Chikondi cha Hazrat Uthmaan (radhiyallahu anhu) pa Hazrat Rasulullah (sallallahu alaih wasallam)

 

Nthawi ya Hudaybiyah, Hazrat Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) adatumidwa ndi Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) kukakambirana ndi ma Quraish ku Makka Mukarramah. Pamene Hazrat Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) adanyamuka kupita ku Makka Mukarramah, ena mwa maswahabah adamchitira kaduka Uthmaan (radhiyallahu anhu) chifukwa chokwanitsa kuchita tawaaf ya nyumba ya Allah (ka’bah). Komano mthenga wa Allah (sallallahu alaih wasallam) adati, “Sindikuganiza kuti angakwanitse kuchita twawaaf popanda ine.”

Pamene Uthmaan (radhiyallahu anhu) adalowa munzinda wa Makkah Mukarramah, Abaan bin Said adamutenga ndikumuteteza ndipo adati kwa iye: “Ukhoza kuyenda momasuka kulikonse kumene ungafune. Palibe amene angakugwire pano.”

Hazrat Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) adachita zokambilana zake ndi Abu Sufyaan ndi nduna zina za Makkah Mukarramah mmalo mwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), ndipo pamene adatsala pang’ono kubwelera, ma Quraish adamuuza okha kuti: “Tsopano ukakhala kuno ku Makkah Mukarramah ukhoza kuchita tawaaf usanabwerere.” Uthmaan adayankha: “Zingatheke bwanji kwa ine kuchita tawaaf (popanda Hazrat Rasulullah)?”

Yankho limeneli silidawasangalatse ma Quraish ndipo adaganiza zomutsekera Uthmaan ku Makkah Mukarramah. Nkhani idawafikira Asilamu kuti Hazrat Uthmaan waphedwa. Pankhani imeneyi yomwe idafika kwa Hazrat Rasulullah (sallallahu ‘alaihi wasallam), adalumbirira Maswaabah onse kuti amenyane ndi dontho lomaliza la magazi awo. Akuraishi atamva izi khutu lidawagonjetsa ndipo nthawi yomweyo adammasula Uthmaan (radhiyallahu anhu). (Musnad Ahmed, 18910, Kunzul Umaal, 30152)

Check Also

Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) aluza mano ake pa nkhondo ya Uhud

Pankhondo ya Uhud, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamenyedwa koopsa ndi adani ndipo mano awiri …