Sunnah yosala kudya tsiku la Ashurah

Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) mwini wake adasala kudya tsiku la Ashurah ndikulambikitsanso maswahabah kuti asale kudya patsiku limeneli, khumbo lofuna kukwaniritsa sunnah imeneyi tingainvetse bwino kudzera mu Hadith iyi:

عن الربيع بنت معوذ بن عفراء رضي الله عنها قالت فكنا بعد ذلك نصومه ونصوم صبياننا الصغار منهم ان شاء ألله ونذهب الى المسجد فجعل لهم اللعبة من العهن فإذا بكى أدهم على الطعام أعطيناهم إياه عند الإفطار

Sayyidatuna Ruhayy (Radhiyallahu anha) akufotokoza kuti tinkasala kudya tsiku la Ashura komanso tinkawapalimbiktsa ana athu kusalanso, tinkakonza matoyi opangidwa kuchokera ku thonje kuti adzisoweretsa akalira ndi njala pamene akusala kudya kufuna chakudya tinkawapatsa matoyiwa kuti akopeke nawo kufikira nthawi yofutulu itakwana. (Saheeh Muslim #1136)

Mbiri ya Ashura

Pambuyo pa nsamuko (hirah) Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankasala kudya pa tsiku la Ashura mu nzinda olemekezeka wa Makkah Mukarramah,atasamukira ku Madina Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adapeza ayuda akusala kudyanso pa tsiku limeneli la Ashurah, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) atawafunsa kuti ndichifukwa chiyani akusala kudya pa tsiku limeneli iwo adayankha kunena kuti ili ndi tsiku limene Allah adamupulumutsa Nabi Musah (alaih wasallam) komanso bani Israail kwa Farao ndi anthu ake komanso Allah adamuononga Farao ndi anthu ake pa tsiku lomweli.

عن ابن عباس رضي الله عنهما قال قدم النبي صلى الله عليه وسلم المددينة فرأى اليهود تصوم يوم عاشوراء فقال ما هذا قالوا هذا يوم صالح هذا يوم نجى الله بني إسرائيل من عدوهم فصامه موسى قال فأنا أحق بموسى منكم فصامه وأمر بصيامه

Sayyiduna Ibnu Abbaas (radhiyallahu anhuma) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) atasamukira ku Madinah adawapeza Ayuda akusala kudya tsiku la Ashura, atawafunsa kuti ndichifukwa chiyani akusala kudya tsiku limeneli iwo adayankha kuti ili nditsiku lopambana kwambiri, nditsiku lomwe Allah adawapulumutsa Bani Israil kwa Farao ndi anthu ake kumazunzo omwe ankakumana nawo oponderezedwa, komanso kuthokoza kumuyamika Allah, Nabi Musah (alaihi salaam) ankasala kudya tsiku limeneri Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha nati “ife ndi amene tikuyenera kumutsatira Musah alaih salaam kusiyana ndi inuyo” kenaka Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankasala kudya tsikuli likafika ndipo adawalimbikitsa ophunzira ake kuti adzisalanso. (Saheeh Bukhaari #2004)

Poyamba kusala kudya m’mwezi wa Ramadhaan kusadakhale lamulo, kusala kudya tsiku la Ashura kudali kokakamizidwa. kenaka ndipamene lamulo losala kudya m’mwezi wa Ramadhan lidaperekedwa ndipo kusala kudya tsiku la Ashura kudakhala sunnah.

عن عائشة زوج النبي صلى الله عليه وسلم أنها قالت :كان يوم عاشوراء يوما تصومه قريش في الجاهلية وكان رسول الله صلى الله عليه و سلم يصومه في الجاهلية فلما قدم رسول الله صلى الله عليه وسلم المدينة صامه وأمر بصيامه فلما فرض رمضان كان هو الفريضة وترك يوم عاشوراء فمن شاء صامه ومن شاء تركه

Sayyidatuna Aisha (radhiyallahu anha) akufotokoza kuti , chisilamu chisadafike ma Quraish ankasala kudya patsiku la Ashura ,Nabi (sallallahu alaih wasallam) nayenso ankasala , atasamukira ku Madina Munawwarah Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adapitilizabe kusala kudya, ndipo adawauzanso ophunzira ake kuti adzisala kudya nawonso popeza lidali lamulo, komano pambuyo poti kudalamuridwa kusala m’mwezi wa Ramadhan kusala tsiku limeneli la Ashura kudasanduka kukhala sunnah. (Muatta Imaam Maalik #842)

Kusala kudya tsiku la Ashura kudakhalabe chizolowezi cha Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuphatikizanso ma Swahabah (radhiyallahu anhum) mpaka pomwe Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adasiyana nalo dziko lino. Komano Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) asadamwalire Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adawalamura ophunzira ake kuti atsutsane ndi Ayuda poonjezera tsiku limodzi patsiku limeneli la Ashura.

عن ابن عباس رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم صوموا يوم عاشوراء وخالفوا فيه اليهود صوموا قبله يوما أو بعده يوما

Abdullah bin Abbaas (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, salani kudya patsiku la Ashura ndikutsutsana ndi Ayuda pomanga tsiku limodzi lapambuyo pake kapena lamawa lake lomwe ndi pa 9 ndi 10 kapena 10 ndi 11 Muharram. (As-Sunanul Kubra lil Baihaqi #8406, At-Talkheesul Habeer #931)

Check Also

Chikondi Cha Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) Kumukonda Nabi (sallallahu alaih wasallam)

Nabi (sallallahu alaih wasallam) adawuyamba nsamuko pamodzi ndi Abu Bakr (radhwiyallahu) anhu chakumadzulo, nkatikati mwa …