بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمٰنِ الرَّحِيْمِ
الْقَارِعَةُ ﴿١﴾ مَا الْقَارِعَةُ ﴿٢﴾ وَمَآ اَدْرٰىكَ مَا الْقَارِعَةُ ﴿٣﴾ يَوْمَ يَكُونُ النَّاسُ كَالْفَرَاشِ الْمَبْثُوثِ ﴿٤﴾ وَتَكُونُ الْجِبَالُ كَالْعِهْنِ الْمَنفُوشِ ﴿٥﴾ فَاَمَّا مَن ثَقُلَتْ مَوَازِيْنُهُۥ ﴿٦﴾ فَهُوَ فِى عِيشَةٍ رَّاضِيَةٍ ﴿٧﴾ وَاَمَّا مَنْ خَفَّتْ مَوَازِينُهُۥ ﴿٨﴾ فَاُمُّهُۥ هَاوِيَةٌ ﴿٩﴾ وَمَآ اَدْرٰىكَ مَا هِيَهْ ﴿١٠﴾ نَارٌ حَامِيَةٌ ﴿١١﴾
Kugunda kwaphokoso (la qiyaamah). Kodi kugunda kwaphokoso ndichiyani?. Ndichiyani chingakudziwise zakugunda kwaphokoso?. (Kugunda kwaphokoso kudzachitika)Tsiku limene anthu adzakhala ngati agulugufe obalalika. Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya omwazidwa. Tsono munthu amene muyeso wazinthu zabwino udzalemere(ndikupepuka zoipa). Ndiye kuti adzakhala osangalala pa tsiku lachiwerudzo. Ndipo amene muyeso wake wazabwino udzapepuke(ndikulemera zoipa). Ndiye kuti kumalo ake ofikila kudzakhala ku Hawiya(dzenje lamoto wa jahannama). Chingakudziwitse mchiyani zamoto wa Hawiya. Umenewo ndimoto oyaka mwaukali.
يَوْمَ يَكُونُ النَّاسُ كَالْفَرَاشِ الْمَبْثُوثِ ﴿٤﴾
Tsiku limene anthu adzakhale ngati agulugufe obalalikana/omwazikana.
(Kugunda kwaphokoso kudzachitika) mu tsiku limene anthu adzakhale ngati agulugufe omwazikana. Mu surah imeneyi Allah Taala akufotokoza zakusungulumwa koopsa kumene kudzachitike pa tsiku la Qiyamah. Patsiku limeneli anthu azidzathamanga kupita uku ndi uku ali ndi nkhawa komanso osungulumwa kamba koopa kuwerengetseredwa zintchito zawo, Allah Ta’ala akulongosola mu Quran mmene zidzakhalire pa tsikulo nati: Tsiku limenelo munthu adzathawa mbale wake weniweni, Adzathawa mayi ake ndi bambo ake, komanso adzathawa Mkazi wake ndi ana ake. aliyense patsiku limenelo adzakhala ozidandaulira yekha. (Surah Abas: 34-37)
Mndime imeneyi Allah Ta’ala akufotokoza mmene anthu adzakhalire osungulumwa ndiozipatula pakati pawo patsiku lachiweruzo, Komanso mmene anthu azidzathawirana pakati pawo . Allah Ta‘ala akuti, Patsikuli anthu adzakhala ngati agulugufe omwazikana. Kusonyeza kuti anthu adzakhala obalalikana ndi omwazikana kwa wina ndi mnzake kamba koti sadzatha kuthandizana komanso adzakhala odandaula, ngati monga mmene amachitira agulugufe.
وَتَكُونُ الْجِبَالُ كَالْعِهْنِ الْمَنفُوشِ ﴿٥﴾
Ndipo mapiri adzakhala ngati Ubweya wanyama omwazika.
Pakadali pano, mapiri padziko pano aima molimba ndipo palibe chilichonse chingakwanitse kuwasuntha mapiriwo. Komano patsiku limenelo, Pamene mapiri adzanyenyedwenyenyedwe,ndipo adzauluzika nabalalikana, ndipo adzakhala akuuluzika ngati ubweya othothoredwa kunyama.
فَاَمَّا مَن ثَقُلَتْ مَوَازِيْنُهُۥ ﴿٦﴾ فَهُوَ فِى عِيشَةٍ رَّاضِيَةٍ ﴿٧﴾
Tsono munthu amene muyeso wantchito zabwino udzalemere (ndikupepuka zoipa)ndiye kuti ameneyo adzakhala osangalala patsikuli.
Patsiku la qiyama ntchito zabwino ndizoyipa zidzayesedwa mmasikelo. Kuchokera mmavesi ochuluka ndi mahadith tikumvetsedwa kuti kuyesedwa kwantchito kudzachitika maulendo awiri patsikuli.
Kuyesa koyamba kudzakhala koyesa Imaan ya anthu amene anali ndi Imani. Mukuyesa kumeneku kudzasiyanitsa pakati pa anthu okhulupilira ndi makafiri.
kuyesa kwachiwiri kudzakhala kusiyanitsa pakati pantchito zabwino ndizoyipa za asilamu okha.
Musurah imeneyi, kuyeza komwe kwatchuridwaku zachidziwikire kukuimilira kuyesa koyamba, kuyesa kumene kwamsilamu aliyense sikelo yake idzakhale yolemera, Posatengera zazintchito zina, Pamene sikelo yamakafiri idzakhala yopepuka.
Kuchokera mmahadith, pali zina mwa ntchito zabwino zomwe zatchuridwa zimene zidzapangitse kuti sikelo ya ntchito zabwino idzakhale yolemera kwambiri patsiku laqiyamah.
Zina mwa ntchitozi zilipo zisanu ndipo ndi izi:
1) Kugwira ntchito iliyonse ndi niyyat yabwino(ndichisimikizo choyeresa mtima) Ngati ungagwire ntchitoyo moyeretsa mtima (ikhlaswi) kumapangitsa ntchitoyo kukhala yabwino ndiyapamwamba. Mmene tingayeretsere maniyyat athu pantchito zathu ndimmenenso ntchito zathu zidzalemelere kwambiri pasikelo zantchito zathu ndiponso tidzapeza malipiro ochuluka patsiku laqiyamah.
2 Kugwira ntchito potsatira masunnah. Kukongora ndiubwino wantchito ndizimene zingapangitse kubweretsa kulemera pasikelo yantchito zabwino ndiponso idzapangitsa kupeza malipiro apamwamba. Sintchito zochuluka zimene zingapangitse kuti sikelo yanu idzalemere ayi. Ngati ntchitoyo ikuchitika potsatira mchitidwe wa Mtumiki (sallallah alayhi wasallama) (masuna) ndiye kuti umapeza kukongora kwantchitoyo komanso ubwino wake.
3) Kukhala chete osamayankhula zopanda pake. Mchitidwe okhala chetewu pamaso pa Allah Taala umawerengeredwa pakati pantchito zabwino zimene zikapangitse kuti sikelo ikalemere passiku lachiweruzo.
4) Kukhala ndimakharidwe abwino. kuwachitira anthu ulemu ndikumawawonetsera makharidwe abwino pakati pawo ndichinthu chimodzi chimene ndi chofunikira kwambiri komanso chidzalemeretsa sikelo yantchito zabwino patsiku la Qiyamah.
5) Kuwerenga mawu awa “Laa ilaaha illallah”. mukusimbidwa muhadith kuti kuwerengawerenga mawu amenewa kudzapangitsa kuti sikelo idzalemere kwambiri patsiku laqiyamah, komano ngati mungawanene mawu amenewa moyeretsa mtima.
Zimenezi ndi ntchito zapamwamba kwambiri zimene wina aliyense Okhulupilira akuyenera kuzichita, chifukwa zidzabweretsa zabwino mukaundula wathu wantchito zabwino ndiponso zidzapangitsa kuti masikelo athu adzalemere ndi ntchito zabwino patsiku la qiyamah.
Chimodzimodzinso munthu okhulupilira akuyenera kudzitalikila ntchito zimene zingapangitse kuti ntchito zathu zabwino zidzapepuke pasikelo patsiku la Qiyamah.
