
́Allaamah Zurqaani (Rahimahullah) wapereka nkhani iyi kuchokera kwa Haafiz ibn ‘Asaakir (rahimahullah) ndi mndandanda wamphamvu wa osimba nkhani:
Atamwalira Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam), zinali zovuta kwa olemekezeka Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) kupitiriza kukhala ku Madinah Munawwarah cha okondeka wake kwambiri Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ndi kukumbukira zosaiŵalika za Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) mu mzinda odalitsika.
Choncho Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu) adachoka ku Madinah Munawwarah nakakhanzikika ku Daariyyaa (malo omwe ali ku Syria). Patapita nthawi, akukhala ku Syria, Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) usiku wina anamulota Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam). Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) adamuuza kuti, “Iwe Bilaal! N’chifukwa chiyani wadzipatula kwa ine? Kodi si nthawi yoti ubwere kudzandiona?”
Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) atadzuka, adadzadzidwa ndi chisoni chachikulu komanso nkhawa, kotero kuti nthawi yomweyo adakwera pa chokwera chake ndikupita ku Madinah Munawwarah.
Atafika pafupi ndi manda odalitsika a Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam), adagwidwa ndi chikondi chachikulu kwa Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) komanso chisoni chachikulu chifukwa cha kusiyana kwake kotero kuti nthawi yomweyo anayamba kulira kwambiri.
Hasan ndi Husain (radhwiyallahu ‘anhuma) pambuyo pake anabwera kudzakumana naye. Atawaona, Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) adawakumbatira ndi kuwapsompsona chifukwa cha chikondi chomwe anali nacho pa banja la Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam). Pambuyo pake adauza Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu), “Tikufuna kukumvani mukuosnga azaan monga momwe munkachitira nthawi ya Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam).”
Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) adakwera pamalo okwera kuti akachite azaan. Atayamba kupanga azaan ndi mau onena kuti “Allahu Akbar Allahu Akbar!” misewu ya Madinah Munawwarah idayamba kumveka ndi mawu ake odalitsika.
Pamene ankapitiriza ndi kutchula mawu otsatira a azaan, mawu a ku Madinah Munawwarah anawonjezeka, kufika kwa anthu, mpaka akazi ndi ana anatuluka m’nyumba zawo. Onse ankaoneka akulira chifukwa chokumbukira kwambiri nthawi ya Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam). Chikondi chosayerekezeka chomwe anali nacho pa Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) chinali chotere, moti sichinakhalepo tsiku limodzi pambuyo pa imfa ya Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) momwe anthu a ku Madinah Munawwarah analilira kwambiri kuposa tsiku limenelo. (Zurqaani 5/71)
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu