Zikhulupiliro Zokhudza Atumiki a Mulungu (alaihim Salaam)

1. Allah Ta’ala adatumiza atumiki osiyanasiyana kumayiko kuti awatsogolere anthu kunjira yowongoka.[1] 

2. Mtumiki ankachita kusankhidwa ndi Allah Ta’ala. Allah Ta’ala ankasankha mwa akapolo ake amene wamufuna pantchito yotamandikayi. Utumiki sungapezeke ndimunthu aliyense kudzera mu ntchito zake ndikulimbikira kwake ayi (koma umachokera kwa Allah Taala).[2] 

3. Mtumiki amene adapatsidwa bukhu ndi malamulo ameneyo pacharabu amatchedwa kuti Rasuul ndipo mtumiki amene sadapatsidwe bukhu ndi malamulo ashariya koma nalamuridwa kutsatira bukhu ndi shariya yamtumiki yemwe adabwera kale amatchedwa Nabi.[3] 

4. Atumiki ndi anthu amene adali omvera kwambiri Allah Ta’ala kuposa aliyense. Sadanyozepo Allah Ta’ala nthawi zonse.[4] 

5. Atumiki onse (alaihim salaam) ndi otetezeka ku Mchitidwe wa machimo, kotero atumiki onse alibe tchimo.[4] 


[١] (وقد أرسل الله تعالى رسلا من البشر إلى البشر مبشرين) لأهل الإيمان والطاعة بالجنة والثواب (ومنذرين) لأهل الكفر والعصيان بالنار والعقاب فإن ذلك مما لا طريق للعقل إليه وإن كان فبأنظار دقيقة ولا يتيسر إلا لواحد بعد واحد (ومبينين للناس ما يحتاجون إليه من أمور الدنيا والدين) (شرح العقائد النسفية صـ ١٦٠)

[٢] اَللّٰهُ يَصْطَفِىْ مِنَ ٱلْمَلٰئِكَةِ رُسُلًا وَّمِنَ النَّاسِ ط اِنَّ اللّٰـهَ سَمِيْعٌ م بَصِيْرٌ (سورة الحج: ٧٥)

والبعثة لتضمنها مصالح لا تحصى لطف من الله تعالى ورحمة يختص بها من يشاء من عباده من غير وجوب عليه خلافا للمعتزلة ( شرح المقاصد صـــــ 5/5)

[٣] والرسول إنسان بعثه الله تعالى إلى الخلق لتبليغ الأحكام وقد يشترط فيه الكتاب بخلاف النبي فإنه أعم (شرح العقائد النسفية صـ ٤٠)

الرسول له شريعة وكتاب فيكون أخص من النبي (شرح المقاصد ٥/٦، شرح الفقه الأكبر لابن المنتهي صـ 105)

[4] والأنبياء عليهم الصلاة والسلام كلهم منزهون عن الصغائر والكبائر والكفر والقبائح (الفقه الأكبر صـ ٥٦)

Check Also

Zikhulupiliro zokhudza mabukhu a Allah

1. Allah Ta’ala adavumbulutsa mabukhu osiyanasiyana kwa aneneri osiyanasiyana (ntendere wa Allah upite kwa iwo)kuti …