدٌ

Oh Allah! Tumizani Durood kwa Muhammad (sallallahu alaih wasallam), Mtumiki amene anali osatha kulemba ndi kuwerenga, akazi ake onse, amayi a anthu onse omwe ndi okhulupilira, akubanja kwake ndi fuko lake lonse monga munatumizira Durood ku banja la nabi Ibrahim alaih salaam, ndinthudi ndiinu otamandidwa komanso olemekezeka.

Ulemu wa Imaam Maalik rahimahullah

Imaam Maalik (rahimahullah) ankaukonda nzinda wa Madinah Munawwarah kwambiri, ankaukonda nzindawu chifukwa chomukonda Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kwambiri.

Allaamah Ibnu Khallikaan (rahimahullah adalemba) kuti:

Imaam Maalik (rahimahullah) sadakweleko chokwera munzinda olemekezeka wa Madinah Munawwarah. Ngakhale pamene adakalamba kufikira kuti adafooka kukanika Kuyenda chifukwa chokalamba, adasankha Kuyenda wapansi Kusiyana ndikukwera chokwera, Imaam Malik (rahimahullah) atafunsidwa kuti ndi chifukwa chiyani amachita zimenezi, iye adayankha kuti, zimandivuta Kuyenda mu nzinda wa Madinah ndiri pa chokwera kumachita kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adagonekedwa mu nthaka imeneyi yamunzinda wa Madinah. (Wafayat Ul Aa’yaan, 136/4)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …