Kuwerenga Durood mkatikati mwa swalah ndi kunja kwa swalah

عن أبي أمامة عن النبي صلى الله عليه وسلم قال: من دعا بهؤلاء الدعوات في دبر كل صلاة مكتوبة حلت له الشفاعة مني يوم القيامة اللهم أعط محمدا الوسيلة واجعله في المصطفين محبته، وفي العالين درجته وفي المقربين داره (المعجم الكبير للطبراني، الرقم: 7926، وفيه مطرح بن يزيد وهو ضعيف كما في مجمع الزوائد، الرقم: 16981، وقد تحرفت كلمة العالين إلى العالمين في المعجم الكبير ومجمع الزوائد كما نبه عليه الشيخ محمد عوامة في حاشيته على القول البديع صـ 363)

Hazrat Abu Umaamah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, wina aliyense amene angawerenge mawu awa pambuyo pa swalah ya Fardh chiombolo changa pa iye chhidzakakamizidwa pa tsiku lachiweruzo.

اَللّٰهُمَّ أَعْطِ مُحَمَّدًا الْوَسِيْلَةَ وَاجْعَلْهُ فِيْ الْمُصْطَفَيْنَ مَحَبَّتَهُ وَفِيْ الْعَالِيْنَ دَرَجَتَهُ وَفِيْ الْمُقَرَّبِيْنَ دَارَهُ

Allahummah A’twii Muhammadanil wasiilata waj’alhu fii Mustafiina mahabbatahu, wafil Aalamiina darajatahu wafil muqarrabiina daarahu.

Oh Allah mupatseni Muhammad (sallallah alaih wasallam) wasiilah (mwayi owombola pa tsiku lachiweruzo) ikaninso chikondi m’mitima mwa anthu omwe mudawasankha mumuikenso mgulu la anthu apamwamba ndipo malo ake muwapange kukhala limodzi ndi akapolo omwe ndi okondedwa kwambiri kwa inu.

Nsembe ya maswahabah radhiyallahu anhum pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)

Nyumba ya Bibi Faatimah (radhiyallahu anha) idali potalikirako ndi nyumba ya Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Tsiku lina Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamuuza kuti “khumbo langa ndiloti udzikhala nane pafupi” Bibi Faatimah (radhiyallahu anha) adayankha nati, Nyumba ya Haarithah ili pafupi ndi yanu, ngati mungamupemphe kuti tisinthanitse ndi yanga adzavomera mwansangala. Tidasinthanapo kale m’mbuyomu ndiye ndikuchita manyazi kuti ndimupemphenso”.

Ngakhale zidali choncho olemekezeka Haarithah (radhiyallahu anhu) adazadziwabe kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) amafuna Faatimah atamakhala naye pafupi. Ulendo wina anabwera kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndikumuuza kuti: Oh Mthenga wa Allah, ndamvetsedwa kuti mukukhumba mutamakhala moyandikana ndi Faatimah, nyumba zanga ndi zimenezi, palibe nyumba ina yomwe ili pafupi ndi inu kupatula nyumba zangazi, titha kusinthana ndi Faatimah nyumba iliyonse m’nyumbazi, Oh Mthenga wa Allah, chomwe mungapemphe ndikutenga kuchokera kwa ine ndichomwe chingakhale chokondeka kwa ine kuposa chomwe mungandisiile,”

Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamvomera ndikumuuza kuti,” ndikudziwa kuti zomwe ukuyankhula zikuchokera pansi pa mtima”. Ndipo Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamangira Dua. (Tabaqaat kubra 19/8)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …