Munthu yemwe ndi waumbombo

عن حسين بن علي بن أبي طالب قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: البخيل الذي من ذكرت عنده فلم يصل علي (سنن الترمذي، الرقم: ٣٥٤٦، وقال هذا حديث حسن صحيح غريب)

Sayyiduna Husain (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki wa Allah (madalitso ndi ntendere zipite kwa iye) adati, “munthu waumbombo ndi amene amati akanva dzina langa samandifunira zabwino ponditumizira durood”.

Kupanga ulendo ndicholinga chokaphunzira Hadith imodzi yokha

Sayyiduna Kathir bin Qais (rahimahullah) akulongosola kuti:

Tsiku linalake ndiri limodzi ndi Sayyiduna Abu Dardaa (Radhiyallahu anhu) munzikiti ku Damascus, padadzabwera munthu wina kwa iye nati, ‘’Eee Abu Dardaa (Radhiyallahu anhu), Ndayenda ntunda wautali kuchokera ku Madinah Tayyibah kudzafufuza Hadith imodzi kuchokera kwa inu, monga mmene ndidaphunzirira kuti inu mudamumva Mtumiki (swalallahu alyihi wasallam) mwiniwake”.

Sayyiduna Abu Dardaa Radhiyallahu anhu adamufunsa “Umagwira ntchito ku Dumascus?” Munthu uja adayankha, “Ayi (Basi Ndabwera kuchokera ku Damascus kudzaphunzira Hadith)”. Sayyiduna Abu Dardaa (radhiyallahu anhu) adamufunsa kenanso, “Ukunena zowona kuti ku Damascus ulibe ntchito yomwe umagwira?” Munthu uja adayankhanso kuti, “Ndabwera ndi mtima onse ndi cholinga chodzaphunzira Hadith imeneyi.”

Sayyiduna Abu Dardah (radhiyallahu anhu) adati: ‘’tanvetsera ndidamunva mthenga wa Allah (madalitso ndi ntendere zipite kwa iye) akunena kuti Allah amanfewetsera njira yokalowera ku jannah munthu yemwe wayenda ulendo kupita kukaphunzira maphunziro a dini, angelo amatambasura mapiko awo pansi pa mapazi ake komanso chinachirichonse chopezeka kumwamba ndi pansi (ngakhale nsomba m’madzi) zimampemphera chikhululuko kwa Allah. Kulemekezeka kwa munthu yemwe ali ndi maphunziro a Dini kuposa munthu yemwe ndiopembedza kwambiri koma alibe maphunzirowa kulingati Kusiyana kwakuwala kwa pakati pamwezi ndi nyenyezi, machehe ndi alowa mmalo a Mtumiki (madalitso ndi ntendere zipite kwa iye), aneneri sadasiye chuma komano adasiya maphunziro a dini, munthu amene waphunzira dini ndithudi ali ndi ulemerelo kuposa munthu wachuma.’’ (Sunan Abi Dawood #3641)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …