Tafseer Ya Surah Dhuha

وَالضُّحٰى  ﴿١﴾ وَالَّيْلِ إِذَا سَجٰى ﴿٢﴾ مَا وَدَّعَكَ رَبُّكَ وَمَا قَلٰى ﴿٣﴾ وَلَلْـاخِرَةُ خَيْرٌ لَّكَ مِنَ الْاُولٰى ﴿٤﴾ وَلَسَوْفَ يُعْطِيكَ رَبُّكَ فَتَرْضٰى ﴿٥﴾ اَلَمْ يَجِدْكَ يَتِيمًا فَـاوٰى ﴿٦﴾ وَوَجَدَكَ ضَآلًّا فَهَدٰى ﴿٧﴾ وَوَجَدَكَ عَآئِلًا فَاَغْنٰى ﴿٨﴾ فَاَمَّا الْيَتِيمَ فَلَا تَقْهَرْ ﴿٩﴾ وَاَمَّا السَّآئِلَ فَلَا تَنْهَرْ ﴿١٠﴾ وَاَمَّا بِنِعْمَةِ رَبِّكَ فَحَدِّثْ ﴿١١﴾

Ndikulumbilira mmawa dzuwa litakwera (imene ili nthawi ya ntchito), ndi usiku pamene ukuvindikira, sadakusiye mbuye wako (iwe mneneri) (sallallahu alaih wasallam) ndiponso sadakude, ndithu moyo watsiku lomwe lirimkudza ndiwabwino kwa iwe kuposa umoyo oyambawu, ndiponso ndithu posachedwapa akupatsa mbuye wako (zabwino zamdziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro) ndipo usangalala, kodi sadakupeze uli wamasiye ndipo adakupatsa pokhala pabwino?, ndipo adakupeza uli osazindikira (Quran) nakuongola pokuzindikiritsa Quraaniyo ndi malamulo achipembedzo)? Ndiponso adakupeza uli osauka ndipo adakulemeretsa? basi wamasiye usamchitire nkhanza, ndiponso opempha usamukalipire, tsono ntendere wambuye wako uwutchule (pothokoza ndikuchita ntchito zabwino.

Mmasiku oyambilira achisilamu apatu nkuti Mtumiki wa Allah madalitso ndi ntendere zipite kwa iye adakali ku Makka Mukarramah sadalandire wahyi kuchokera kwa Allah kwamasiku angapo, chifukwa cha zimenezi makafiri aku Makkah adayamba kumunyoza Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ponena kuti: mbuye wako sakusangalatsidwa nawe kotero sakukutumiziranso wahyi.

Mnyozo otere ndizachidziwikire kuti ndiopweteka kwa munthu wina aliyense, ngakhale ziri chonchi, komabe Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adali ndi chikhulupiliro kuti Allah alinaye limodzi ndipo Allah sadakhumudwe naye kapena kunyansidwa naye, pofuna kumukhazikitsa ntima pansi komanso ngati phunziro kwa ummah onse Allah adavumbulutsa Surah imeneyi imene ikulongosora kuti anthu onse amene akuchita zinthu ndicholinga chofuna kusangalatsa  Allah ndipo akukumana ndi mavuto osiyanasiyana asaganizire ngakhale pang’ono kuti Allah wawataya kapena kukhala ndi maganizo oti Allah sakusangalatsidwa nawo.
Kotero, Allah akuyamba ndi surayi motere.

وَالضُّحٰى  ﴿١﴾ وَالَّيْلِ إِذَا سَجٰى ﴿٢﴾ مَا وَدَّعَكَ رَبُّكَ وَمَا قَلٰى ﴿٣﴾

Ndikulumbilira mmawa dzuwa litakwera (imene ili nthawi ya ntchito), ndi usiku pamene ukuvindikira, sadakusiye mbuye wako (iwe mneneri) (sallallahu alaih wasallam) ndiponso sadakude.

Mu mavesi amenewa, Allah Ta’ala akulumbilira mmawa omwe uli ndi kuwala komanso usiku omwe uli ndi mdima, muzinthu ziwirizi muli uthenga onena kuti munthu ayenera kudutsa munyengo zosiyanasiyana ndipo monga mdima ukadza ndiye kuti chotsatira chake ndi kuwala zirinso chimodzimodzi kuti pambuyo pamavuto pamabwera ntendere.
Kotero, ngati munthu angakumane ndi nthawi zamasautso asamaganize ngati Allah wakwiya naye kapena kumutaya, komano akungofunika kuti atembenukire kwa Allah ndikukhala otsatira malamulo ake nthawi zonse.

وَلَلْـاخِرَةُ خَيْرٌ لَّكَ مِنَ الْاُولٰى

Ndithu moyo wa tsiku lirimkudza ndiwabwino kwa iwe kuposa umoyo woyambawu.

Tanthauzo la Ayah imeneyi ndilokuti umoyo omwe ulimkudza ndiwabwino kwambiri kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) poyerekeza ndi umoyo wapadziko lino lapansi. Komabe zikhonza kutanthauzaso kuti Nyengo yomwe ilimkudza zikhale zabwino kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) poyerekeza ndi nyengo yomwe yadutsa.

Mmawu ena, iyi ndi nkhani yabwino yapaderadera ya Mtumiki (sallallah alaih wasallam) kunena kuti Allah apitilizabe kumudalitsa, kumuonjezera nzeru, kumuzindikra Allah ndikuyandikira kwa iye. Palinso chizindikiro chakuonjezeredwa kwa chakudya chake, ulemelero wake komanso utsogoleri wake.

Sizikuthera pomwepo, monga Ayah imeneyi ikutiuzira za nkhani yabwino yomwe ikuperekedwa kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), ndichirimbikitsonso kwa anthu ochita ntchito zabwino kuti adzikhala ndichiyembekezo nthawi zonse kuti chifundo cha Allah chiri pa iwo.

Ngati munthu yemwe ndi okhulupilira angakhanzikike pa sunnah ya Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) nthawi zonse pamoyo wake ndikumenya nkhondo yodziyandikitsira kwa Allah ndiye kuti nyengo ina iliyonse yomwe ingadze kwa iye idzakhala yabwino kuposa yomwe yadutsa. Chifukwa Allah adzapitiliza kumuonjezera nzeru ndichina chirichonse.
Kotero, ngati angamadutse mnyengo zopweteka asamakhumudwe kapena kutaya mtima. Mmalo mwake akuyenera kubwelera kwa Allah ndikukhala ndi chiyembekezo kuti Allah amuchitira chifundo.

وَلَسَوْفَ يُعْطِيْكَ رَبُّكَ فَتَرْضٰى

Ndithu posachedwapa akupatsa mbuye wako (zabwino zamdziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro) ndipo ukondedwa.

Kuchokera pa Ayah imeneyi tikuona kuti Allah akumudziwitsa Mtumiki wake okondedwa kuti iye akwaniritsa zofuna zake zonse kufikira kuti iye (Mtumikiyo sallallahu alaih wasallam) asangalala.

Limodzi mwa Khumbo lomwe Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adalinawo ndiye loti chisilamu chifalikire pena paliponse komanso kuti asilamu apambane nkhondo zawo zolimbana ndi adani awo. Zonsezi ziri mgulu la mitendere imene Allah adamulonjeza.

Zanenedwa mu hadith kuti ayah imeneyi itavumbulutsidwa Mtumiki (sallallahua alaih wasallam) adanena kuti:

إذا والله لا أرضى وواحد من أمتي في النار.

Sindidzasangalala kuona nsilamu ngakhale m’modzi akukalowa ku Jahannam.

Kuchokera pa Hadith imeneyi, tikuphunzirapo za chikondi chimene Mtumiki (sallallahua alaih wasallam) adali nacho pa ummah wake, pamene iye sadapeze Chisangalaro kuti ngakhale munthu m’modzi akavutike ku moto wa Jahannam. Mukunena kwina, Mtumiki (sallallahua alaih wasallam) amaukonda ummah wake kwambiri ndipo Khumbo lake ndi lonena kuti wina aliyense wa ummah wake akalowe ku Jannah. Kotero pa tsiku la Qiyamah Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adzawapemphera kwa Allah anthu ake kuti akalowetsedwe ku Jannah.

Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) amaukonda ummah wake ndipo chikondi chake ndichovuta kuchiganizira, chikondi cha Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) chikufunika chitipangitse ife monga ummah wake kukhulupilika kwa iye komanso kumutsatira ndikumunvera nthawi zonse. Kuti zimenezi zitheke pakufunika zinthu ziwiri zomwe ndizofunikira kwambiri.

Choyambilira ndikuti tikufunika kutsatira sunnah ya Mtumiki (madalitso ndi ntendere zipite kwa iye) muchina chirichonse chomwe tingachite pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku nthawi zonse komanso kutalikirana ndi zinthu zimene zingabweretse mkwiyo wake pa ife komanso zonse zimene adatiletsa. Kudzera mukuchita zimenezi, komanso kudzera mukutsatira sunnah yake ndi mtima onse tidzakhala kuti tikuonetsa kuthokoza komanso kuyamika pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam).

Chachiwiri chake ndichakuti tidziwerenga Durudu kawirikawiri makamaka lachisanu, kuchita zimenezi kudzabweretsa Chisangalaro mu mtima wa Mtumiki madalitso ndi ntendere zipite kwa iye.

اَلَمْ يَجِدْكَ يَتِيمًا فَـاوٰى

Kodi sadakupeze uli wamasiye ndipo adakupatsa pokhala pabwino?

Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adali wamasiye kuyambira pachiyambi (ku umwana wake). Popeza bambo ake adamwalira iye asadabadwe, mayi ake adamwalira iye ali ndi zaka zisanu ndichimodzi (6) kenaka agogo ake omwe ndi Abdul-Muttalibi anamutenga ndikumamulera kufikira pomwe Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adakwanitsa zaka zisanu ndi zitatu (8) ndipo amalume ake Abu Twaalib adatenga udindo omulera kufikira pomwe Mtumiki madalitso ndi mtendere zipite kwa iye adakwanitsa zaka pafupifupi makumi asanu (50).

Abu Twaalib adamuonetsera chikondi Mtumiki (sallallah alaih wasallam) kuposaso chikondi chomwe bambo angaonetse pa mwana wake. Izi zinkachitika kwa wina aliyense amene adamulerapo Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankumuonetsera chikondi chapamwamba kwambiri kuposa chimene Kholo kimaonetsa kwa mwana wake. Zonsezi zidali zochoka kwa Allah kuti wina aliyense amene angamuone ankamukonda kwambiri kuchokera pansi pa mtima.

وَوَجَدَكَ ضَآلًّا فَهَدٰى

Ndipo adakupeza uli wosazindikira (Quran) nakuongola (pokuzindikiritsa Quran)

Asadalandire utumiki Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sankazindikira zambiri zokhudza Dini, kotero Allah adamudalitsa pomupatsa utumiki, adamuphunzitsa china chirichonse chokhudza dini ndikumuonetsera njira yomwe angagwiritse ntchito kuwaongolera anthu ku dini ya Allah.

وَوَجَدَكَ عَآئِلًا فَاَغْنٰى

Ndipo adakupeza uli osauka kufikira adakulemeretsa

Mu Ayah imeneyi, Allah Ta’ala akumulankhula Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kumukumbutsa za mtendere umene adamupatsa poleredwa ngati mwana wamasiye opanda chuma kenaka Allah ndikumudalitsa ndi chuma.

فَاَمَّا الْيَتِيمَ فَلَا تَقْهَرْ

Basi, mwana wamasiye usamchitire nkhanza

Rasulullah (sallallah alaih wasallam) adakulanso ndi umoyo wamasiye, ndipo ankadziwa zopweteka, maganizo ndi Kukhudzidwa komwe mwana wamasiye amakhala nako mwana wamasiye ndi munthu amene nthawi zambiri amakhala amasowekera munthu amene angamuonetsere chikondi komanso chisoni. Kotero Allah walonjeza malipiro apamwamba kwa onse omwe akuyang’anira ana amasiye. Hadith ikutiphunzitsa kuti khomo lodala ndilomwe likusunga ana amasiye ndipo khomo loyipisitsa ndilomwe ana amasiye akuleredwa mwankhanza.

Kotero, mu Ayah imeneyi Allah akumuuza Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) komanso ummah wake kuti adziwalera ana amasiye mwaubwino komanso mwachikondi ndipo osawazunza.

وَاَمَّا السَّائِلَ فَلَا تَنْهَرْ

Ndiponso wopempha usamukalipire.

Mu Ayah imeneyi, Allah subhaanahu wataala akumuuza Mtumiki (sallallah alaih wasallam) kuti ngati munthu wabwera kwa iye kudzapempha chithandizo usamumane, mmawu ena titha kunena kuti ukuyenera kumuchitira chifundo ndikumuyang’anira, mukuchita izi anthu ako adzakutsatira ndipo athandize osauka ndi osowa..

وَاَمَّا بِنِعْمَةِ رَبِّكَ فَحَدِّثْ

Tsono mtendere wa mbuye wako uwutchule (pothokoza ndi kugwira ntchito zabwino)

Mu Ayah imeneyi Allah Tabaaraka wataala akumulankhula komanso kumulamula Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti adziyankhula zokhudzana ndi mtendere umene Allah adamudalitsa nawo, kotero kuchokera pa Aya imeneyi tikuphunzirapo kuti ndizoloredwa kumautchulatchula mtendere wa Allah kwa anthu umene adatidalitsa nawo posonyeza kumuyamika Allah, Mopanda kudzikweza kapena kudzitamandira kuti mtenderewo wadzipezera wekha, mmalo mwake tichitenge kuti ndimadalitso ochokera Allah.

Check Also

Tafseer ya Surah Ikhlaas

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ قُلْ هُوَ اللَّهُ أَحَدٌ ‎﴿١﴾‏ اللَّهُ الصَّمَدُ ‎﴿٢﴾‏ لَمْ يَلِدْ وَلَمْ يُولَدْ ‎﴿٣﴾‏ وَلَمْ يَكُن لَّهُ كُفُوًا …