Kuwerenga Durood ukadzukira Tahajjud

عن عبد الله بن مسعود قال يضحك الله إلى رجلين رجل لقي العدو وهو على فرس من أمثل خيل أصحابه فانهزموا وثبت فإن قتل استشهد وان بقي فذلك الذي يضحك الله إليه ورجل قام في جوف الليل لا يعلم به أحد فتوضأ فأسبغ الوضوء ثم حمد الله ومجده وصلى على النبي صلى الله عليه وسلم واستفتح القرآن فذلك الذي يضحك الله إليه يقول انظروا إلى عبدى قائما لا يراه أحد غيري (عمل اليوم والليلة، الرقم: 867، وسنده صحيح كما في القول البديع صـ 376)

Olemekezeka Abdullah bin Masood (radhiyallahu anhu) adati, Allah amasangalatsidwa ndi anthu awiri, munthu oyamba ndi amene wakumana ndi mdani yemwe ali pa Hashi yake yabwino kwambiri limodzi ndi anzake. Ndikupezeka kuti anzake onse agonja koma iye ndikupitiriza kumenya nkhondo, ngati angamwalire ndiye kuti wamwalira ali Shahid, ngati sangaphedwe ndiye kuti ali mgulu la anthu amene Allah wasangalatsidwa nawo. Munthu wina ndi amene amadzuka usiku kuswali Tahajjud mopanda wina aliyense kuzindikira kuti iyeyu wadzukira Tahajjud, amapanga wudhu wake moyenera ndipo akatero amamutamanda Allah ndikumuyeretsa, komanso amamfunira zabwino Mtumiki (swallallahu alaih wasallam). Ndipo akatero amayamba kuwerenga Quran. Uyu ndiye munthu amene Allah amasangalatsidwa naye, Allah akuyankhula zokhudza munthu amene “Tamuonani kapolo wanga amene akuswali pamene wina aliyense sakumuona kupatula ine”.

Chikondi chopanda malire cha maswahabah pa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam)

Munthu wina adabwera kwa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) nati, Oh Mtumiki wa Allah (swallallahu alaih wasallam) chikondi changa pa inu chili ponena kuti ndikangokuganizani ndimazadzidwa ndi chikondi chopanda malire, ndipo mtima wanga siumakhala mmalo pokhapokha ndikuoneni, Oh Mthenga wa Allah, maganizo amandifika kuti ngati Allah anganditenge ndikukandilowetsa ku Jannah zidzakhala zovuta kwa ine kuti ndidzakuoneni popeza inu mudzakhala Jannah ya pamwamba kwambiri yomwe ine sindingakwanitse kuifika.

Mtumiki swallallahu alaih wasallam adamukhazikitsa mtima pansi pomuwerengera Ayah iyi:

 

وَمَن يُطِعِ ٱللَّهَ وَٱلرَّسُولَ فَأُو۟لَٰٓئِكَ مَعَ ٱلَّذِينَ أَنْعَمَ ٱللَّهُ عَلَيْهِم مِّنَ ٱلنَّبِيِّـۧنَ وَٱلصِّدِّيقِينَ وَٱلشُّهَدَآءِ وَٱلصَّٰلِحِينَ ۚ وَحَسُنَ أُو۟لَٰٓئِكَ رَفِيقًا ‎﴿٦٩﴾‏

Onse amene amatsatira malamulo a Allah ndikutsatira sunnah ya Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) ali limodzi ndi anthu omwe ali mchisomo cha Allah monga Atumiki, ma Siddiiqiin, anthu ofera ku nkhondo komanso anthu olungama. (mujamul kabeer lit tabraani, #12559)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …