Olemekezeka Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) Msungichuma wa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam)

Olemekezeka Abdullah Al-Hawzani (rahimahullah) akufotokoza kuti nthawi ina adakumana ndi Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) ku Halab (mzinda wa Shaam). Atakumana ndi Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adamufunsa kuti: “E, Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu)! Ndiuze momwe Nabiy (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ankagwiritsira ntchito chuma chake (pa ntchito ya dini).

Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) anayankha kuti:

“Kuyambira pamene Allah Ta’ala anamuika Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) kukhala Nabi mpaka pamene adachokera pa dziko lapansi, khalidwe la Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) lidali loti (kuyambira nthawi imene ndidali naye), akalandira chuma chilichonse, amandisungitsa.

“Nthawi zonse Msilamu akabwera kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ndipo Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) akaona kuti munthuyo alibe chobvala chokwanira (kapena chakudya), amandilangiza kuti ndimupatse zovala (ndi chakudya). Ngati Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) alibe chuma chilichonse, ndikatenga ngongole iliyonse yomwe ndinkagulira chobvala ndi china chilichonse chomwe chafunikira zomwe pambuyo pake ndinkamupatsa munthuyo kuti avale ndi kumupatsa chakudya. Izi zidapitilira chomwechi mpaka tsiku lina munthu wina wachikunja adandiyandikira nati: “E, iwe Bilaal! Ndili ndi chuma chambiri, choncho usatenge ngongole kwa wina aliyense kupatula ine.” Choncho, ndinayamba kupita kwa iye kukatenga ngongole ndipo ndinasiya kutenga ngongole kwa anthu ena.

Tsiku lina nditamaliza kupanga wudhu wanga ndipo ndidatsala pang’ono kuyitana azaan kuti ndiswali. Pamene Ndidamuona wachikunja yemwe uja ali pakati pa gulu la amalonda pafupi. Atandiona, nthawi yomweyo anandiitana kuti, “O Abyssinian” Kenako anayamba kundilankhula mwamwano komanso monyoza. Anandifunsa kuti, “Kodi ukudziwa kuti watsala ndi nthawi yochuluka bwanji kuti mwezi uthe?” Ndinayankha, “mwezi watsala pang’ono kutha.” Adati: “Kwatsala masiku anayi okha. Mwezi ukatha, ngati sundibwezera ngongole yanga, ine ndikutenga kukhala kapolo wanga posinthana ndi ndalama yomwe unandikongola. Sindinakukongoze chuma chifukwa cha ulemu wanga pa iwe kapena mnzako (Rasulullah sallallahu alaihi wasallam). Ndinakubwereka ndi cholinga choti udzakhale kapolo ndikumadyetsera ziweto zanga monga unkachitira kale (pamene udali kapolo). Nditamva mawu amenewa, ndinadabwa kwambiri. Komabe, ndidaitana azaan kuti tiswali ndipo tidaswali Swalaah ya Esha.

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atabwerera kunyumba Swalah ya Esha itatha, ndinapita kwa iye ndikupempha chilolezo cholowa m’nyumba mwake kuti ndilankhule naye. Atandilola, ndidalowa ndikumuuza kuti: “E, Mtumiki wa Allah(Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam)! Abambo ndi amayi anga aperekedwe nsembe chifukwa cha inu! Kafiri yemwe ndidakuuzani kuti ndikumwe ndikukongola ndalama uja, wandiopseza kuti anditenga kukhala kapolo wake ngati sindimulipira pakutha kwa mwezi. Iwe ndi ine tilibe njira yomulipira ndipo akufuna kundiyalutsa (pakati pa anthu). Ndiloreni ndithawire dela lina kumene anthu ake ndi asilamu kuti ndikakhale pakati pawo kufikira Allah Ta’ala atakupatsani ndalama zoti tidzabweze zimene ndinakongola kwa anthu osakhulupirira.’

“Nditamuuza Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam), ndinachoka kunyumba kwake ndikupita kunyumba kwanga. Nditafika kunyumba kwanga, ndinatenga lupanga langa, thumba langa, mkondo wanga ndi nsapato zanga ndikuzisiya kumutu kwanga kenako ndinagona pansi moyang’anizana nazo. Umo ndi momwe nkhawa yanga idalili ndipo ndimalephera kugona. Tjlo likabwera ndinkadzidzimuka ndiri okhumudwa mpaka mwamwayi ndidakwanitsa kugona ndikudzuka patatsala pang’ono kukwana subh saadiq.

M’bandakucha, ndinali nditatsala pang’ono kuchoka kunyumba kwanga, ndipo munthu wina anabwera akuthamanga uiu akufuula kuti, “E iwe Bilaal! Bwera! Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) akukuitana!” Nthawi yomweyo ndinathamangira kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ndipo nditafika kwa iye, ndinapeza kuti pafupi ndi nyumba ya Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) padali nyama zokwana zinayi zitanyamuka katundu.

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Adandiuza: “Uthenga wabwino (E iwe Bilaal)! Allah Ta’la wakupangira njira yoti ulipilire ngongole yako. Nditamva nkhani yabwinoyi, nthawi yomweyo ndinamutamanda Allah Taala.

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adandifunsa kuti, ‘Kodi sunadutse nyama zinayi zitagwada (pafupi)?’ Ndinayankha, “Inde, ndaziona.” Kenako Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati: “Ndithu, ngamira pamodzi ndi katundu wake ndi zako.” Nditayang’ana, ndidaona kuti zasenza zovala ndi chakudya chimene Mtsogoleri waku wa Fadak (malo apafupi ndi Madinah Munawwarah) adapereka kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam). Mtumiki swallallahu alaiklhi wasallam adati: tenga ngamira zimenezo ndi katundu wakeyo ndi kubweza ngongole zonse zomwe ulinazo. Ndidamvera Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam), ndidatenga ngamira ndikuyamba kutsitsa katundu. Kenako ndidamanga ngamira ndikupita kukayitana Azaan kuti tiswali Fajr.

Titamaliza Swalah ya Fajr, ndidapita ku Baqee’ ndipo ndidalowetsa zala zanga m’makutu mwanga (kuti zindithandize kukweza mawu) ndipo ndinaitana ndi liwu langa, ‘Amene akufuna kutenga ngongole yake yomwe Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) anatenga kwa iye adzionetsere yekha!’ Ndinapitirizabe kugulitsa katunduyo ndi kulipira ngongole eni ake akangobwera, kusinthanitsa ndalama zomwe anali nazo, mpaka ngongole iliyonse inatha (kuphatikiza ngongole ya munthu osakhulupirira yemwe adandiopseza kuti anditenga kukhala kapolo uja). Nditalipira ngongole zonse, ndinatsala ndi uuqiyah imodzi ndi theka kapena ziwiri.

Panthawiyi, gawo lalikuku la tsiku linali litadutsa kale. Ndidapita ku musjid komwe ndidapeza Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atangokhala yekha. Nditamupatsa salaamu, adandifunsa zomwe ndachita ndi ngamila ndi katundu ochuluka zija. Ndidayankha kuti, ‘Allah Ta’ala walipira ngongole iliyonse ya Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) mpaka simadatsalekonso ngongole iliyomse.

Kenako anandifunsa kuti, ‘Kodi pali chuma chomwe chatsalako? Ndidati, “Inde, ndalama ziwiri zagolide.” Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Adandiuza: “(Pereka sadaka ndi kundichotsera mtolo wanga! Sindipita kunyumba kwa mkazi wanga aliyense mpaka utandichotsera ndalama ziwiri zagolide (popereka sadaka kwa osauka). Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) Sadapite kunyumba kwa akazi ake olemekezeka, ndipo adakhala usiku onse m’Musjid.

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adakhalabe munzikiti mpaka tsiku lachiwiri lidatha. Apa m’pamene panafika alendo awiri amene ndinapita nawo kukawapatsa chakudya ndi zovala. Titamaliza Swalah ya Esha, Rasullullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) anandiitana ndikundifunsa kuti ndatani ndi ndalama zotsalazo? Ndidati kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam), Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam), ‘Allah Taala wakuchotserani chumacho.

Mwachimwemwe, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati ‘Allahu Akbar!’ ndipo adamutamanda Allah Taala kuthokoza popeza ankaopa kuchoka dziko lapansi ali ndi chuma. Kenako ndinamutsatira pamene ankapita kunyumba za akazi ake onse olemekezeka kuwalonjera wina pambuyo pa wina kufikira mpakana adafika kwa mkazi yemwe adali masiku ake oti usiku umenewo agone kumeneko.
Olemekezeka Bilal Radhwiyallahu anhu kenako adati kwa Abdullah Al-Awzani rahimahullah “ili ndiye yankho la funso lako, umu ndimomwe Rasulullah swallallahu alaihi wasallam ankagwiritsira ntchito chuma chomwe ankalandira mu njira ya Allah Ta’ala” (Dalaailun Nubuwwah lil Baihaqi 1/348)

Check Also

Olemekezeka Abu Zar (Radhwiyallahu ‘anhu) Kulemekeza Alendo

‘Isa bin ‘Umailah (Rahimahullah) akufotokoza za munthu wina amene adawona khalidwe la Abu Zar (Radhwiyallahu …