Ndi dongosolo la Allah Ta’ala kuti anadalitsa zinthu zina kuposa zinzake, mwa anthu onse, aneneri ndi omwe adadalitsika kwambiri popatsidwa ulemelero wa pamwamba kwambiri kuposa anthu ena onse, malo onse osiyanasiyana omwe alipo padziko lapansi pano Allah adaidalitsa haramain (Makkah Mukarramah ndi Madinah Munawwarah) kuphatikizapo Aqsa, ndipo pa miyezi 12 ya pachaka mu kalendala ya chisilamu miyezi inayi ndiimene ili yodalitsika ndipo ndi Zul-Qa’dah, Zul-Hijjah, Muharram komanso Rajab, chimodzimodzinso m’masiku achisilamu tsiku la Aashurah ladilitsika kwambiri ndikupatsidwa ulemelero kuposa masiku ena onse. pamene mwezi wa Zul-hijjah udasankhidwa kuti ndimwezi umene uli okwaniritsa ibadah ina yapaderadera a Hajj, mwezi wa muharram ndi odala popeza ukutchuridwa kuti ndimwezi wa Allah komanso komanso mwezi umene uli nditsiku lomwe tingasale kudya tsiku la Aashurah. ubwino ndi kuchuluka kwa madalitso atsiku limeneri tingakunvetse bwino kudzera mu khumbo limene Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankakhala nalo lofuna kukumana nawo mwezi umenewu.
عن ابن عباس رضي الله عنهما قال ما رأيت النبي صلي الله عليه وسلم يتحري صيام يوم عاشوراء
Sayyiduna Abdullah bin Abbas (radhiyallahu anhuma) akufotokoza kuti, “sindidamuone Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) akudikilira mwachidwi kusala kudya komwe kuli ndi malipiro ochuluka kuposa tsiku la Aashurah.(Saheeh Bukhaari #2006)
عن أبي قتادة رضي الله عنه قال قال رسول الله صلي الله عليه وسلم صيام يوم عاشوراء اني أحتسب علي الله أن يكفر السنة التي قبله
Zafotokozedwa kuchokera kwa Abu Qataadah (radhiyallahu anhu) kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, Chifukwa chosala kudya pa tsiku la Aashura ndiri ndi chiyembekezo kuti Allah adzakhululuka machimo a munthu amene angasale kudya tsiku limeneri machimo omwe adachita m’chaka chimenechi .(Ibnu Maajah #1738, Saheeh Muslim #1162)
Malipiro osala kudya kwa mwezi onse
Mwezi wa Muharram umatengedwa kuti ndimwezi wa Allah, ndipo kusala kudya m’mwezi umenewu ndikopambana kwambiri pambuyo pa mwezi wa Ramadhaan, uli ndi madalitso apadera omwe amabwera m’mwezi okhawu wa Muharram, kotero kuti munthu amene angasale kudya kwa tsiku limodzi lokha amapeza sawabu zoti wasala kudya kwa mwezi onse. Sawabu zimenezi zimapezeka m’mwezi wa Muharram okha Chifukwa palibe mwezi wina omwe ulindi sawabu ngati zimenezi.
عن ابن عباس رضي الله عنهما قال قال رسول الله صلي الله عليه وسلم من صام يوم عرفة كان له كفارة سنتين ومن صام يوما من المحرم فله بكل يوم ثلاثون يوما
Zafotokozedwa kuchokera kwa Abdullah bin Abbas (radhiyallahu anhuma) kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, munthu amene angasale kudya tsiku la Arafah (pa 9 Zul Hijjah) adzakhululukidwa machimo amene adachita kwazaka ziwiri ndipo amene angasale kudya tsiku lililonse m’mwezi wa Muharram tsiku lina lililonse lomwe angasale kudya adzalandira sawabu zoti wasala kudya kwa mwezi onse watunthu.(At-Targheeb wat-Tarheeb #1529)
عن أبي هريرة رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم أفضل الصيام بعد رمضان شهر الله المحرم وأفضل الصلاة بعد الفريضة صلاة الليل
Zafotokozedwa kuchokera kwa Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, Saum imene ili ndi madalitso ambiri pambuyo pa mwezi wa Ramadhaan ndi saum ya mwezi wa Muharram ndipo salah imene ili yopambana kwambiri pambuyo pa swalah za fardh ndi swalah yomwe imapheredwa usiku ya Tahajjud.(Saheeh Muslim #1163)