Tafseer Ya Surah Takaathur

اَلْهٰكُمُ التَّكَاثُرُ ‎﴿١﴾‏ حَتّٰى زُرْتُمُ الْمَقَابِرَ ‎﴿٢﴾‏ كَلَّا سَوْفَ تَعْلَمُوْنَ ‎﴿٣﴾‏ ثُمَّ كَلَّا سَوْفَ تَعْلَمُوْنَ ‎﴿٤﴾‏ كَلَّا لَوْ تَعْلَمُوْنَ عِلْمَ الْيَقِينِ ‎﴿٥﴾‏ لَتَرَوُنَّ ٱلْجَحِيمَ ‎﴿٦﴾‏ ثُمَّ لَتَرَوُنَّهَا عَيْنَ ٱلْيَقِينِ ‎﴿٧﴾‏ ثُمَّ لَتُسْـَٔلُنَّ يَوْمَئِذٍ عَنِ ٱلنَّعِيمِ ‎﴿٨﴾‏

Kwakutangwanitsani kusonkhanitsa (chuma chambiri ndi ana). Mpakana mwapita kumanda (mwamwalira ndikuikidwa m’manda). Sichincho, mudziwa posachedwapa.Ndiponso sichoncho, mudziwa posachedwapa.Sichonch, mukadakhala mukudziwa kudziwa kwachitsimikizo (siwenzi mukutangwanika ndi zamdziko).Ndithudi mudzauona moto. Kenako mudzauona ndithu ndi diso lachitsimikizo. Tsono patsikulo ndithudi mudzafunsidwa za mtendere (omwe mudapatsidwa).

اَلْهٰكُمُ التَّكَاثُرُ ‎﴿١﴾‏ حَتّٰى زُرْتُمُ الْمَقَابِرَ ‎﴿٢﴾‏

kupikisana posonkhanitsa chuma (komanso kufuna kupeza katundu ndizokoma zamdziko lapansi) zakutangwanitsani (ndikukuiwalitsani malamulo a Allah). Mpakana mwapita kumanda (mwamwalira ndikuikidwa m’manda).

Mpikisano osonkhanitsa chuma ndi zokoma zamdziko lapansi zawachotsa anthu ku cholinga chomwe adapezekera pano padziko lapansi, chifukwa chimene munthu adapezekera padziko lapansi lino ndikuti adzichita zinthu zokhanzo zomwe zingamusangalatse Allah komanso kukamulowetsa ku Jannah. Tsoka ilo chifukwa chokonda chuma komanso kulitengelera dziko lapansi kwapezeka kuti munthu watembenuka poyera ndikuiwala cholinga chenicheni chapano padziko ndipo akutangwanika popikisana zamapezedwe a zinthu zamdziko.

Mu aya imeneyi Allah Tabaaraka wata’ala akumudandaulira munthu – kuti akupitilizabe chikhalidwe chimenechi kufikira kumwalira, kufikira kuti akuikidwa m’manda.

Sayyiduna Abdullah bin Shikheer (radhiyallahu anhu) akulongosora kuti, nthawi inayake ndidamuyendera Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndipo nthawi imeneyo ankawerenga surah imeneyi. Atamaliza kuwerenga surah imeneyi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “mwana wa Adam (modzikweza) akumulankhula kuti chuma changa, chuma changa, komano palibe phindu lina lirilonse mu chuma chako kupatula chomwe wadya ndipo chatha, kapena chovala chomwe udavala kale ndipo chidaguga kapena chimene udachipeleka ngati sadaqah.”

Mu hadith yomwe ikupezeka Mchitabu cha Muslim, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adalankhulanso kuti chuma china chirichonse kupatula chomwe chatchuridwa m’mwambachi chidzatsala ndikugawidwa kwa anthu otsala iye atamwalira.

Ndichibadwi cha munthu wina aliyense kuti siumakhutitsidwa ndi zomwe ulinazo ndipo amakhala akupitiriza kusaka zina ndikuonjezera pamenepo. Potengera ndi kusakhutitsidwa kwa munthu pa zomwe alinazo ndikukhala ndi mtima ofuna kupeza zochuluka Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “ngati mwana wa Adamu atapatsidwa nkhokwe yodzadza ndi golide adzalakalaka kuti apezenso ina ndipo palibe chomwe chingadzadzitse mimba yake kupatula dothi la m’manda ndipo Allah adzalandira kulapa kwa munthu amene angapange chiganizo chofuna kubwelera kwa iye,”

كَلاَّ لَوْ تَعْلَمُونَ عِلْمَ الْيَقِينِ

Sichoncho! Mukadazindikira kuzindikira kwenikweni (sibwezi musakulabaladira za tsiku lomaliza).

Mu Ayah imeneyi, Allah akunena kuti, mukadadziwa kudziwa kwachitsimikizo (sibwezi musakulabadira za tsiku lomaliza).

Mukuyankhula kwina titha kunena kuti, ukadalingalira za imfa komanso kulingalira za mathero ako, pamene udzagonekedwe m’manda wekhawekha opanda nzako wina aliyense ndipo ulemelero onse umene udali nawo lero watheratu, siukanamaphwanya malamulo a Allah ndipo siukanamaliiwala tsiku lomaliza.

