Machimo a zaka 80 akhululukidwa, kulandira malipiro ochita ibaadah kwa zaka 80 kudzera mu kuwerenga Duruud

عن أبي هريرة رضي الله عنه قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: من صلى صلاة العصر من يوم الجمعة فقال قبل أن يقوم من مكانه اللهم صل على محمد النبي الأمي وعلى آله وسلم تسليما غفرت له ذنوب ثمانين عاما وكتبت له عبادة ثمانين سنة (القول البديع صـ 399)

Hazrat Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki sallallahu (sallallahu alaih wasallam) adati: munthu amene angaswali Asr tsiku la Jumuah ndipo kenako ndikuyamba kuwerenga Duruud iyi kokwana ka 80 asadaimilire malo wakhalawo, amakhululukidwa machimo a zaka 80 ndiponso amalipidwa zabwino kukhala ngati wapanga ibaadah kwa zaka 80.

اَللّٰهُمَّ صَلِّ عَلٰى مُحَمَّدٍ النَّبِيِّ الْأُمِّيِّ وَعَلٰى آلِهِ وَسَلِّمْ تَسْلِيْمًا

Allahummah swalli alaa Muhammad nabiyyil ummiyyi waala aalihi waswahbihi wasallim tasliimaa.Oh Allah! Mupatseni zabwino Mtumiki wanu Muhammad akubanja ake ndi ophunzira ake.

Chikondi Cha Sahabah Wina Pa Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasalla)

Munthu wina adafunsa Aliy (radhwiyallahu anhu) kuti, ndi Chikondi chochuluka bwanji chomwe masahabah adali nacho pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)?

Aliy (Radhwiyallahu anhu) adayankha nati, ndikulumbira mwa Allah, Mtumiki  (sallallahu alaih wasallam) adali okondeka kwambiri kwa ife kuposa munthu wachuma, ana athu ndi amayi athu, ndipo kukhala limodzi ndi iye kunali kokoma kuposa kumwa madzi ozizira pamene uli ndi ludzu kwambiri. (As-Shifaa Pg, 52/2)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …