Yearly Archives: 2021

Ubwino wa Muadhin

5. Muadhin walonjezedwa kuti adzakhululukilidwa machimo ake Chimodzimozinso kwapatsidwa kwa iye nkhani yabwino yoti kuti Muadhin amadalitsidwa popatsidwa malipiro (sawabu) mofanana ndi amene abwera kudzapemphera malingana kuti iwowo ayankha kuitana kwa Muadhiniyo.

Read More »

Zikhulupiliro Zokhudza Qiyaamah

1. Qiyamah idzachitika lachisanu. Amenewa adzakhala mapeto a dziko lapansi. Allah Tabaaraka wata’ala adzaliononga dziko lonse lapansili. Palibe amene akudziwa za tsiku limene dziko lidzathe.[1] 2. Allah Ta’ala adzamula Mngelo Israafeel (alaihis salaam) kuti ayimbe lipenga lomwe liri ndi maonekedwe onga nyanga manvekedwe alipengali adzayamba motsika ndipo azidzakwera pang’onopang’ono kufikira …

Read More »

Zotsatira Za Msonkhano Umene Unasowekera Zikr Komanso Durood

Sayyiduna Jaabir (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti nthenga wa Allah (madalitso ndi ntendere zipite kwa iye) adati, nthawi ina iliyonse imene anthu asonkhana ndikumaliza nkumano wawowo ndikumwazikana popanda kumutchula Allah kapena kumufunira zabwino Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) pankumanowo, ziri ngati kukumana pamalo pomwe pali fungo lonyasa la chinthu chakufa ndipo kenaka amwazikana.(nkumano umene wayamba ndikutherapo popanda kutchula dzina la Allah lafaniziridwa ndi malo omwe ndi onyasisitsa lomwe palibe munthu angalakelake kukhalapo.

Read More »

Ubwino wa Muadhin

3. Pali mphotho zochuluka zomwe adzalandire ndi munthu amene amapanga Adhaan.

Olemekezeka Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati: “anthu akadakhala kuti akudziwa malipiro aakulu amene amapeza mukuchita adhaan komanso kuswali utaima nzere oyamba Ndipo Pamapeto ake sipakadapezeka kusemphana kulikonse posankha kupatula kupanga mayele ndithu akadapanga mayele kuti apanga chiganizo."

Read More »

Zikhulupiliro Zokhudza Taqdeer (Chikonzero)

1. Taqdeer imatanthauza nzeru zobisika ndi zakuya zimene Allah alinazo, tanthauzo lina ndikuti Allah yekha ndi amene amadziwa chinachirichonse komanso zochitika mtsogolo, chabwino kapena choipa kaya zam’mbuyo zatsopano ngakhalenso za mtsogolo iye amazidziwa kale (kuti zochitika) zisanachitike.[1] 2. Allah Tabaaraka wataala adawapatsa anthu chisankho chochita zabwino kapena zoipa, pa zabwino …

Read More »

Kuyankhidwa Kwa Ma Duwa

Umar (radhwiyallahu anhu) akulongosora kuti: Duwa imakhala idakali pakati pa mitambo ndi nthaka (munlengalenga). Siimapititsidwa mpakana kumwamba ngati muduwamo simunawerengedwe Durood (kutanthauza kuti sipamakhala chitsimikizo cha kuyankhidwa kwa duwayo).

Read More »

Ubwino wa Muadhin

Adhaan ndi chimodzi mwazizindikiro za chisilamu, chisilamu chimalemekeza kwambiri anthu amene amapanga Adhaan, kuwaitanira anthu kuti adzaswali.Tsiku lachiweluzo anthu adzawasilira anthu amene ankachita adhaan padziko lino lapansi chifukwa cha ulemelero umene anthuwa adzakhale nawo. Ma hadith ochuluka alongosora za maubwino a muadhin ndi zabwino zimene akalandire patsikuli. 1. Muadhin adzakhala …

Read More »

Zikhulupiliro zokhudza mabukhu a Allah

5. Quran ndi bukhu lomaliza ndipo idavumbulutsidwa kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Kudzera mukuvumbulutsidwa kwa Quran mabukhu ena onse adachotsedwa. 6. Allah Ta’ala adatenga udindo oyiteteza Quran kufikira tsiku la Qiyaamah, kotero, palibe kusintha kapena kupungula kulikonse komwe kungachitike ku bukhu limeneri. Tidakali mkati molongosora za mabukhu olemekezeka, Allah adapeleka …

Read More »

Kuona Malo Ako Ku Jannah

Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “amene anganditumizire Durood ka 1000 tsiku lachisanu, sadzamwalira kufikira ataonetsedwa malo ake ku Jannah.”

Read More »

Zikhulupiliro zokhudza mabukhu a Allah

1. Allah Ta’ala adavumbulutsa mabukhu osiyanasiyana kwa aneneri osiyanasiyana (ntendere wa Allah upite kwa iwo)kuti adzawaongole anthu. Tauzidwapo za mabukhu amenewa mu Quran yolemekezeka komanso mma hadith ndipo za mabukhu ena sitinadziwitsidwe.[1] 2. Timakhulupilira mabukhu onse amene adavumbulutsidwa ndi Allah kwa atumiki onse monga m’mene adavumbulutsidwira. Ndipo sitimakhulupilira m’mabukhu amene …

Read More »