Kulowa Chisilamu kwa Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu)

Khalidwe lake Asanalowe Chisilamu: Asanalowe Chisilamu, Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) anali chigawenga. Anali olimba mtima kwambiri kotero kuti popanda kuthandizidwa ndi anzake ena, ankakwanitsa yekha kubera anthu ndikuwachita uchifwamba. Nthawi zina, ankaukira anthu apaulendo atakwera pahatchi, ndipo nthawi zina, ankaukira akuyenda pansi. (Siyar A’laam min Nubalaa 3/373)

Pambuyo pake, anasiya makhalidwe ake oipa obera anthu mmisewu ndipo anayamba kupembedza Allah Ta’ala yekha, kukhulupirira Tauhiid (Umodzi wa Allah Ta’ala).

Zanenedwa kuti zaka zitatu asanalowe Chisilamu, ankalambira Allah Ta’ala yekha ndipo ankakhulupirira Tauheed (Umodzi wa Allah Ta’ala). (Usdul Ghaabah 1/343)

Kulowa Chisilamu kwa Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu)

Abu Zar Ghifaari (radhwiyallahu ‘anhu) ndi otchuka kwambiri pakati pa ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) chifukwa cha kudzipereka kwake komanso uzindikiri wake.

Ali (radhwiyallahu ‘anhu) ankakonda kunena kuti, “Abu Zar ndiye nkhokwe ya uzindikiri omwe anthu ena sangathe kuupeza.”

Atangomva koyamba za utumiki wa Mneneri (swallallahu ‘alaihi wasallam), adatuma mchimwene wake kuti apite ku Makkah Mukarramah kukafufuza za ‘munthu’ amene ankanena kuti ndiye walandira utumiki. Anamulangiza mchimwene wake kuti akafunse za momwe munthuyo alili, ndikumvetsera uthenga wake mwachidwi.

Mchimwene wake anapita ku Makkah Mukarramah ndipo anabwerera atafufuza mozama, ndipo anamuuza kuti anapeza Muhammad (swallallahu ‘alaihi wasallam) kukhala munthu amene amalamula anthu kuti azitsatira makhalidwe abwino ndi machitidwe abwino, ndipo ananenanso kuti chivumbulutso chake ndi chodabwitsa ndipo sindakatulo kapena.

Lipotili silinafotokozedwe mokwanira ndipo sanakhutire nalo, motero anaganiza zopita ku Makkah Mukarramah kuti akapeze yekha zoona zake. Atafika ku Makkah Mukarramah, anapita molunjika ku Haram. Sanamudziwe Mneneri (swallallahu ‘alaihi wasallam), ndipo sanaone kuti ndi bwino (malingana ndi zichitochito zomwe zinalipo panthawiyo) kufunsa za iye kwa aliyense.

Anakhalabe mu Haram mpaka madzulo. Pamene kunada, Hazrat Ali (radhiyallahu ‘anhu) anamuzindikira, ndipo poona kuti anali mlendo, sakanatha kumunyalanyaza, chifukwa kumusamalira mlendo ndi kusamalira, osauka ndi akunjira, zinali khalidwe lachiwiri la Masahaabah. Choncho, adamutengera kunyumba kwake ngati mlendo. Sanamufunse za cholinga cha ulendo wake ku Makkah Mukarramah, komanso Hazrat Abu Zar (radhiyallahu ‘anhu) mwiniwake sanamuuze.

Ali (radhiyallahu ‘anhu) adamutengeranso kunyumba usiku, adamupatsa chakudya ndi malo ogona, koma sanakambirane nayenso cholinga chomwe wabwelera mumzindawo. Komabe, usiku wachitatu, Ali (radhiyallahu ‘anhu) atamulandira, monga momwe zinalili usiku wapitawo, adamuwuza kuti, “M’bale, cholinga cha ulendo wako obwera kuno ndi chiyani?”

Asanafotokoze cholinga chake, Hazrat Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) adamupempha Ali (radhwiyallahu ‘anhu) kuti alonjeze kuti adzanena zoona pa zomwe akufuna kumufunsa. Pambuyo pake, adamufunsa za Muhammad (swallallahu ‘alayhi wasallam).

Ali (radhwiyallahu ‘anhu) anayankha kuti, “Ndithudi iye ndi Mneneri wa Allah. Ubwere nane mawa m’mawa ndipo ndidzakutengera kwa iye. Pali kutsutsana kwakukulu (kotsutsana ndi Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) ndi Asilamu, kotero ndikuopa kuti ngati angakuoneni muli ndi ine, mungakumane ndi mavuto). Ngati ndiona vuto panjira, ndiye kuti ndipita m’mbali mwa msewu, ndikunamizira ngati ndikufunika kudzithandiza kapena ndikukonza nsapato zanga, ndipo uyenera kupita patsogolo osaima kuti anthu asaganize kuti tili limodzi.”

M’mawa otsatira, adatsata Hazrat Ali (radhiyallahu ‘anhu) yemwe adamutengera kwa Mneneri (swallallahu ‘alaihi wasallam). Pankumano oyamba, adalowa Chisilamu.

Poopa kuti ma quraish angamuvulaze, Mneneri (sallallahu ‘alaihi wasallam) adamupempha kuti asunge chinsinsi chake cha Chisilamu. Anamupemphanso kuti abwerere kwawo kubanja lake ndi kubwerera pamene Asilamu akadzachuluka kwambiri ndipo chisilamu chili ndi mphamvu kwambiri.

Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) anayankha kuti, “Iwe Mneneri wa Allah! Ndikukhulupirira Iye amene ali bwana wa moyo wanga, ndiyenera kupita kukawerenga kalimah pamaso pa osakhulupirira awa!”

Mogwirizana ndi mawu ake, anapita molunjika ku Haram, ndipo pakati pa khamu la anthu, ndiposo mokweza mawu, anawerenga shahaadah:

اشهد أن لا إله إلا اللهُ وأَشْهَدُ أَنَّ مُحَمَّدًا رَسُولُ الله

Ndikuchitira umboni kuti palibe Mulungu wina kupatula Allah, ndipo ndikuchitira umboni kuti Muhammad (sallallahu ‘alaihi) ndi Mtumiki wake

Anthu anamuukira kuchokera mbali zonse, ndipo akanamumenya mpaka kufa pakapanda Abbaas, amalume ake a Mtumiki (Sallallahu ‘alaihi wasallam) omwe anali asanalowe Chisilamu mpaka nthawi imeneyo, sanamuteteze ndikumupulumutsa ku imfa.

Abbaas adati kwa gulu la anthu, “Kodi mukudziwa kuti ndi ndani? Ndi wa fuko la Ghifaar lomwe limakhala Mnjira yathu yopita ku Syria. Ngati aphedwa, adzatipha ndipo sitidzatha kuchita malonda ndi dzikolo.”

Anthuwo adamvetsetsa kuti kuchita malonda ndi Syria ndiye njira yokwaniritsira zosowa zawo zapadziko lapansi, ndipo ngati msewuwu ungatsekedwe, zikanabweretsa mavuto ambiri kwa iwo. Kotero, adachoka ndikumusiya yekha.

Tsiku lotsatira, Hazrat Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) adabwerezanso shahaadah pamaso pa anthu, ndipo mosakayikira akanamenyedwa mpaka kufa ndi khamulo pakapanda Abbaas kulowereraponso ndikumupulumutsa kachiwiri.

Zimene Hazrat Abu Zar (radhiyallahu ‘anhu) anachita zinali chifukwa cha chikondi chake chachikulu chofuna kufuula Kalimah pakati pa ma Kuffaar. Malangizo a Mneneri (sallallahu ‘alaihi wasallam) omuletsa anali chifukwa cha chikondi chomwe chinali mumtima mwake kwa Abu Zar (radhiyallahu ‘anhu). Mneneri (sallallahu ‘alaihi wasallam) sanafune kuti ma Kuffaar amuvutitse zomwe zingakhale zovuta kwambiri kuti apirire.

Mu nkhaniyi, palibe kusamvera komwe kunapezeka kuchokera kwa Hazrat Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) pankhani ya uphungu omwe Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) adamupatsa, popeza Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam) mwiniwake ankakumana ndi mavuto osiyanasiyana chifukwa cha Allah Ta’ala pofalitsa uthenga wa Chisilamu. Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) nayenso ankaganiza kuti ndi bwino kutsatira chitsanzo chake m’malo mogwiritsa ntchito chilorezo chake kuti apewe ngozi.

Uzimu wa ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) ndi umene unawafikitsa pamwamba pa kupita patsogolo kwa zinthu zakuthupi ndi zauzimu m’magawo onse a moyo. Ma Sahaabah (radhiyallahu ‘anhum) anali oti akangowerenga kalimah ndikulowa Chisilamu, panalibe mphamvu padziko lapansi yomwe ikanawabweza m’mbuyo ndipo palibe kupondereza kapena nkhanza zomwe zikanawaletsa kufalitsa mawu a Allah Ta’ala. (Fazaa’il-e-A’maal (Chingerezi) tsamba 23-25, (Chiurdu) tsamba 14-16)

Check Also

Olemekezeka Abu Zar (Radhwiyallahu ‘anhu) Kulemekeza Alendo

‘Isa bin ‘Umailah (Rahimahullah) akufotokoza za munthu wina amene adawona khalidwe la Abu Zar (Radhwiyallahu …