24. Sizili zoloredwa kumuchotsa munthu pamalo ake mumzikiti cholinga choti akhalepo wina.[1]
عن ابن عمر رضي الله عنهما عن النبي صلى الله عليه وسلم أنه نهى أن يقام الرجل من مجلسه ويجلس فيه آخر ولكن تفسحوا وتوسعوا (صحيح البخاري، الرقم: 6270)
Olemekezeka Ibnu Umar (radhwiyallah anhu) akunena kuti Mtumiki (salallah alayhi wasallama) adaletsa kuchotsedwa munthu wina pamalo ake ndikuti mumthu wina akhale pamalo ake. Choncho anthu akhoze malo oti akhale munthu amene (wabwera kumeneyo ngati zili zotheka kumupangira maloko).
25 Osaongora fungulo zanu (majointi) pamene muli mumzikiti, chimodzimodzinso osalowanitsa zala zanu za dzanja lina muzala za dzanja lina pamene muli mumzikiti.[2]
عن مولى لأبي سعيد الخدري قال بينا أنا مع أبي سعيد رضي الله عنه وهو مع رسول الله صلى الله عليه وسلم إذ دخلنا المسجد فإذا رجل جالس في وسط المسجد محتبيا مشبكا أصابعه بعضها في بعض فأشار إليه رسول الله صلى الله عليه وسلم فلم يفطن الرجل لإشارة رسول الله صلى الله عليه وسلم فالتفت إلى أبي سعيد فقال إذا كان أحدكم في المسجد فلا يشبكن فإن التشبيك من الشيطان وإن أحدكم لا يزال في صلاة ما كان في المسجد حتى يخرج منه (مجمع الزوائد، الرقم: 2047، الترغيب والترهيب، الرقم: 450)
Kapolo omasuridwa wa Olemekezeka Abuu Saeed Khudri (radhiyallahu anhu) akusimba kuti; panthawi ina pamene ndinali ndi Abuu Saeed (radhiyallahu anhu) ndipo iye adali ndi Mtumiki (swallallah alayhi wasallama), tidalowa mumzikiti ndipo tidawona munthu atakhala pakati pa Mzikiti. Munthu ameneyi adakhalira matako ake, maondo ake adawayimika m’mwamba, mikono yake idazungulilitsidwa pogwirizira maondo ake ndipo zala zake za dzanja lake lina adalowanitsa muzala za dzanja lina. Mtumiki (sallallah alayhi wasallama) adampatsa sayini koma munthu uja sadazindikire chomwe Mtumiki (sallallahu alayhi wasallama) amatanthauza. Kenako Mtumiki (sallallahu alayhi wasallama) adatembenukira kwa Abuu Saeed khudir (radhiyallahu anhu) nati; Ngati wina aliyense mwa inu walowa mumzikiti sakuyenera kulowanitsa zala zakumanja zake chifukwa kulowanitsa zala za dzanja lina ndi dzanja lina ndi mchitidwe wa satana. Pamene inu muli mumzikiti kudikilira swalah mudzalandira malipilo a swalah, ngati inuyo muli mu swalayo, mpakana mutatuluka mumzikitimo (choncho ngati mukulowanitsa zala zanu zakumanja pamene muli muswalah ndikusemphana ndimiyambo ya swalah, I choncho musalowanitse zala zamanja pamene mukudikilira swalah).
[1] قال أصحابنا لا يجوز أن يقيم الداخل رجلا من موضعه لما ذكره المصنف وسواء في هذا المسجد وسائر المواضع المباحة التي يختص بها السابق (المجموع شرح المهذب 4/293)
ولا يجوز أن يقيم رجلا من مجلسه ليجلس فيه (التهذيب في فقه الإمام الشافعي 2/351)
[2] اتفق الأصحاب على كراهة تشبيك الأصابع في طريقه إلى المسجد وفي المسجد يوم الجمعة وغيره، وكذا سائر أنواع العبث ما دام في الصلاة أو منتظرها لأنه في صلاة (المجموع شرح المهذب 4/391 ، مغني المحتاج 1/652)
ولا يشبك بين أصابعه ولا يفرقع في الطريق ولا في المسجد كما لا يفعل في الصلاة (التهذيب في فقه الإمام الشافعي 2/351)