عن فاطمة رضي الله عنها قالت: كان رسول الله صلى الله عليه وسلم إذا دخل المسجد صلى على محمد وسلم وقال رب اغفر لي ذنوبي وافتح لي أبواب رحمتك وإذا خرج صلى على محمد وسلم وقال رب اغفر لي ذنوبي وافتح لي أبواب فضلك (سنن الترمذي، الرقم: 314، وحسنه)
Olemekezeka mama Faatimah (radhiyallahu anha) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) akamalowa munzikiti choyambilira ankawerenga Durood ndipo kenako amawerenga dua yotsatirayi:
رَبِّ اغْفِرْ لِيْ ذُنُوْبِيْ وَافْتَحْ لِيْ أَبْوَابَ رَحْمَتِك
Rabbigh firlii dhunuubii waftahlii Abuwaaba rahmatika.
Oh Allah, ndikhululukireni machimo anga ndiponso munditsegulire makomo a chifundo chanu.
Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) akamatuluka munzikiti ankawerenga Durood ndipo kenako ankawerenga duwa yotsattirayi:
رَبِّ اغْفِرْ لِيْ ذُنُوْبِيْ وَافْتَحْ لِيْ أَبْوَابَ فَضْلِك
Rabbigh firlii dhunuubii waftahlii Abuwaaba fadhwilika
Oh Allah ndikhululukireni machimo anga ndikunditsegulira makomo a ulemelero wanu.
Olemekezeka Waail radhiyallahu anhu ameta tsitsi lake
Waail (radhiyallahu anhu) akusimba kuti :
Tsiku lina ndidapita kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kukamuyendera pamenepo ndikuti tsiku langa litatalika kwambiri, ndiri chikhalire ndi iye adayankhula mawu oti, “Zubaab,Zubaab” (omwe akutanthauza kuti China chake choipa) ndinaganiza kuti akunena tsitsi langa, ndidabwelera kunyumba ndikumeta tsitsi langa mwachangu.
Tsiku lotsatira nditakamuonanso adati, sindimatanthauza tsitsi lako poyankhula mawu amene aja dzulo, komano wachita bwino kumeta tsitsi lako. (Saheeh Bukhari, #2731)
Zomwe adachita sahabi ameneyu pamenepa zikungowonetseratu chikondi chenicheni chomwe adalinacho mu mtima mwake pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Sadatenge nthawi poganiza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sadasangalatsidwe ndi tsitsi lake lalitali, mwachanguchangu adameta tsitsi lake. Wina atha kungoona kuti ichi ndi chikondi chimene maswahabah adali nacho, kungoganizira chabe kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) wakhumudwa zinkawasowetsa mtendere, kodi pali kuthekera koti akadatha kuphwanya lamulo la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kapena kutsutsana ndi Sunnah yake?