بسمِ اللَّهِ ألرَّحْمٰنِ الرَّحِيمِ
وَالْعَصْرِ ﴿١﴾ اِنَّ الْاِنسَانَ لَفِى خُسْرٍ ﴿٢﴾ إِلَّا الَّذِينَ اٰمَنُوْا وَعَمِلُوْا الصّٰلِحٰتِ وَتَوَاصَوْا بالْحَقِّ وَتَوَاصَوْا بالصَّبْرِ ﴿٣﴾
Ndikulumbilira nthawi; ndithudi munthu ndioluza, kupatula amene akhulupilira namagwira ntchito zabwino ndipo amalimbikitsana wina ndimnzake kutsatira choonadi komanso namalimbikitsana kupilira (komanso kupewa uchimo)
وَالْعَصْرِ ﴿١﴾ اِنَّ الْاِنسَانَ لَفِى خُسْرٍ ﴿٢﴾
Ndikulumbilira nthawi, ndithudi munthu ndioluza
Surah iyi ndi surah yaifupi komano ili ndi kufunikira kwambiri kwa munthu. Kufunikira kwa uthenga wa surah imeneyi tikuona kuchokera kwa maswahabah. zikunenedwa kuti padali maswahaba radhwiyallahu anhuma amene adagwirizana pakati pawo kuti akakumana asamasiyane mpakana atawerengerana surah imeneyi kwa wina ndi mnzake kuti azikumbutsana wina ndi mnzake uthenga wabwino wasurayi,
Olemekezeka Imaam Shafi rahimahullah zikunenedwa kuti adati, uthenga wamusurah imeneyi ndiokwanilira ndipo kukanakhala kuti sikunavumbulutsidwe mu Quran uthenga wina, uthenga wa Surah iyi yokha ukanakwanira kukhala chiongoko ku Ummah onse .
Ngati tingalingalire za malumbiliro amene akupezeka musurah imeneyi komanso ndi uthenga wasurayi imene ukutsatira malumbilirowo tikupeza kuti pali mgwirizano waukulu kwambiri pakati pawo.
Poyamba Allah Ta’ala akulumbilira nthawi kenako Allah Ta’ala akukamba za munthu kuti ali oluza. Choncho Allah Ta’ala akutidziwitsa kuti munthu angaziteteze mwa iye yekha pakuluza napeza chipambano ngati angasamale nthawi yake imene ili mpamba wamoyo wake.
Munthu amene amasamala nthawi umoyo wake umakhala opindula ndipo adzapeza maphindu ochuluka kuchokera mu mpamba wake, chimodzimodzinso munthu amene akuononga nthawi yake ndiye kuti akuononga mpamba wake ndiye kuti iye ali oluza kwambiri.
Ndipo pali kusiyana kwakukulu kwa mpamba wa nthawi ndi mipamba ina chifukwa mipamba ina ikaluzika umatha kuyibwezeretsanso. pomwe nthawi ikaluzika singabwezeretsedwenso.
Chilichonse chomwe munthu akufuna kukwaniritsa munthuawi ya mtsogo mwake akuyenera kuchita mu nthawi yoyenerera. Choncho nthawi chilengedwe chake simadikilira munthu komano umangopitilira basi. choncho ngati munthu akufuna kukhala opambana, akuyenera kusamala nthawi iliyonse yamoyo wake.
وَالْعَصْر﴿١﴾ اِنَّ الْاِنسَانَ لَفِى خُسْرٍ﴿٢}
Ndikulumbilira nthawi ndithudi munthu ali oluza
Hadith imanena kuti munthu aliyense amadzuka nthawi ya kummawa namaziguritsa iye mwini kuti apeze chabwino kapena choipa. Ndipo mumawu ena tinganene kuti; amayionongera nthawi yake pochita ntchito zabwino kuti apeze malipilo kwa Allah Ta’ala komanso jannah pa tsiku lachiweruzo. Kapena akuionongera nthawi yake pochita ntchito zoipa kuti apeze chilango cha Allah Ta’ala mdziko lino ndi tsiku lachiweruziro.
Choncho, zili kwa munthu aliyense payekhapayekha kuganizira chomwe akufuna pa umoyo wake zabwino zapadziko pano kapena dziko lomwe lili mkudzalo.
Nthawi sikatundu oti munthu atha kumusunga mukukwanitsa kwake. Chuma monga ngati golide siliva, miyala yamtengo wapatali ndi zina. zikhonza kusamaridwa komano nthawi ili ngati madzi oundana amene akusungunuka pamene kukutentha kwambiri sangathe kutetezeka kapena kusungidwa ndikudzagwiritsa ntchito mtsogolo. choncho, uthenga wamusurah imeneyi ikupereka kwa munthu uthenga kuti munthu athokoze nthawi yake ndikuigwiritsira ntchito moyenerera komanso mopindulitsa.
