عن أوس بن أوس رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم إن من أفضل أيامكم يوم الجمعة فأكثروا علي من الصلاة فيه فإن صلاتكم معروضة علي قال: فقالوا: يا رسول الله: وكيف تعرض صلاتنا عليك، وقد أرمت قال: يقولون بليت قال: إن الله تبارك وتعالى حرم على الأرض أجساد الأنبياء صلى الله عليهم (سنن أبي داود، الرقم: 1531، وإسناده صحيح كما في خلاصة الأحكام للنووي 1/441)
Aws bin Aws (radhwiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adati tsiku labwino kwabwino kwambiri ndi tsiku la Jumuah (lachisanu) kotero Chulukitsani kundiwerengera duruud tsiku limeneli chifukwa duruud yanu imandifika, swahabah wina adafunsa nati Oh Mthenga wa Allah Duruud yathu idzakufikani bwanji mukadzamwalira ndipo mafupa anu adzakhala awola? Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adayankha nati, “ndithudi Allah Tabaaraka wata’ala adailetsa nthaka kudya matupi a aneneri alaihim salaam .”
Chikondi chochokera pansi pa mtima komanso chikumbutso cha Umar (radhwiyallahu anhu pa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam)
Usiku wina olemekezeka Umar (radhwiyallahu anhu) ali mkati moyendayenda kupereka chitetezo adaona moto ku nyumba inayake komanso adamva mawu. Atapita komweko adapeza mayi wachikulire akuluka ndikumalakatula ndakatulo iyi:
Allah alandire mapemphero a anthu omwe ali olungama komanso Okhala ndi udindo wapamwamba kupempha madalitso pa Mtumiki Muhammad (swallallahu alaih wasallam).
Oh Mthenga wa Allah unkachita ibaadah usiku onse ndipo unkatulutsa misonzi kulira usiku onse
Ndikufuna ndidziwe ngati nkotheka kudzakhala limodzi ndi okondedwa wanga Mtumiki Muhammad (swallallahu alaih wasallam) popeza imfa imabwera mosiyanasiyana ndipo sindikudziwa kuti ndidzamwalira motani.”
Atamva mawu amenewa, Umar (radhiyallahu anhu) adakhala pansi kulira ndikumkumbukira Mtumiki (swallallahu alaih wasallam). (kitaabuz Zuhd War Raqaaiq, 1024)