عن حسين بن علي رضي الله عنهما قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم من ذكرت عنده فخطىء الصلاة علي خطىء طريق الجنة (المعجم الكبير للطبراني، الرقم: 2887، وقال المناوي في فيض القدير (٦/232) تحت حديث من نسي الصلاة علي خطئ طريق الجنة: لكن انتصر له ابن الملقن فقال: حديث ضعيف لكنه تقوى بما رواه الطبراني عن الحسن بن علي مرفوعا: من ذكرت عنده فخطئ الصلاة علي خطئ طريق الجنة، وتبعه الحافظ ابن حجر فقال: خرجه ابن ماجه عن ابن عباس والبيهقي في الشعب عن أبي هريرة والطبراني عن الحسين بن علي قال: وهذه الطرق يشد بعضها بعضا)
Sayyiduna Husain bin Aliy (radhiyallahu anhuma) akufotokoza kuti Mthenga wa Allah madalitso ndi ntendere zipite kwa iye adati: munthu amene dzina langa latchulidwa pamaso pake ndiye osandifunira zabwino (osawerenga Durood) munthu ameneyo wasiya ntchito yabwino yokakulowetsa ku Jannah.
Kupambana kwa usiku kuposa usana
Mchitabu chotchedwa Nuzhatul-Majaalis muli ntsutso umene udalipo pakati pa usiku ndi usana wina aliyense kuyesetsa kudziikira kumbuyo kuti iye ndiopambana kuposa nzake. Usana udanena kufotokozera usiku kuti, “ndiine opambana kuposa iwe chifukwa swalah zitatu zimapempheredwa munthawi yanga pomwe mnthawi yako swalah ziwiri zokha ndi zomwe zimapempheredwa, ndiri ndi nthawi imene maduwa amayankhidwa pa tsiku la Jumuah (lachisanu) china chirichonse chomwe munthu angapemphe amapatsidwa. Swaum ya Ramadhan imamangidwanso munthawi yanga. Nthawi yako ndi yomangogona basi komanso ndi nthawi imene anthu amakhala kuti nzeru zawo sizikugwira ntchito chifukwa cha tulo, pomwe ine ndiri limodzi ndi kuchangamuka komanso ntchito zosiyanasiyana, ndipo mukuchangamuka muli madalitso ochuluka, chinanso ndikuti dzuwa limatuluka mnthawi yanga lomwe limawalitsa dziko lonse.”
Usiku udayankha ndi mawu okuti, ngati ukudzimenya pa mtima chifukwa cha dzuwa kuti limatuluka mu nthawi yako yamasana ine ndiye ndikuwaganizira anthu awo amene amadzukira usiku nthawi ya Tahajjud kupemphera komanso awo amene amalingalira za chilengedwe cha Allah kukhala apamwamba kuposa dzuwa, ungafikire bwanji ulemelero wa anthu amene ali pachikondi ndipo ali mu M’bindikiro kwaokhaokha, ungawafikire bwanji anthu amenewo pamene abindikira mwa ine? Ungazifanizire bwanji ndi usiku wa “Mi’raaj”? ndi yankho lanji lomwe ulinalo pa lamulo la Allah kwa Mtumiki wake (madalitso ndi mtendere zipite kwa iye) pamene ankamuuza kuti, ndipo mu ola la usiku dzuka upemphere ngati ibadah yako yoonjezera, Allah adalenga kaye ine asadalenge iweyo, ndiri ndi usiku wa chikonzero umene Allah amapereka madalitso osawerengeka, Allah amaitana pakati pa usiku kunena kuti, “kodi pali munthu yemwe akufuna kundipempha kuti ndimuyankhe” pali amene akufuna andipemphe chikhululuko ndipo ndimukhululukira? kodi siukudziwa kuti Allah adanena kuti, “oh iwe amene wadzikutila mu nsalu imilira ndipo uswali mkatikati mwa usiku pang’ono pokha! Kodi siudanve mawu a Allah onena kuti alemekezeke (Allah) yemwe adamuyendetsa kapolo wake mkatikati mwa usiku kuchoka ku Musjidul-Haraam upite ku Musjidul-Aqsa. (Nuzhatul Majaalis 90/2)