Chikondi chakuya  komanso chikumbutso cha Umar (radhwiyallahu anhu pa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam)

Usiku wina olemekezeka Umar (radhwiyallahu anhu) mu ulamuliro wake ali mkati moyendayenda kupereka chitetezo adaona kuwala kuchokera nyumba inayake komanso adamva mawu. Atapita komweko adapeza mayi wachikulire akuluka uku akulakatula ndakatulo iyi,

عَلَى مُحَمَّدٍ صَلَاةُ الْأَبْرَارْ ** صَلَّى عَلَيْكَ الْمُصْطَفَوْنَ الْأَخْيَارْ

Ndikuppha anthu onse olungama kuti apitirize kumfunira zabwino Mtumiki Muhammad (swallallahu alaih wasallam), ndikupempha kuti akapolo osankhika a Allah omwe kuti akuwerengereni  Duruud inu oh Mthenga wa Allah!

قَدْ كُنْتَ قَوَّامًا بَكِيَّ الْأَسْحَارْ

Oh Mthenga wa Allah unkachita ibaadah usiku onse ndipo unkatulutsa misonzi kulira usiku onse.

يَا لَيْتَ شِعْرِي وَالْمَنَايَا أَطْوَارْ ** هَلْ تَجْمَعُنِي وَحَبِيبِي الدَّار

Ndikadakhala ndikudziwa kuti ndidzakhala limodzi ndi okondeka wanga umoyo umene uli nkudzawo, sinankha imfa imampeza munthu mnyengo zosiyansiyana, ndikakhala ine ndiye sindikudziwa ndidzachoka bwanji pano padziko.

Atamva mawu amenewa, Umar (radhiyallahu anhu) adakhala pansi kulira ndikumkumbukira Mtumiki (swallallahu alaih wasallam).

Check Also

Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) aluza mano ake pa nkhondo ya Uhud

Pankhondo ya Uhud, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamenyedwa koopsa ndi adani ndipo mano awiri …