Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) Aitana Azaan pa Ka’bah

Nthawi ya Fath-e-Makkah (Kugonjetsa kwa Makka), Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adalowa mu Ka’bah Shariif pamodzi ndi Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) komanso Usaamah (radhwiyallahu ‘anhu). Pa nthawiyo, Mzikiti udali odzadza ndi ma Quraishi omwe adali mmizeremizere, akumuyang’ana Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) kuti aone zimene achite ndi momwe awachite ma Quraishi omwe adamutulutsa mu Makka Mukarramah zaka zingapo zapitazo.

Ena mwa ma Quraishi ankayang’ana zomwe zinkachitika kuchokera pamwamba pa mapiri ozungulira Makka Mukarramah, pomwe ma ma Quraishi ena adathawa ndikubisala.

Inali nthawi ya mbiri imeneyi pamene Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamulangiza Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu) kuti akwere pa Ka’bah Shariif ndi kuitana azaan kuti apemphere Swala ya Zuhr.

Olemekezeka Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) atakwera pa Ka’bah kukayitana azaan, Attaab bun Asiid, Haarith bun Hishaam, Suhail bun Amr ndi Abu Sufyaan adali m’gulu la ma Quraish omwe adakhala m’dera lozungulira Ka’bah.

Atamuona Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) akuitana azaan, Attaab bun Asiid adati: “Allah adawalemekeza bambo anga Aseed powachotsa padziko lino lapansi lisanafike tsiku la lero, potero adawapulumutsa kuti asamve kuitana kwa azaan lero! Akadakhala kuti ali moyo ndikumva kuitana uku, akadakwiya kwambiri!”

Haarith bun Hishaam adalumbira nati: “Ndikadaona kuti chipembedzochi ndi choona ndi kumuona kuti akuitanira kuchoonadi, ndikadamutsatira. Koma Haarith ananenanso mawu onyoza awa kumunyoza Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu). “Muhammed (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) sanapeze wina aliyense oitana azaan kupatula khwangwala wakuda uyu?”

Suhail bun Amr adati: “Ngati Mulungu sakonda chinthu, adzachisintha.”

Abu Sufyaan adati: “Sindinganene chilichonse chifukwa ndikuopa kuti miyala iyi ingathe kumudziwitsa Nabiy (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) pazimene ndayankhula.”

Atangomaliza kuyankhula, Jibraa’iyl (‘alaihis salaam) adadza kwa Nabiy (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) ndipo adamuuza zomwe anthuwa ayankhula.

Nabiy (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adawaitana nati kwa iwo: “Ndauzidwa zomwe mwanena anthu inu.” Kenako adawauza aliyense wa iwo zomwe adanena.

Haarith ndi Attaab adadabwa ndipo nthawi yomweyo adavomereza Chisilamu uku akufuula kuti: “Ife tikuikira umboni kuti iwe ndi Mthenga wa Allah,panalibeso wina aliyense pa gulu pathu yemwe akanatha kubwera kwa iwe kudzakudziwitsa zomwe tayankhula.

Ndipamene Allah Taala adavumbulutsa aya ya Qur-aan Majiid:

يأَيُّهَا النَّاسُ إِنَّا خَلَقْنَاكُم مِّن ذَكَرٍ وَأُنثَى وَجَعَلْنَكُمْ شُعُوبًا وَقَبَابِلَ لِتَعَارَفُوْا إِنَّ أَكْرَمَكُمْ عِندَ اللَه أَتْقَاكُمْ إِنَّ اللَّهَ عَلِيمٌ خَبِيْرٌ

E inu anthu! Tidakulengani kuchokera m’gulu limodzi la mwamuna ndi mkazi (Nabiy Aadam [alaihis salaam) ndi mkazi wake olemekezeka Hawwa [alaihas salaam]), ndipo tidakuchitani kukhala mitundu ndi mafuko kuti mudziwane. Ndithu, olemekezeka kwambiri mwa inu pamaso pa Allah ndi yemwe ali oopa kwambiri (kuopa Allah Taala), ndipo Allah Ngodziwa (zonse) ndipo akudziwa (zonse zomwe zikuchitika). (Surah Hujuraat)

(Tafseer Baghawi 4/195, Ibn Hishaam 4/43, Subulul Hudaa war Rashaad 5/248, Zaadul Ma’aad 3/358-361)

Check Also

Olemekezeka Abu Zar (Radhwiyallahu ‘anhu) Kulemekeza Alendo

‘Isa bin ‘Umailah (Rahimahullah) akufotokoza za munthu wina amene adawona khalidwe la Abu Zar (Radhwiyallahu …