Dua ya Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) kumupangira Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu)

Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu ‘anhu) akufotokoza kuti:

Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) atachoka kupita ulendo wa ku nkhondo ya Tabuuk, anthu ena sanapite nawo paulendowo ndipo anasankha kutsala. Ambiri mwa anthuwa anali ma munaafiqiin (achipha maso).

Maswahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) akamauza Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) za anthu omwe anatsala, Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) ankayankha kuti, “Musiyeni! Ngati pali chabwino chilichonse mwa iye, ndiye kuti Allah Ta’ala amuika mgulu lanu posachedwa, ndipo ngati palibe chabwino mwa iye, ndiye kuti Allah Ta’ala wakumasurani kwa iwo.”

Pamapeto pake, wina anauza Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) kuti Abu Zar (radhiyallahu anhu) anatsala chifukwa ngamila yake siimayenda. Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) anayankha nati, “Musiyeni! Ngati muli chabwino chilichonse mwa iye, Allah Ta’ala akulum8kizanitsani naye posachedwa, ndipo ngati mulibe chabwino mwa iye, Allah Ta’ala akhala kuti wakupulumutsani ku kupezeka kwake.”

Olemekezeka Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) ataona kuti sangathe kupitiriza kuyenda pa ngamila yake, anaika katundu wake kumbuyo kwake nayamba kuyenda pansi kuti akakumane ndi Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam).

Atayenda kwa kanthawi, Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) ndi ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) anaima pamalo ena kuti apumule. Ali pamalopo, m’modzi mwa ma Swahaabah atayang’ana mmbuyo anaona munthu wina ali patali akuyandikira akuyenda pansi. Analankhula ndi Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) nati, “E, Rasulullah wa Allah, ndikuona munthu akuyenda pansi (akutiyandikira kuchokera patali)!”

Atamva izi, Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) anafuula mokondwera, “Akhale Abu Zarl.” Ma Swahaabah (Radhiwyallahu ‘anhum) atayang’ana kwambiri munthu amene akubwera wapansi ndipo anazindikira kuti ndi iyeyo, anafuula mosangalala ndi chimwemwe, “Ndikulumbira mwa Allah, ndi Abu Zar!”

Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam) adamupangira dua Abu Zar (Radhwiyallahu ‘anhu) kuti, “Allah atsitse chifundo Chake chapadera pa Abu Zar Akubwera (kwa ife) akuyenda yekha, adzafa yekha ndipo adzaukitsidwa yekha.” (Siyar Alaam min Nubalaa 3/384)

Check Also

Kulowa Chisilamu kwa Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu)

Khalidwe lake Asanalowe Chisilamu: Asanalowe Chisilamu, Abu Zar (radhwiyallahu ‘anhu) anali chigawenga. Anali olimba mtima …