Nthawi Zimene Miswak Ikufunika Kugwirtsidwa Ntchito

4. Pamene mukupanga wuzu.[1]

عن أبي هريرة رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم لولا أن أشق على أمتي لأمرتهم بالسواك عند كل وضوء (صحيح البخاري تعليقا ١/٢٥٩)

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akuakufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih Wasalaam) adati, “chikhala kuti sichipsinjo pa ummah wanga ndikadawalamula (ndikadazipanga kukhala zokakamiza) kuti adzigwiritsa ntchito miswaak nthawi inailiyonse pamene akupanga wudhu (komano Sizili zokakamiza kutero koma ndisunnah yomwe yalimbikitsidwa pamene mukupanga wudhu).”

5. Pamene mano asintha ntundu kapena mkamwa mukutulutsa fungo loipa (chifukwa chosatsuka).[2]

عن جعفر بن أبي طالب رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم أنه قال ما لي أراكم تدخلون علي قلحا استاكوا ولولا أن أشق على أمتي لأمرتهم أن يستاكوا عند كل صلاة (كتاب الآثار، الرقم: ٤١)

Zafotokozedwa kuchokera kwa Sayyiduna Ja’far (radhiyallahu anhu) kuti nthawi inayake Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adawayankhula anthu ena ake kuti “vuto lanu ndichani ndimakuonani nthawi zina mano anu atasintha ntundu kubwera chikasu/yelo, ndikukulangizani kuti muzitsuka mano anu pogwiritsa ntchito miswaak” kenaka Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, kukadakhala kuti sichingakhale chipsinjo kwa ummah wanga, ndikadawalamula (ndikupanga kukhala zokakamiza kwa iwo) kuti azitsuka mkamwa pogwiritsa ntchito miswaak nthawi zonse za swalah (komano kugwiritsa ntchito miswaak sikokakamiza koma ndisuunah yomwe yolimbikitsidwa kutsatira pamene tikupanga wudhu).”

عن عبد الله بن بشر المازني رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم قصوا أظافيركم وادفنوا قلاماتكم ونقوا براجمكم ونظفوا لثاتكم من الطعام وتسننوا ولا تدخلوا علي قخرا بخرا (نوادر الأصول تحت الأصل التاسع والعشرين في باب النظافة)[3]

Sayyiduna Abdullah Bin Bishr (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, wengani zikhadabu zanu ndikuzikwilira pansi, tsukani bwino mmajoini mwanu, nkhama zanu zisamalireni ndipo musabwere kwaine pamene mano anu asanduka achikasu ndipo mkamwa mwanu mukutulutsa fungo lonunkha.

6. Musanadye komanso mukamaliza kudya.[4]

عن أبي هريرة رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال إن كان قاله لولا أن أشق على أمتي لأمرتهم بالسواك مع الوضوء وقال أبو هريرة رضي الله عنه لقد كنت أستن قبل أن أنام وبعد ما أستيقظ وقبل ما آكل وبعد ما آكل حين سمعت رسول الله صلى الله عليه وسلم يقول ما قال (مسند أحمد، الرقم: ٩١٩٤)[5]

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati ndpo mawuwa ndithudi adayankhuladi, “chikhala kuti sichikhala chipsinjo pa ummah wanga ndikawalamula kuti (ndikuwakakamiza) adzigwirtsa ntchito miswaak nthawi ina iliyonse pomwe angapange wudhu (komano Sizili fardh kugwiritsa ntchito miswaak koma kuti ndi sunnah yomwe ndi yolimbikitsidwa kwambiri kutsatira).” Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akupitiriza kuyankhula kuti kudzera mu kulimbikitsa kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) pankhani yogwiritsa ntchito miswaak ndidasankha kukhala chizolowezi changa kuti ndidzigwiritsa ntchito miswaak pamene ndikugona, ndikadzuka, ndisanayambe kudya komanso ndikamaliza kudya.”


[1] وأما سنن الوضوء فكثيرة إحداها السواك وهو سنة مطلقا ولا يكره إلا بعد الزوال لصائم وفي غير هذه الحالة مستحب في كل وقت ويتأكد استحبابه في أحوال … وعند الوضوء وإن لم يصل … ويحصل السواك بخرقة وكل خشن مزيل لكن العود أولى والأراك منه أولى … ولا يحصل بأصبع خشنة على أصح الأوجه … ويستحب أن يستاك عرضا (روضة الطالبين ١/١٦٧)

[2] ويتأكد استحبابه في أحوال … وعند اصفرار الأسنان وإن لم يتغير الفم وعند تغير الفم بنوم أو طول سكوت أو ترك أكل أو أكل ما له رائحة كريهة أو غير ذلك (روضة الطالبين ١/١٦٧)

[3] قال صاحب نوادر الأصول وقوله لا تدخلوا علي قخرا بخرا المحفوظ عندي قلحا وقحلا والأقلح الذي اصفرت أسنانه حتى بخرت من باطنها ولا نعرف القخر والبخر إلا الذي نجد له رائحة منكرة يقال رجل أبخر ورجال بخر

[4] (ويسن للصلاة) … وللأكل (مغني المحتاج 1/166)

[5] قال الهيثمي: رواه أحمد ورجاله ثقات (مجمع الزوائد، الرقم: 1119)

Check Also

Njira Ya Sunnah Yogwiritsira Ntchito Miswaak (mswachi ochokera ku mtengo)

1. Njira yogwilira miswaak ili motere, Munthu ayenere ayike chala chachikulu ndi chaching´ono pansi pa …