Munthu omwalira amapemphanso nthawi yoonjezera komanso kumutalikitsira umoyo wake. pamene amayamba kuona zotsatira zamoyo wake, amalakalaka kuti akadapatsidwa nthawi yoonjezera ndicholinga choti athe kukwanitsa kuchita ntchito zabwino. komabe sangapatsidwe nthawi yoowonjezera padziko lino. Choncho munthu akuyenera kukhala othokoza nthawi iliyonse yamoyo wake, ndiponso asamalore nthawi iliyonse yamoyo wake kuonongeka opanda kugwiramo ntchito yabwino ndikukhonzekera zamoyo umene uli mkudza.
اِنَّ الْاِنسَانَ لَفِى خُسْرٍ ﴿٢﴾ إِلَّا الَّذِينَ اٰمَنُوْا وَعَمِلُوْا الصّٰلِحٰتِ
Ndithudi munthu ndi oluza, kupatula omwe akhulupilira ndikumachita ntchito zabwino
Mu surah imeneyi Allah Ta‘ala akufotokoza kuti onse amene sadakhulupilire mwa Allah Ta’ala ndi oluza. Kuyankhula kwina ndiye kuti aononga mpamba wawo wa nthawi yamoyo wawo ndiye kuti iwo ndioluza alibe chipambano.
Funso likubwera kuti zitheka bwanji munthu kupeza zabwino zochuluka kumachita kuti umoyo wathu ndiwaufupi wokhalira padziko pano?.
Allah Ta’ala akuyankhula ntchito zinayi zimene munthu akuyenera kuzichita m’nthawi yake ndicholinga choti apeze phindu loyenera mdziko lino lapansi. munthawi yake. Ngati wina angaigwiritsire ntchito yake moyenerera muntchito zinayizi, ndiye kuti nthawi yake yambiri adzakhala akupanga mpamba wamoyo wake…
Ntchito zinayizo ndi izi:
(1) Kusunga Imaan
(2) Kugwira ntchito zolungama komanso kupewa machimo
(3)Kulimbikitsana kukhala olungama.
(4)Kuthandiza ndikulimbikitsana kupewa machimo ndizoipa.
اِنَّ الْاِنسَانَ لَفِى خُسْرٍ ﴿٢﴾ إِلَّا الَّذِينَ اٰمَنُوْا
Ndithudi munthu ndi oluza, kupatula omwe ali okhulupilila.
Ntchito yoyamba
Chinthu choyamba chomwe munthu akuyenera kukhala nacho ndi Imaan. Munthu amene ali ndi imaan angafaniziridwe ndi munthu amene ali ndi munda waukulu. mmunda umenewo akhonza kulimamo mitengo yazipatso komanso kulimamo mbewu zakumunda, kotero azipezamonso zomuthandiza iye mwini. popanda kukhala ndimalo munthu sangathe kudzala mitengo yazipatso kapena kudzala mbewu iliyonse.
Ngakhale kafiri atamagwira ntchito zabwino zochuluka mu umoyo wake monga kuwachitira chifumdo anthu, kupereka maswadaqah kuthandiza osauka. etc komano kumachita kuti alibe Imaan, ntchito zake zabwinozo zidzakhala zopanda pake komanso zidzakanidwa pa tsiku lachiweruzo.
Ntchito iliyonse kafiri angagwire padziko lino adzalipidwanso padziko pompano ndipo sadzalandila malipiro ndichabwino chirichonse pa tsiku lachiweruzo. Chifukwa chake imaan ndi kiyi yachipambano komanso ndi mtendere waukuulu wa Allah Taala. Choncho chinthu choyambilira chimene munthu akuyenera kukhala nacho ndiye ndi Imaan komanso akuyenera kulimbikira pa imaan yakeyo.
Ndipo munthu akuyenera kudziwa kuti imaan ndi kiyi yantchito iliyonse ndipo ndimtendere waukulu wa Mulungu umene adamupatsa munthu, choncho munthu akuyenera kulemekeza imaan komanso kuyisamala.
Mtumiki wa Allah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anatichenjeza ife kuti nthawi idzafika imene munthu adzaluze imaani yake muusiku umodzi kapena usana wake. Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati munthu adzayamba tsiku lake ali ndi imaan ndipo adzaluza imaani yake madzulo a tsikulo. komanso munthu adzakhala ndi imaan madzulo ndipo pofika mmawa wake munthu adzakhala ataluza Imaan. alibe imaani. Adzaguritsa Dini yake ndi Ulemelero wadziko lapansi. (Saheeh Muslim #118)
Munthu angaluze imaani yake kudzera mnjira yochita zinthu zaharaam ndi kuchita ntchito za uchimo, kapena kukhala limodzi ndi ndi anthu oipa, kumwa mowa kuyenda njuga kuona zithuzi kapena mafilimu olaula ndizina. Pamene munthu akupanga zoipazi, iman yake imakhala yofooka kenako amakhala kutali ndi dini ndiponso amakhala okopeka ndi ntchito zoipa za anthu osakhulupilira. Ndipo pamakhala chiopsezo chachikulu kuti munthu otereyu akhoza kulowa chipembedzo chamakafiri nasiya chisilamu.