لَتَرَوُنَّ الْجَحِيمَ (٦) ثُمَّ لَتَرَوُنَّها عَيْنَ الْيَقِينِ

Ndithudi mudzauona moto wa Gahena Kenako ndithu mukauona motowo ndi diso lachitsimikizo.

Pali ma levulo awiri a chitsimikizo, levo yoyamba ndi imene kuli kuzindikira komwe munthu umakhala nako m’mutu, ndipo gawo lina la chitsimikizo ndiye kuzindikira kumene kumabwera pambuyo poti wadzionera wekha ndi maso ako.

Ndizachidziwikire kuti kuchiona china chake ndi maso ako zimaonjezera chikhulupiliro chomwe chidali chocheperako pachiyambi.

Mwachitsanzo, munthu akudziwa zoti kunja kuno kuli chilombo chotchedwa njoka komanso akudziwa kuopsya kwake komano sanaiwoneko, komano akangoti wakumana nayo maso ndi maso ndikuona kuopsya kwake zimaonjezera kuizindikira komwe adali nako pachiyambi.

Sayyiduna Musah (alaihis salaam) ankazindikira za ukulu wa Allah ndipo ankaidziwa njoka komanso nsato, komano ngakhale zidali chonchi, pamene Allah adamulamula kuti aponye ndodo yake pansi ndipo idasanduka njoka nthawi yomweyo adatembenuka ndikuyamba kuthawa, kotero, kukumana ndi chinthu ndikuchiona ndi maso ako ndizosiyanabe ndithu Kusiyana ndi kungochidziwa chabe.

ثُمَّ لَتُسْـَٔلُنَّ يَوْمَئِذٍ عَنِ ٱلنَّعِيمِ

Kenako ndithu mudzafunsidwa pa tsiku limenelo (lachiweruzo) za mtendere (omwe munali nawo padziko lapansi)

PA tsiku lachiweruzo, munthu wina aliyense adzafunsidwa za mtendere osiyanasiyana omwe adali nawo pano padziko lapansi, adzafunsidwa za momwe adagwiritsira ntchito umowo wake, chuma chake ndizina zotero. Mu Ayah ina yamu Quran Allah akufotokoza kuti :

اِنَّ ألسَّمْعَ وَالْبَصَرَ وَالْفُؤَادَ كُلُّ أُوْلَٰٓئِكَ كَانَ عَنْهُ مَسْـٔولًا

Makutu, maso ndi mtima (nzeru zako) , zonsezi zidzafunsidwa (pa tsiku la Qiyamah).

Kuchokera pa Ayah imeneyi taphunzirapo kuti pa tsiku lachiweruzo wina aliyense adzafunsidwa zokhudzana ndi mamvedwe ake, zakuyang’ana kwake kumvetsa kwake ndi zina zotero, wina aliyense adzafunsidwa m’mene adagwiritsira ntchito zinthu zimenezi, kodi adagwiritsira ntchito mnjira za Haraam kapena Halaal, chimodzimodzinso wina aliyense adzafunsidwa za cholinga chimene ankachitira ntchito zabwino komanso maganizo amene adali nawo pa nkhani yokhudza Allah komanso zolengedwa zake.

Mu hadith ina, Mtumiki Muhammad (sallallah alaih wasallam) adati, pa tsiku lachiweruzo munthu akadzabwera pabwalo la mahshar, sadzakwanitsa kusuntha pa malo omwe adzaime kufikira atayankha mafunso asanu, mafunso amenewa adzakhala okhudzana ndi mtendere umene ndi opatulika wa Allah omwe munthuyo adagwiritsa ntchito padziko lino lapansi.

1) Adachipeza bwanji chuma chake?

2 ) Adagwiritsa ntchito bwanji chuma chake?

3) Chinyamata chake adachigwiritsa ntchito bwanji?

4) Umoyo wake adagwiritsa ntchito bwanji?

5) Adagwiritsa ntchito motani maphunziro a Dini omwe adali nawo?

Nthawi zambiri anthu amaganiza kuti maphunziro omwe alinawo ndi chinthu chimene angagwiritse ntchito podzitenga kuti iye ndi wapamwamba, Komano tikufunika tizindikire kunena kuti kukhala ndi maphunziro a Dini ndi mphatso ya Namalenga pa ife, ndipo adzafunsidwa pa tsiku lachiweruzo.

Tsiku lachiweluzo munthu adzafunsidwa za momwe adagwiritsira ntchito maphunziro ake omwe adali nawo, kotero, ngati adaphunzira koma osatsatira zomwe waphunzirazo adzalandira chilango pa mlandu osatsatira zomwe adaphunzira.

Check Also

Tafseer ya Surah Ikhlaas

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ قُلْ هُوَ اللَّهُ أَحَدٌ ‎﴿١﴾‏ اللَّهُ الصَّمَدُ ‎﴿٢﴾‏ لَمْ يَلِدْ وَلَمْ يُولَدْ ‎﴿٣﴾‏ وَلَمْ يَكُن لَّهُ كُفُوًا …