عن أبي هريرة قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم من صلى علي مرة واحدة كتب الله عز وجل له بها عشر حسنات (مسند أحمد، الرقم: 7561، ورجاله رجال الصحيح غير ربعي بن إبراهيم وهو ثقة مأمون كما في مجمع الزوائد، الرقم: 17282)
Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, munthu amene angandifunire zabwino (pondiwerengera Durood) kamodzi Allah adzamulembera zabwino (m’bukhu la zintchito zake) zokwana khumi (10).
Kutetezeka ku mavuto obwera nthawi yomwalira kudzera mukuchulukitsa kuwerenga Durood
Mchitabu chotchedwa Nuzhatul Majaalis mukupezeka nkhani iyi:
Munthu wina adapita kukazonda nzake wina yemwe adadwazika kwambiri ndipo pamenepo ndikuti atatsala pang’ono kumwalira, winayu adafunsa odwalayu kuti, ukunva bwanji ululu pa nthawi ino pamene watsala pang’ono kumwalira? Iye adayankha nati, sindikunva ululu wina ulionse, ndidanva ma shaikh akunena kuti, “munthu amene angawerenge durood kumuwerengera Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kwambiri adzatetezeka ku mavuto odza pomwalira akamadzamwalira.”