Olemekezeka Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) achita Azaan ku Shaam

‘Umar (Radhiyallahu ‘anhu) ulendo wina atapita ku Baitul Muqaddas m’nthawi ya Khilaafat yake, adayendera Jaabiyah (malo ena ake ku Shaam). Ali ku Jaabiyah anthu adadza kwa iye ndikumupempha ngati angamupemphe Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu) yemwe ankakhala ku Shaam kuti awachitire azaan chifukwa iye adali muazzin wa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ku Madina Munawwarah.

‘Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) adamupempha Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) kuti apange azaan ndipo nthawi yomweyo adavomera.

Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) atangoyamba kupanga azaan, anthu adakumbutsidwa nthawi ya Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Bilaal (radhiyallahu ‘anhu) ankapanga Azaan ku Madina Munawwarah. Izi zidawapangitsa kulira chifukwa chodandaula za kulekana kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) pa dziko lapansi.

Pofotokoza kukula kwa chisoni ndi kudandaula kwa anthu, Aslam (rahimahullah), kapolo omasulidwa wa ‘Umar (radhwiyallahu ‘anhu), adati: “Sindinaonepo anthu akulira tsiku lina lililonse kuposa momwe ndidawaonera tsiku limenelo.” (Siyar A’laamin Nubalaa 3/222, Sharhuz Zarqaani 5/71)

Check Also

Olemekezeka Abu Zar (Radhwiyallahu ‘anhu) Kulemekeza Alendo

‘Isa bin ‘Umailah (Rahimahullah) akufotokoza za munthu wina amene adawona khalidwe la Abu Zar (Radhwiyallahu …