Kupeza nawo pempho la Mtumiki (sallallahua alaih wasallam)

عن ابن عمر عن النبي صلى الله عليه وسلم قال من زار قبري بعد موتي كان كمن زارني في حياتي (المعجم الأوسط، الرقم: 287) رواه الطبراني والدارقطني والبيهقي وضعفه كذا في الإتحاف وفي المشكوة برواية البيهقي في الشعب بلفظ : من حج فزار قبري بعد موتي كان كمن زارني في حياتي واستدل به الموفق في المغني على استحباب الزيارة (فضائلِ حج صـ 184)

Ibnu Umar (radhiyallahu anhuma) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahua alaih wasallam) adati; munthu yemwe angadzazonde/angadzayendere manda anga adzafunikira pempho langa kwa Allah lomupemphela chikhululuko iyeyo pa tsiku lachiweluzo.

Mphoto Zakulemba Mau Oti “Sallallah Alayhi Wasallama”

Hassan bin Muhammad (rahimahullah) akunena kuti:

Ndidamuonapo Imaam Ahmad bin Hambal (rahimahullah) ku maloto, ndipo adati kwaine” Ungathe kuchitira umboni ndi maso ako malipiro aakulu ndi madalitso ochuluka amene akuwala patsogolo pathu amene asungiridwa anthu amene amalemba Durood kwa Mtumiki – (sallallahu alayhi wasallam) m’mabuku mwawo”.

Chidziwitso: Pamene mukulemba dzina la olemekezeka Mtumiki) sallallahu alayhi wasallam), Mukuyenera kulemba mokwanirira mau oti “Sallallahu alayhi wasallam” muchiyankhulo cha charabu kapena mukhonza kulemba muchiyankhulo chilichonse.
Sizili zokwanilira kulemba mofupikitsa monga S.A.W kapena P.B.H.U ndikalembende kena kalikonse kofupikitsa chifukwa kutere sizikupereka ulemu ofunika kuuwonetsa kwa Mtumiki (Sallallahu alayhi wasallam). (Al Qawlul Badee, Pg,486)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …