Ubwino wa Muadhin

9. Chidali chikhumbokhumbo cha maswahaba (radhiyallahu anhum) kuti azipanga adhaana ndiponso ankalakalaka kuti ana awonso azipanga adhaana.

Mmusimu muli ena mwamahadith amene akuonetseratu poyera kufunitsitsa kwa maswahaba kuti nawo adzipanga adhaana:

kufunisitsa kwa Olemekezeka Ali radhiyallahu anhu kuti ana ake Hassan ndi Hussein (Radiyallah anhumaa) azipanga adhaana.

عن علي رضي الله عنه قال ندمت أن لا أكون طلبت إلى رسول الله صلى الله عليه وسلم فيجعل الحسن والحسين مؤذنين (مجمع الزوائد، الرقم: 1836)

Zikufotokozedwa kuti Olemekezeka Ali (radiyallah anhu) adati; Ndikudzidandaulira kuti sindinamupemphe Mtumiki (sallallahu alaihi wasallam) kuti awasankhe ana anga awiri Hassan ndi Hussein (Radhiyallahu anhuma) kuti akhale opanga adhaana.

Kufunisitsa kwa Olemekedzeka Umar (radiyallah anhu) kuti azipanga azaana

عن قيس بن أبي حازم قال قدمنا على عمر بن الخطاب رضي الله عنه فسأل من مؤذنكم فقلنا عبيدنا وموالينا فقال بيده هكذا يقلبها عبيدنا وموالينا إن ذلكم بكم لنقص شديد لو أطقت الأذان مع الخلافة لأذنت (السنن الكبرى للبيهقي، الرقم: 2002)

Qais ibn Hazim (rahimahullah) akusimba kuti “Nthawi ina pamene tidafika ku Madinah Munawwarah kukakumana ndi Umar (radhiyallahu anhu), Mkatikati mwakukambirana kwathu adatifunsa ife kuti; “ndindani amapanga adhaana kudera lomwe mumakhala? “Tidayankha kuti tidasankha akapolo athu kuti azipanga adhaana. Umar (radhiyallah anhu) anapereka masayini ndimanja ake kenako modabwitsa adatsatizira mau athu amene tidayankhula, amvekere” Tasankha akapolo athu kuti azipanga adhaana” kenako Umar adati; Ndithudi uku ndiye kulephera kwanu kwakukulu kwa inu potsankha anthu amtundu umenewu kuti azipanga adhaana kumachita kuti iwowo sakudziwa kanthu padini,(adhaana ndi ibaada yolemekezeka kwambiri ndiponso ili ndimalipiro ochuluka kwambiri) kukanakhala kuti mkotheka kuti ndizipanga adhaana pamodzi ndi utsogoleri wa ukhalifa, ndithudi ndikanavomereza ndikanavomereza udindo wamuadhin kuti ndizipanga adhaana.

وعن عمر رضي الله عنهما أنه قال لو كنت مؤذنا لكمل أمري وما باليت أن لا أنتصب لقيام ليل ولا لصيام نهار سمعت رسول الله صلى الله عليه وسلم يقول اللهم اغفر للمؤذنين ثلاثا قلت يا رسول الله تركتنا ونحن نجتلد على الأذان بالسيوف فقال كلا يا عمر إنه سيأتي زمان يتركون الأذان على ضعفائهم تلك لحوم حرمها الله على النار لحوم المؤذنين (كشف الخفاء، الرقم: ٢١١٨)

Kudanenedwa zokhudza Umar (radhiyallahu anhu) kuti iye adati: “Ndikanakhala kuti ndizotheka kupanga adhaana (pamodzi ndi utsogoleri wa ukhalifa) ndithudi chisangalalo changa chikanakwanilira. (Malipiro opangira adhaana ndi aakulu kwambiri koti kukadakhala kuti ndiri ndiulemerero okhala muadhin kenako ndikukhala osamaswali swala za nafl (zachifuniro) mkatikati mwa usiku tahajjudi kenakonso ndikukhala osamasala swaum yasunnah masanawa, Sizikanandidandaulitsa ine chirichonse. (chifukwa chokhala ine muadhin) ndithudi ndinamumva mtumiki wa Mulungu (sallallah alaihi wasallam) akupangira dua yapadera anthu opanga adhaan akunena kuti: Ambuye Mulungu akhululukireni mamuadhin machimo awo! Mtumiki (salallah alayhi wasalllama) adachita duwa imeneyi mowilikiza katatu. Ine modabwitsidwa ndinati: Inu Mtumiki wa Mulungu (sallallahu alaihi wasallam) (Mwakweze udindo wamuadhin kwambiri mpakana) mwatisiya ife pakondishoni yoti tikhoza kuyamba kumenyana pakati pathu ndimalupanga cholinga choti mmodzi mwaife apeze mwayi opanga azana.

Mtumiki – sallallah alayhi wasallam) adati: Sichoncho iwe Umar (radhiyallah anhu); Nthawi idzafika imene chikhumbokhumbo chopangira adhaana sichidzakhala mmitima ya anthu, ndiudindo waukulu ngati umenewu anthu azidzadalira anthu ofooka mwa iwo kuti azidzapanga azaana. Anthu amenewa (mamuazin) ndi anthu ameme Allah Taala waupanga moto wa Gehena kukhala haraam mmatupi awoke, Matupi ake aanthu opanga adhaana.”

Check Also

Mawu A Iqaamah Komanso Njira Ya Sunnat Yopangira Iqaamah

1. Mawu a Iqaamah ndichimodzimodzi ndi azaana. Koma popanga iqaamah mukuyenera kunena kamodzikamodzi kupatula mawu …