Mbiri Za Muadhin

1. Munthu ochita adhana (muadhin) akuyenera akhale wamwamuna.[1]

عن ابن عمر رضي الله عنهما قال ليس على النساء أذان ولا إقامة (السنن الكبرى للبيهقي، الرقم: 1996)[2]

Zikunenedwa kuti Olemekezeka Ibn umar (radhiyallah anhuma) adati; “Kupanga azaana ndi iqaamah siudindo wa azimayi ayi”

2. Akhale wanzeru (ozindikira zomwe akuchita).[3]

3. Akhale otha nsinkhu oti amatha kumvetsa zinthu. Adhaan yamwana wamng’ono yemwe sadafike pansinkhu omvetsa zinthu adhanayo siimakhala yolondola ayi.[4]

4. Akuyenera kuti azitha kunena molondoloza mau a adhan.

5. Akhale ozindikira nthawi zaswalah.[5]

6. Akhale msilamu wolungama ndi woopa Mulungu.[6]

عن ابن عباس رضي الله عنهما قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم ليؤذن لكم خياركم وليؤمكم قراؤكم (سنن أبي داود، الرقم: 590)[7]

Olemekezeka Ibn Abbas (radhiyallah anhuma) akusimba kuti Mtumiki (sallallah alaihi wasallam) adati; ” Wabwino kwambiri (Olungama kwambiri) mwa inu akuyenera kuti asankhidwe kuti azipanga adhaan, komanso amene ali odziwa bwino kwambiri mwainu kuwerenga Quran (ophunzira bwino, odziwa kuwerenga quran komanso odziwa malamulo a swalah) akuyenera kutsogolera swalah zanu.”

zindikirani kuti malamulo atatu oyambilira atchulidwawa ndimalamulo opangitsa kuti adhanayo itheke. choncho ngati sapezekapo Malamulowo adhaana sidzakhala yolondora.


[1] فصل في صفة المؤذن وآدابه وشرطه أن يكون … ذكرا (روضة الطالبين 1/312)

[2] لهذا الحديث شاهد مرسل من حديث إبراهيم النخعي: حدثنا محمد بن الحسن الشيباني قال أخبرنا أبو حنيفة عن حماد عن إبراهيم قال ليس على النساء أذان ولا إقامة (كتاب الآثار، الرقم: 64)

[3] فصل في صفة المؤذن وآدابه وشرطه أن يكون … عاقلا (روضة الطالبين 1/312)

[4] (و) شرط من ذكر (التمييز) فلا يصحان من غير مميز لعدم أهليته للعبادة (مغني المحتاج 1/323)

[5] استحب كونه عالما بالمواقيت (مغني المحتاج 1/333)

[6] فصل في صفة المؤذن وآدابه … ويستحب … أن يكون عدلا وهو الثقة (روضة الطالبين 1/312-313)

[7] سكت الحافظ عن هذا الحديث في الفصل الثاني من هداية الرواة (2/4) فالحديث حسن عنده

Check Also

Mawu A Iqaamah Komanso Njira Ya Sunnat Yopangira Iqaamah

1. Mawu a Iqaamah ndichimodzimodzi ndi azaana. Koma popanga iqaamah mukuyenera kunena kamodzikamodzi kupatula mawu …