عن عبد الله بن مسعود قال إذا أراد أحدكم أن يسأل فليبدأ بالمدحة والثناء على الله بما هو أهله ثم ليصل على النبي صلى الله عليه وسلم ثم ليسأل بعد فإنه أجدر أن ينجح (المعجم الكبير للطبراني، الرقم: ٨٧٨٠، ورجاله رجال الصحيح إلا أن أبا عبيدة لم يسمع من أبيه كما في مجمع الزوائد، الرقم: ١٧٢٥٥)
Sayyiduna Abdullah bin Mas’ood (radhiyallahu anhu) adafotokoza kuti, “pamene m’modzi mwa inu akufuna kupanga Duwa kumupempha Allah yambani ndi kumutamanda pogwiritsa ntchito maina ake omwe akusonyeza kumutamanda ndi kumuyamikira komanso kukweza ulemelero wake ndipo kenako Werengani Durood ndipo Pamapeto pake Pangani duwa chifukwa choti (kutsatira ndondomeko imeneyi popanga duwa) pali kuthekera koti munthuyo adzapambana (duwa yake idzalandiridwa).
Moyo Ndi Chuma Cha Sayyiduna Abu Bakr (Radhiyallahu Anhu) ziperekedwa Nsembe Chifukwa Cha Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasallam)
Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti tsiku lina lake Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “palibe chuma cha munthu chomwe chidandithandiza kwambiri kuposera chuma cha Abu Bakr Siddeeq (radhiyallahu anhu).” Pakunva zimenezi Sayyiduna Abu Bakr (radhiyallahu anhu) adayamba kulira kwambiri ndipo adati, “oh Mtumiki wa Allah (sallallahu alaih wasallam), chuma changa ndi moyo wanga zonse ndi zanu.” (Sunan Ibnu Majah, #94)