6. Kuchuluka kwa aneneri onse akudziwa ndi Allah yekha, timakhulupilira mwa atumiki onse angakhale ochuluka bwanji.
7. Monga ziliri kuti ndi chizindikiro cha utumiki, Allah amamulora mtumiki kuchita zodabwitsa zomwe zimatchedwa kuti Mu’ujizaat. Komano Tikuyenera kuzindikira kuti mtumiki ndi munthuso ndipo sangapange zodabwitsa mwa iye yekha, zimangochitika kudzera muchifuniro cha Allah komanso mothandizidwa ndi iye.
8. Mtumiki oyambilira ndi Adam (alaihi salaam) ndipo omaliza ndi mtumiki Muhammad (sallallahu alaih wasallam), aneneri ena onse anabwera pakati pa aneneri awiriwa.
9. Ena mwa maina aneneri omwe adatchuridwa mu Quran komanso m’mahadeeth olemekezeka ndi monga; Nabi Nuuh (alaihi salaam), Nabi Ibrahim (alaihi salaam), Nabi Ishaaq (alaihi salaam), Nabi Ismail (alaihi salaam), Nabi Ya’aqub (alaihi salaam), Nabi Yusuf (alaihi salaam), Nabi Dawud (alaihi salaam), Nabi Sulaimaan (alaihi salaam), Nabi Ayyub (alaihi salaam), Nabi Musah (alaihi salaam), Nabi Haarun (alaihi salaam), Nabi Zakariyyah (alaihi salaam), Nabi Yahya (alaihi salaam), Nabi Isah (alaihi salaam), Nabi Ilyaas (alaihi salaam), Nabi Al-Yasa’ (alaihi salaam), Nabi Yunus (alaihi salaam), Nabi Luut (alaihi salaam), Nabi Idriis (alaihi salaam), Nabi Zul Kifl (alaihi salaam), Nabi Swaalaih (alaihi salaam) ndi Nabi Shu’aib (alaihi salaam).
10. Qiyaamah isadafike Isah alaihi salaam adzatumizidwa kuti adzaphe Dajjaal. utumiki wa Nabi Isah (alaihi salaam) siudzathetsedwa. adzatumizidwa kuti adzathandizire ummah wa Mtumiki Muhammad (sallallahu alaih wasallam) ndiponso adzatsatira sharia cha Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) nthawi imeneyo pamene adzakhalebe ali padziko lino lapansi adzalandira wahi (chibvumbulutso) kudzera m’nchibvumbulutsochi iye adzauthandiza ummah kulimbana ndi bodza.