Olemekezeka Abdullah Al-Hawzani (rahimahullah) akufotokoza kuti nthawi ina adakumana ndi Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) ku Halab (mzinda wa Shaam). Atakumana ndi Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adamufunsa kuti: “E, Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu)! Ndiuze momwe Nabiy (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ankagwiritsira ntchito chuma chake (pa ntchito ya dini). Bilaal (Radhwiya Allaahu …
Read More »Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) Aitana Azaan pa Ka’bah
Nthawi ya Fath-e-Makkah (Kugonjetsa kwa Makka), Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adalowa mu Ka’bah Shariif pamodzi ndi Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) komanso Usaamah (radhwiyallahu ‘anhu). Pa nthawiyo, Mzikiti udali odzadza ndi ma Quraishi omwe adali mmizeremizere, akumuyang’ana Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) kuti aone zimene achite ndi momwe awachite …
Read More »Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) Amva kuyenda kwa Mapazi a Olemekezeka Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) ku Jannah.
Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiya Allaahu ‘anhu) akusimba kuti nthawi ina, nthawi ya Swalah ya Fajr, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati kwa Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu): “E, Bilaal! Pa ntchito zabwino zomwe umachita mchisilamu, ndi ntchito iti yomwe imakulimbikitsa kuti udzapindula nayo pa tsiku lachiweruzo,chifukwa usiku wapitawu ndamva kuyenda …
Read More »Olemekezeka Bilal Radhwiyallahu anhu asankhidwa kukhala Muazin wa Rasulullah swallallahu alaihi wasallam
“Mtumiki (sallallahua alaih wasallam) atapanga Hijrah (atasamukira) kupita ku Madina Munawwarah adamanga nzikiti. Atamanga nzikiti adakambirana ndi ophunzira ake nkhani yopezera njira imene angamawaitanire anthu kuti adzaswali. Lidali Khumbo la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti anthu adzisonkhana ndikuswalira pamodzi munzikiti. Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sankasangalatsidwa kuti masahabah adzaswali aliyense payekha …
Read More »Kukhanzikika kwa Hazrat Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu) pa Chisilamu
Hazrat Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu) ndi Sahaabi otchuka pakati pa ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum), ndipo anali muazzin wa mzikiti wa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam). Poyamba, iye anali kapolo wa ku Abyssinia wa osakhulupirira ku Makkah Mukarramah. Kutembenuka kwake kukhala Msilamu sikunali kokondedwa ndi bwana wake, kotero adazunzidwa mopanda …
Read More »Olemekezeka Sa’d bin Abi Waqqaas (Radhiyallahu ‘anhu) atenga nawo gawo kusambitsa thupi la Hazrat Saiid bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu)
Olemekezeka Saiid bun Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) atamwalira, Hazrat Sa’d bun Abi Waqqaas (Radhiyallahu ‘anhu) ndi Hazrat Abdullah bun Umar (Radhwiyallahu ‘anhuma) adali m’gulu la anthu omwe adasambitsa thupi lake. Mwambo osambitsa utatha Jenezah idanyamuridwa ndi anthu ochokera ku Aqeeq kupita nayo ku Madina Munawwarah kuti akaikidwe ku manda otchedwa Baqi’ …
Read More »Kukhudzika kwa olemekezeka Sa’iid bin Zaid (radhwiyallahu ‘anhu) pa kusankhidwa kwa Khalifah.
Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) adakhala pansi ndi mwana wake Abdullah bun Umar, msuweni wake, Said bun Zaid, ndi Abbaas (radhwiyallahu ‘anhum). Umar (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adawauza kuti: “Ndaganiza kuti sindidzaika munthu wina aliyense kukhala Khalifah pambuyo panga.” Olemekezeka Sa’iid bin Zaid (Radhwiya Allaahu ‘anhu) pokhudzika za ubwino wa Asilamu ndi …
Read More »Kulemekezeka kwa Sa’iid bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) pamaso pa Abdullah bin Umar (radhwiyallahu ‘anhuma)
Tsiku lina Abdullah bin Umar (Radhwiyallahu ‘anhuma) akukonzekera kupita ku Swalaah, adamva kuti amalume ake, Sa’iid bin Zaid (radhiyallahu ‘anhu) akudwala kwambiri ndipo atha kumwalira. Nkhaniyi idamufika pa nthawi yomwe adali atadzola kale (mafuta onunkhiritsa) thupi lake ndipo ali pafupi kuchoka kwawo kupita ku Swalaah ya Jumuah. Koma atamva nkhani …
Read More »Kulemekeza kwa Saiid bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) kumulemekeza Uthmaan (Radhwiyallahu ‘anhu)
Zanenedwa kuti nthawi ina munthu wina adadza kwa olemekezeka Saiid bin Zaid (Radhwiya-Allahu anhu) nati: “Ndili ndi chikondi chachikulu pa Ali (Radhwiya-Allahu ‘anhu) mu mtima mwanga moti sindikonda china chilichonse monga momwe ndimamukondera.” Saiid bin Zaid (Radhwiya-Allahu ‘anhu) adamuyamikira iye chifukwa cha chikondi ndi ulemu wake kwa Ali (Radhwiyallahu ‘anhu) …
Read More »Udindo Wapamwamba wa Olemekezeka Said bin Zaid (Radhwiya Allaahu ‘anhu) Pakati pa anthu a ku Madinah Munawwarah
M’nthawi ya khilaafah ya Olemekezeka Mu’aawiyah (Radhwiya Allahu ‘anhu) adalembera kalata Marwaan bin Hakam bwanamkubwa wake yemwe adasankhidwa ku Madinah Munawwarah pomwe adamulangiza kutenga bay’at (chikole cha chikhulupiriro) kwa anthu a ku Madinah Munawwarah m’malo mwa mwana wake, Yaziid bin Mu’aawiyah, yemwe adzakhale Khalifah m’malo mwake mwake. Mu’aawiyah (Radhwiyallahu ‘anhu) …
Read More »
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu