Kuikonzekera Ramadhan

27. Pangani itikafu (M´bindikiro) masiku khumi otsirizira a mwezi wa Ramadan ngati mungakwanitse kutero.

عن ابن عباس الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه و سلم قال في المعتكف هو يعتكف الذنوب ويجري له من الحسنات كعامل الحسنات كلها (سنن ابن ماجة، الرقم: ٢١٠٨)

Olemekezeka Ibn Abbas (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adanena zokhudza kukhala mu itikafu kuti: ‘’Munthu amene akupanga itikafu (akubindikira munzikiti) amakhala kutali ndi machimo ndiponso nthawi yomweyo amalandila mphotho za ntchito zomwe akadatha kuzigwira pamene iye asali mu itikaafu.

عن ابن عباس الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال من اعتكف يوما ابتغاء وجه الله تعالى جعل الله بينه وبين النار ثلاث خنادق أبعد مما بين الخافقين رواه الطبراني في الأوسط والبيهقي واللفظ له (الترغيب والترهيب الرقم: ١٦٥٠)

Olemekezeka Abbas (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu lallah alayhi wasallam) adati ‘’Amene angakhale mu M’bindikiro (itikafu) tsiku limodzi lokha pofunafuna Chisangalaro cha Allah Ta’ala, Allah Ta’ala adzaika pakati pa iyeyo ndi moto wa Jahannam zitchingo zitatu, Kukula kwa tchingo lililonse ngati mtunda umene uli pakati pa ku m’mawa ndi kumadzulo.

28. Kusakasaka usiku umene umatchedwa kuti Laylatul Qadr (usiku wa mphamvu) m’masiku khumi omaliza m’mwezi wa Ramadhan omwe nambala yake siigawidwa ndi 2.

عن أنس بن مالك قال: دخل رمضان فقال رسول الله صلى الله عليه وسلم: إن هذا الشهر قد حضركم وفيه ليلة خير من ألف شهر من حرمها فقد حرم الخير كله ولا يحرم خيرها إلا محروم (سنن ابن ماجه، الرقم: ١٦٤٤)

Sayyiduna Anas (radhwiyallahu anhu) akulongosola kuti, pamene Ramadhan inayambika, Sayyiduna Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adanena kuti, ndithu mwezi uwu (wa Ramadhan) wakubwererani, ndipo mkati kati mwake mwa mwezi umenewu mukupezeka usiku omwe ndi olemekezeka kuposa miyezi yokwana zana limodzi (1000). Munthu amene angamanidwe usiku umenewu (kumudutsa osapanga ibaadah iliyonse) ndiye kuti wamanidwa zabwino zonse, ndipo kumanidwa usiku umenewu ndiko kumanidwa kwa zabwino kwenikweni.

29. Mu usiku wina mwa ma usiku amene sagawidwa ndi 2 amenewa muyenera kuchulukitsa kupanga ibaadah. Pamene mukukagona mu usiku oterewo, mukuyenereka kupanga niyyah yoti mudzukiranso usiku kuti mupange ibaadah yambiri. Yesetsani kupanga ibaadah musanapite kukagona, Popeza kuti pamatha kukhala kuthekera koti mutha kulephera kudzukira kuti mupange ibaadayo.

30. Mu usiku wa mphamvu umenewu muwerenge dua yotsatirayi

اَللّٰهُمَّ إِنَّكَ عَفُوٌّ تُحِبُّ الْعَفْوَ فَاعْفُ عَنِّيْ

O Allaah ndithudi inu mumakonda kukhululuka choncho ndikukupemphani kuti mundikhululukile.

عن عائشة قالت: قلت يا رسول الله أرأيت إن علمت أي ليلة ليلة القدر ما أقول فيها ؟ قال قولي اللهم إنك عفو تحب العفو فاعف عني قال هذا حديث حسن صحيح (سنن الترمذي، الرقم: ٣٥١٣)

Sayyidatuna Aisha (radhwiyallahu anha) akulongosora kuti nthawi ina adamufunsa Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) kuti ndi duwa yanji yomwe angawerenge ngati angaupeze usiku wa mphamvu. Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) anamuphunzitsa kuti adziwerenga duwa yotsatirayi

اَللّٰهُمَّ إِنَّكَ عَفُوٌّ تُحِبُّ الْعَفْوَ فَاعْفُ عَنِّيْ

31. Munthu amene amapemphera swalah ya Eshah komanso subuhi limodzi ndi Jamaat komanso ndi kupemphera ma rakaa 20 a Tarawehi kumbuyo kwa Imaam, Allaah amampatsa malipilo okuti usiku onse wachezera kupanga ibaadah ndipo ngati usiku umenewo unali wa Laylatul Qadr ndiye kuti adzapeza malipilo okuti wapanga ibaadah usiku wa Laylatul Qadr.

عن عثمان رضي الله عنه قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: من صلى العشاء في جماعة فكأنما قام نصف الليل ومن صلى الصبح في جماعة فكأنما صلى الليل كله (صحيح مسلم، الرقم: ٦٥٦)

Sayyiduna Uthman (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) anati munthu amene angapemphere swalah ya Eshah limodzi ndi Jamaat (munzikiti) amakhala ngati wapanga ibaadah theka la usiku ndipo munthu amene angapemphere swalah ya Eshah limodzi ndi Jamaat, kenakonso ndikudzapemphera swalah ya subuhi limodzinso ndi Jamaat munzikiti, Allah amampatsa malipilo ngati wachezera Usiku onse kupanga ibaadah.

عن أبي ذر: قال … فقام بنا حتى ذهب ثلث الليل ثم لم يقم بنا في السادسة وقام بنا في الخامسة حتى ذهب شطر الليل فقلنا له يا رسول الله لو نفلتنا بقية ليلتنا هذه ؟ فقال إنه من قام مع الإمام حتى ينصرف كتب له قيام ليلة (سنن الترمذي، الرقم: ٨٠٦)

Sayyiduna Abu Zarr (radhiyallahu anhu) akulongosola kuti mu usiku wa 25 m’mwezi wa Ramadhan, Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) anatiswalitsa swalah ya Tarawehi mpakana kufika pakati pa usiku padadutsa (tidali okondwa kuswali Tarawehi imeneyi mpakana) kumapeto kwa swalayo mpakana tinamuuza Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) kuti bolani mukanapitiriza mpakana kumapeto kwa usiku onse! Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adanena kuti munthu amene angaime usiku kupemphera limodzi ndi Imaam wake, Allaah Ta’ala amamulembela malipilo okuti wapemphera usiku onse.

32. Usiku okuti mawa lake ndi Idi tengani ka nthawi pang’ono kupanga ibaadah.

عن أبي أمامة رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه و سلم قال من قام ليلتي العيدين محتسبا لم يمت قلبه يوم تموت القلوب رواه ابن ماجه ورواته ثقات إلا أن بقية مدلس وقد عنعنه (الترغيب والترهيب، الرقم: ١٦٥٥)

Sayyiduna Abu Umaamah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) anati munthu wina aliyense amene angaime m’masiku ama Idi onse awiri kupanga ibadah ndi chiyembekezo chofuna kupeza zabwino kuchokera kwa Allaah, mtima wake siudzakhala wakufa pamene mitima ya anthu ena idzakhala yakufa (kutanthauza kuti mnthawi ya mayesero pamene anthu azidzakhala akunyozera malamulo a Allaah, m’nthawi imeneyo Allaah adzaupatsa mtima wake umoyo pompatsa mwayi okuti azidzam’kumbukira Allaah).

33. Mwezi wa Ramadhan ukatha aliyense ayesetse kuti asale nawo masiku asanu ndi limodzi (6) a Sunnah m’mwezi wa shawwaal.

عن أبي أيوب الأنصاري أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال: من صام رمضان ثم أتبعه ستا من شوال كان كصيام الدهر. (صحيح مسلم، الرقم: ١١٦٤)

Sayyiduna Abu Ayyuub Al Ansari (radhiyallahu anhu) akulongosola kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adanena kuti wina aliyense amene angasale kudya mwezi wa Ramadhan kenaka ndi kudzatsatizanso kusala kudya masiku 6 a mwezi wa Shawwaal, ndiye kuti adzapeza malipilo oti wasala kudya kwa chaka chonse.

Check Also

Chikondi Cha Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) Kumukonda Nabi (sallallahu alaih wasallam)

Nabi (sallallahu alaih wasallam) adawuyamba nsamuko pamodzi ndi Abu Bakr (radhwiyallahu) anhu chakumadzulo, nkatikati mwa …