اِنَّ الْاِنسَانَ لَفِى خُسْرٍ ﴿٢﴾ إِلَّا الَّذِينَ اٰمَنُوْا وَعَمِلُوْا الصّٰلِحٰتِ
Ndithudi munthu ndi oluza, Kupatula omwe akhulupilira ndikumachita ntchito zabwino.
Ntchito yachiwiri
Ntchito yachiwiri munthu akuyenera kuonongera nthawi yake pogwira ntchito zolungama. Ngakhale imaan ndiye chuma chachikulu kuposa zonse, imaan imaonetsa zizindikiro zake ngati yasakanikirana ndi ntchito zolungama. Zintchito zolungama zimene munthu amachita zimamupangitsa kukhala oyima nganganga panjira ya imaan ndiponso zimamupatsa mwayi kuti apindule ndi imaan.
Mu Quran yolemekezeka kumayambiliro kwa surah mu`min Allah Taala akufotokoza za anthu okalowa ku Jannah ponena kuti “Ndithudi anthu aimaani ndi anthu opambana” pamapeto pake, Allah Taala akulongosora za anthu aimaan polongosora ntchito zawo zomwe amachita pamoyo wawo monga kupemphera moyenelera panthawi yake kupewa ntchito zoipa. kupereka zakat, kupewa chiwerewere komanso kukwaniritsa zomwe alonjeza.
Kumapeto kwa ndimeyi Allah Taala akuti amenewa ndi anthu amene ndi oyenera kukalowa ku Jannah ya firidaus Jannah yapamwamba kwambiri kuposa onse.
Muhadith ina Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati, “pamene nzimayi akupemphera swalah zake zisanu, nasala kudya mwezi wa Ramadhan, naziteteza kuchiwerewere komanso namamvera mwamuna wake, adzalowa mnzimayi ameneyo khomo la Jannah lomwe adzalifune.
Muhadith ina Mtumiki (swallallah alayhi wasallam) akulongosora kuti´palibe tsiku limene dzuwa limatulukamo kupatula kuti tsikulo limalengezetsa nane a kuti; Amene angakwanitse kuchita ntchito yabwino tsiku lalero ayenera kutero, chifukwa ngati ndingachoke sindidzabwereranso.
Choncho munthu akuyenera kuti adzipereke pogwira ntchito zabwino ndikupewa machimo muumoyo wake onse. Mtumiki wa Mulungu (swallallah alayhi wasallama) adati; Munthu amene anganene mawu oti *Laa ilaaaha illallah* moyeretsa mtima)(ikhlaswi) adzalowa ku Jannah. Maswahabah (radhwiyallahu anhum) adafunsa nati; kodi chizindikiro cha ikhlaswi ndichiti pamene munthu ukunena mawu amenewa (kalimah)? Mtumiki wa Mulungu (swallallahu ‘alaihi wasallam) adati; Chizindikiro chosonyeza kuti mawu amenewa wawanena mwa ikhlaswi moyeretsa mtima ndichoti mawu amenewa adzakuteteza kusiya chilichonse chomwe Allah Taala adaletsa.
وَتَوَاصَوْا بالْحَقِّ وَتَوَاصَوْا بالصَّبْرِ ﴿٣﴾
ndipo amalimbikitsana wina ndimnzake kutsatira choonadi komanso namalimbikitsana kupilira (komanso kupewa uchimo)
Ntchito yachitatu ndiyachinayi
Ntchito yachitatu ndiyachinayi ndiko kulimbikitsana zopewa machimo nthawi zonse.
Ngati munthu waigwiritsitsa dini nachita zolungama nthawi zonse namazitalikitsa ku uchimo nakhala osamala moyo wake, munthu otereyunso adzathanso kulimbikitsa ena kuti akhale olungama ngati iye.
Choncho, mndime imeneyi Allah Taala akuyankhula zokhudza kukwaniritsa ntchito zokakamizika ziwiri mwa anthu. Ntchito yoyamba ndikulimbikitsa anthu kuti atsatire choonadi ndi chilungamo, ndipo ntchito yachiwiri ndiko kuwaletsa anthu kuti apewe uchimo ndikuyipa. izi zikutanthauza kuti kukakamizika kowalamulira anthu kuti adzichita zabwino ndikuwaletsa zoyipa.
Mukuyankhula kwina, ngati wina akufuna kuti apeze chipambano chokwanilira, sakuyenera kukhala okhudzidwa zakuchita bwino kwa iye yekha ayi. komano akuyenera kukhuzidwanso mmene akuchitira anthu enanso.
Masiku ano tikupeza kuti anthu ambiri ali okhudzidwa zakulungama ndikuchita bwino kwawo kokha ndipo sakulabadira zokhudza kuchita bwino kwa ena.
Choncho Mndime imeneyi Allah Taala akutidziwitsa kuti monga ngati ife timakhala okhudzidwa zokhuza kupita patsogolo kwa umoyo wathu basi, tikuyeneranso kukhudzidwa kwakukulu zokhuza anthu enanso.