- أَلَمْ نَشْرَحْ لَكَ صَدْرَكَ ﴿١﴾ وَوَضَعْنَا عَنكَ وِزْرَكَ ﴿٢﴾ الَّذِي أَنقَضَ ظَهْرَكَ ﴿٣﴾وَرَفَعْنَا لَكَ ذِكْرَكَ ﴿٤﴾ فَإِنَّ مَعَ الْعُسْرِ يُسْرًا ﴿٥﴾ إِنَّ مَعَ الْعُسْرِ يُسْرًا ﴿٦﴾ فَإِذَا فَرَغْتَ فَانصَبْ ﴿٧﴾ وَإِلَىٰ رَبِّكَ فَارْغَب.
Kodi sitidatsegule chidali chako (pokupatsa chikhulupiliro, chiongoko ndi nzeru zochuluka). Ndipo takuchotsera ntolo wako (pa tchito yolalikira pokuthandiza ndikukufwewetsera zinthu zako) omwe ukadathyola nsana wako. Ntolo umene udalemetsa nsana wako. Ndipo talifalitsa dzina lako pena paliponse. Ndipo ndithu pali chipsinjo palinso zabwino (zambiri).
Pamene wahi unkatsika kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) udali olemetsa kwambiri, ngati Mtumiki (sallallahu alaihi wasallam) adakhala pa ngamila, ngamila inkanjuta pansi osayenda chifukwa chakulemera kwa Wahi.
Polongosora za mphamvu ya wahi ndikulemekezeka kwake, Allah akufotokoza kuti; tikadati tiibvumbulutse Qur’an pa phiri, mukadaliona phiri likusweka chifukwa cha mantha kumuopa Allah. Komano Allah adatsegula chifukwa cha Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndicholinga choti wahi ukhale opepuka kwa iye.
Mu Ayah imeneyi Allah akunena kuti wachotsa chipsinjo pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) chomwe chikadamulemetsa ndikuthyola nsana wake. Chipsinjo chimene Allah akuchifotokoza apa ndikulemetsa kwa wahi komwe Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankakunva pa nthawi imene wahi unkabvumbulutsidwa.
Zikhozanso kutanthauzidwa kuti udindo umene Mtumiki (salallah alaih wasallam) adalinawo ofalitsa uthenga wa mu Qur’an komanso Dini kwatunthu. Pachipanda chithandizo cha Allah kuti sadatsegula chidali cha Mtumiki (sallallahu alaihi wasallam) ndikuzipanga kukhala zotheka komanso zopepuka sizikadakhala zophweka kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti agwire ntchito imeneyi.
وَرَفَعْنَا لَكَ ذِكْرَكَ
Ndipo tidalikweza dzina lako komanso ulemelero wako.
Kuchokera pa Ayah imeneyi tikuphunzirapo za chikondi chimene Allah alinacho pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) komanso ulemelero waukulu umene Allah adamudalitsa nawo Mtumiki (sallallahua alaih wasallam). Nthawi zonse pamene dzina la Allah latchuridwa, dzina la Mtumiki (sallallahu alaih wasallama) limabwera patsogolo pake.
Ukamawelenga kalimah komanso kulowa chisilamu, dzina la Mtumiki (sallallahua alaih wasallam) limatchuridwa limodzi ndi la Allah. Mu Adhaan, Iqaamah komanso Khutbah dzina la Mtumiki (sallallahua alaih wasallam) limabwera ndipo limatchuridwa limodzi ndi la Allah, Mkatikati mwa swalah popanga Tashahhud dzina la Allah limabweranso limodzi ndi la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndipo ngati dzina la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) silidatchuridwe ndipo Durood siidawerengedwe ndiye kuti swalah imeneyo ndiyopelewera, Mu Quran yolemekezeka malo ambiri Allah akumulemekeza Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), Mmenemu ndimmene Allah wamulemekezera Mtumiki (sallallah alaih wasallam).
فَإِنَّ مَعَ الْعُسْرِ يُسْرًا ﴿٥﴾ إِنَّ مَعَ الْعُسْرِ يُسْرًا
Kotero ndithudi pomwe pali mavuto Palinso zabwino, ndithudi pali mavuto pali zabwino.
Allah Tabaaraka wataala adalenga dziko la pansi lino ngati malo amayesero, kotero munthu wina aliyense adzakumana ndi mayesero osiyanasiyana pamoyo wake.
Nthawi zina Allah adzamuyesa munthu kudzera mu thanzi lake, ndipo pena adzayesedwa ndi chuma chake ndipo nthawi zina adzayesedwa kudzera mwa ana ake, ndipo nthawi zina adzayesedwa kudzera mu zinthu zimene alinazo ndizina, posatengera udindo umene munthu alinawo adzayenera kukumana ndi mayesero, kaya ndi kuthupi lake, kaya ndi mmaganizo ndizina. Komano ngakhale ziri choncho, mu Ayah imeneyi Allah akutidziwitsa kuti pali mavuto pali ntendere.
Choncho, ngati nsilamu angaigwritsitse dini ya Allah ndikukhala ndi chitsimikizo mmalonjezo omwe Allah pamodzi ndi Mtumiki wake adalonjeza, zivute zitani adzapeza ntendere pambuyo pa mavuto.
فَإِذَا فَرَغْتَ فَانصَبْ ﴿٧﴾ وَإِلَىٰ رَبِّكَ فَارْغَب
kotero pamene watsiriza zonse zomwe ukumachitira anthu limbikira kupemphera ndipo khala olakalaka za zabwino zomwe ziri kwa mbuye wako.
Mu Aya imeneyi Mtumiki wa Allah (mtendere ndi madaritso za Allah zipite kwa iye) akuuzidwa ndi Allah kuti akamaliza ntchito yowalalikira anthu mmagawo osiyanasiyana a Dini komanso kuwaongolera ku njiira yoongoka akuyenera kutembenukirano kwa Allah ndi maganizo ake onse ndikudzitangwanitsa pochita ibadah yosiyanasiyana.
Ma shehe alongosora kuti onse amene akugwira ntchito zosiyanasiyana za Dini, monga ziliri kuti nkofunika kuwalalikira komanso kuwaphunzitsa anthu Dini, kuwaunikira komanso kuwasonyeza ntchito zabwino zomwe angapezere sawabu, chimodzinso iwo eni ake kuti adzitangwanitse kuchita ibadah ya eni ake,kudziyang’ana ndikudzikonza monse mmene muli mofooka zomwe zingaikire umboni za ubale wawo ndi Allah.
Iyi ndiye pulani yokwanira yomwe munthu angakhale nayo, nthawi zonse kuonesetsa kuti pali kusintha pamoyo wake ndipo nthawi yomweyo akufunikanso kuonetsetsa kuti ummanso ukupita patsogolo pa nkhani ya Dini, osangolongosora mbali imodzi yokha. chidandaulo chonse chisamathere powaongolera anthu ena kudziiwala iwe mwini, kudzidandaulira wekha koma ena osawalabadira , kotero, Ayah imeneyi ikutiphunzitsa kuti fikir kapena kuti chidandaulo chathu pa Dini chikufunika chidzikhala chambali zonse.