Chimodzimodzinso munthu okhulupilira akuyenera kudzitalikila ntchito zimene zingapangitse kuti ntchito zathu zabwino zidzapepuke pasikelo patsiku la Qiyamah. Hadith ikulongosora kuti pali ntchito zambiri zoipa zomwe zingapangitse ntchito zathu zabwino kukhala zopanda pake. Zina mwa ntchitozo nazi:
1. Kuwazunza anthu kapenanso kuwapondereza mwanjira iliyonse. Hadith ikulongosola kuti munthu adzabwera patsiku lachiweruzo ali ndimapili antchito zabwino. Choncho adzapezeka kuti adatukwana munthu wina, anawanamizira anthu ena ndikunyoza ena ndiponso anaononga chuma cha ena.Chifukwa chantchito zoipa zimene adachita, Ntchito zake zabwino zidzaperekedwa kwa omwe adawalakwirawo.
2. Kugwira ntchito opanda kuyeretsa mtima, Pozionetsera kwa anthu ndi mwamatama. Zikuyankhuridwa muhadith kuti patsiku laqiyamah anthu atatu oyambilira omwe adzakalowe kumoto wagehena ndimunthu osoma amene wakhala akufalitsa Dini umoyo wake onse, wina ndimunthu wachuma amene wakhala akupereka swadaqa mowirikiza pothandiza osauka Komanso munthu amene wakhala umoyo wake akumenya Jihadi. Anthu onsewa adzaponyedwa mmoto wagehena mowatsogoza mitu yawo kamba koti sadagwire ntchito zawo moyeretsa mitima yawo koma adagwira pofuna kuzionetsera kwa anthu.
Hadith ina ikufotokoza kuti munthu amene angapemphere swalah kapena kusala kudya ndicholinga chozionetsera kwa anthu ndiye kuti wamuphatikiza Allah ndizolengedwa zake (shirk) pantchito zomwe wachitazo ndipo munthu ameneyo sadzalandira malipiro antchito zake zabwino zomwe adachita.
Muhadith ina Mtumiki (sallallah alayhi wasallama) walongosola kuti munthu wina aliyense amene angachite ntchito yabwino ndicholinga choti anthu amuone, patsiku la Qiyaamah, Allah Ta‘ala adzayankhula kwa iye nati:, “Ndilibe ophatikizana naye ,choncho iwe unandiikira ophatikizana nawo pamene unkachita ntchito zabwino choncho siulandira malipiro antchito zabwinozo kwa Ine. Pita ukalandire malipiro ako kwa amene udawagwilira ntchito kuti akuwonewo”
3. Kumwa zoledzeretsa komanso kudya zinthu za Haraam. Zanenedwa muhadith kuti munthu amene amadya zinthu zaharaam kapena kumwa zolezeresat duwa yake komanso maibaada ake samalandilidwa kwa Allah. Choncho patsiku la Qiyaamah, munthu otere sadzalandira ntchito zake zabwino zomwe adachita pokhapokha atalapa machimo ake nayamba kuchita zolungama pamoyo wake.
4. Kusapemphera Salaah. Kusiya kupemphera swalah ndichiyambi chopangitsa ntchito zabwino zonse kuti zionongeke. Choncho, patsiku laqiyamah chifukwa chosapemphera swalah munthu sadzapeza malipiro ochulukawa zomwe zidzayesedwe pasikelo zomwe akuziyembekezera kuti ndintchito zabwino.
5. Kusapereka zakat. Zalongoseredwa muhadith kuti munthu amene samapereka zakat, Kamba kagawo lamachimo amene amawapeza posapereka zakat iyeyo adzamanidwa malipiro aswala imene amapemphera. Mu kuyankhula kwina titha kunena ngakhale adzakhale mgulu la anthu oswali sadzalandira malipiro a swalayo.
Choncho, Nthawi zonse munthu aliyense akuyenera kukhala osamala ndiokhuzidwa pantchito zomwe akugwira. Chabwino chilichonse kapena choipa, posatengera kuti ndichochepa bwanji osachitenga ngati kuti chopanda pake. Ndizotheka kuti ntchito imene timayitenga ngati ndiyochepa ngati mungaichite moyeretsa mtima (ikhlaswi )possatira njira ya sunnah ndizotheka kudzapangitsa sikelo yake yazabwino kukhala yolemera, komanso ndikukhala chifukwa chobweretsa chipulumutso chake, chikhululuko ndikukalowetsedwanso ku Jannah.