7. Pamene wina ali kumapeto kwa moyo wake (ali pafupi kumwalira).[1]
عن عائشة رضي الله عنها قالت دخل عبد الرحمن بن أبي بكر ومعه سواك يستن به فنظر إليه رسول الله صلى الله عليه وسلم فقلت له أعطني هذا السواك يا عبد الرحمن فأعطانيه فقصمته (وفي رواية وطيبته) ثم مضغته فأعطيته رسول الله صلى الله عليه وسلم فاستن به وهو مستند إلى صدري (صحيح البخاري، الرقم: ٨٩٠)
Sayyidatuna Aisha (radhiyallahu anha) akufotokoza kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) atatsala pang’ono kumwalira, nchimwene wanga amene ndi AbdulRahmaan (radhiyallahu anhu) adalowa mchipinda chomwe Mtumiki (sallallah alaih wasallam) adagona atanyamula miswaak yomwe ankagwiritsa ntchito kutsukira mkamwa. Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) maso ake adagwera pa miswaakiyo (komano sadakwanitse kuti ayitanitse chifukwa chofooka, ndidazindikira kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) akufuna miswaak) kotero ndidamupempha nchimwene wangayu kuti, oh AbduRahmaan, tandibwerekako miswaak yakoyo.’ndidatenga ndikuthyola kuntunda kwake, (kenaka ndidautsuka ndikuufewetsa) ndipo kenaka ndidampatsa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adagwiritsa ntchito uku atatsamira pachidali panga.”
8. Nthawi ya swalah.[2]
9. Usadakakhale nawo pa gulu la anthu ngati pa swalah ya Jumuah, Eid kapena nkumano ulionse.[3]
10. Pamene mukupanga Tayammum chifukwa choti mwadwala kapena kusapezeka kwamadzi kapena madzi alipo koma ndi osakwanira kupangira wudhu mukuyenera kutsuka mkamwa pogwiritsa ntchito miswaak.[2]
[1] (ويسن للصلاة) … وعند الاحتضار (مغني المحتاج 1/166)
[2] (ويسن للصلاة) ولو نفلا ولكل ركعتين من نحو التراويح أو لمتيمم أو فاقد الطهورين أو صلاة جنازة ولو لم يكن الفم متغيرا (مغني المحتاج 1/166)
[3] (ويسن للصلاة) … ولإرادة أكل
(قوله ولإرادة أكل إلخ) أي أو جماع لزوجته أو أمته وعند اجتماعه بإخوانه (حواشي الشرواني على تحفة المحتاج 1/233)