Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adanena kuti " nyumba zanu musazipange kukhala ngati ndi manda (zipangeni nyumba zanu kukhala za moyo popangilamo ntchito za bwino monga ngati swalah, kuwerenga Qur’aan majeed ndi zina zambiri. Choncho mukamatero nyumba zanu sizikhala ngati ndi manda kumene sikumachitikako ma aamaal abwino.) Ndipo manda anga musawatenge ngati ndi malo opangilapo zisangalalo, komanso mudziwerenga durood kwa ine, ndithudi mwa njira ina iliyonse Durood yo imandifika (kudzera mwa angelo) kuchokera kwina kuli konse komwe muli."
Read More »Yearly Archives: 2021
Masunnah Ndi Aadaab (miyambo) Ya Pa Kusamba – Gawo 1
1. Yang’anani ku Qiblah (komwe timayang’ana tikamaswali) mukamasamba. ndibwino kuvala chovala kutchinga maliseche pamene mukusamba.
2. Sambirani malo omwe wina sangakuoneni. ndibwino kusamba mutaphimba maliseche anu. komano ngati wina ali malo omwe sangaonedwe ndimunthu wina (ngati kubafa) ngati wina akusamba maliseche, ndizoloredwa.
Read More »
Kufika Kwa Durood Ya Ummah Kwa Sayyiduna Rasulullaah (Sallallahu Alaih Wasallam)
Hazrat Hassan Bin Ali (radhiyallahu anhuma) akufotokoza kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adanena kuti "Werengani durood kwa ine kwina kulikonse komwe mungakhale popeza durood yanuyo imafikitsidwa kwa ine (kudzera mwa angelo).
Read More »Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo La chisanu Nchinayi
25. Ngati mbali iliyonse yachiwalo chomwe ndi fardh kusambitsa pamene mukupanga wudhu yasiidwa osasambitsa, wudhu udzakhala opelewera.
Sayyiduna Umar (radhwiyallahu anhu) akunena kuti munthu anapanga wudhu nasiya malo amodzi osasambitsa kuphanzi kwake mlingo wachikhadabu poyang’anitsitsa malo amenewo Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) anamuuza iye kuti “pita ukamalizitse kupanga wudhu wako.”
Read More »
Kupempha Chabwino Kuyambira Pa Tsinde Lake
Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, "amene amawerenga Qur'an, amatamanda Allah Ta'ala, amawerenga Durood kumuwerengera Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) komanso amapempha chikhululuko kwa mbuye wake ndiye kuti wapempha zabwino kuyambira pa tsinde lake (kutanthauza kuti wachita ntchito zabwino zomwe ndi Chiyambi cha zabwino Zathu.
Read More »Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo La chisanu Nchitatu
21. Sisitani (kukhula/kutikita ndi dzanja lanu) ziwalo zanu mokwanilira pamene mukusambitsa ndicholinga choti madzi afike paliponse.
22. Ziwalo zonse ziyenera kutsukidwa china pambuyo pachinzake mosachedwetsa.
Read More »Kuona Malo Ako Ku Jannah
Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “amene anganditumizire Durood ka 1000 tsiku lachisanu, sadzamwalira kufikira ataonetsedwa malo ake ku Jannah.”
Read More »Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo La Chisanu Nchiwiri
18. Mukamaliza wudhu, welengeni shahaadah ngati muli malo otakasuka, popanga shahaadah[1] yang’anani kumwamba, momwemonso werengani duwa iliyonse yomwe imabwera m’mahadith. Ena mwamaduwa a sunnah amene anenedwa m’mahadith oyenera kuwerengedwa pamapeto popanga wudhu ndi awa m’musimu: Duwa yoyamba: Amene angawerenge duwa imeneyi makomo asanu ndi atatu a ku Jannah amatseguka kuti …
Read More »Zofuna Zathu Zokwana 100 Kukwaniritsidwa
Sayyiduna Jaabir (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, "amene angawerenge Durood ka 100 tsiku lirilonse, Allah Ta'ala adzakwaniritsa zofuna zake zokwana 100, 70 adzalandira pa tsiku la Qiyamah ndipo 30 adzapatsidwa padziko pompano.
Read More »Kuikonzekera Ramadhan
27. Pangani itikafu (M´bindikiro) masiku khumi otsirizira a mwezi wa Ramadan ngati mungakwanitse kutero.
Olemekezeka Ibn Abbas (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adanena zokhudza kukhala mu itikafu kuti: ‘’Munthu amene akupanga itikafu (akubindikira munzikiti) amakhala kutali ndi machimo ndiponso nthawi yomweyo amalandila mphotho za ntchito zomwe akadatha kuzigwira pamene iye asali mu itikaafu.
Read More »