عن علي بن أبي طالب رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال : من صلى علي صلاة كتب الله له قيراطا والقيراط مثل أحد (مصنف عبد الرزاق، الرقم: 153، وسنده ضعيف كما في القول البديع صـ 260)
Sayyiduna Aliy bin Abi Taalib radhiyallahu anhu akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam adati; munthu angandifunire zabwino kamodzi Allah adzamulembera sawabu zokwana Qeeraat imodzi m’bukhu lake la ntchito zabwino ndipo Qeeraat imadzi ikufanana ndi phiri la Uhdi.
Nkhani Ya Ebrahim bin khawaas (rahimahullah)
Zanenedwa mchitabu chotchedwa “Nuzhatul Basaateen” kuti sayyiduna Ebraahim bin khawaas (rahimahullah)adayankhula kuti: tsiku lina lake ndiri mnjira , ndidali ndi ludzu kwambiri moti mpakana ndidakomoka. ndiri chikomokere choncho ndidanva ngati wina wake akunndiwaza madzi kumaso , nditatsitsimuka ndidamuona mnyamata okongora kwambiri ali pa hashi pafupi ndi ine, adandipatsa kumwa ndipo adandipempha kuti ndikhale naye limopdzi titangoyenda ntunda ochepa adafunsa kuti “ukuona chani ?” ndidamuyankha kuti “uwu ndi nzinda wa Madina Tayyibah”kenaka andiuza kuti, ukhonzano kutsika pano,. pita ku manda a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ukandipelekerenso salaam. ukamuuze kuti m’bale wake Khidar akupeleka salaam. (Fazaail-e-Durood, Pg, 162)