Chikondi cha olemekezeka Ali radhwiyallahu anhu pa Mtumiki Muhammad (swallallahu alaih wasallam)

Usiku umene Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) ankasamuka kupita ku Madinah Munawwarah makafiri adazungulira nyumba yake ndicholinga choti amuphe.

Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) asadasamuke adamuuza Ali (radhwiyallahu anhu) kuti akagone ku nyumba ya Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) ndicholinga choti makafiri aganize ngati Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adakali m’nyumba momwemo sadatuluke ndipo sazindikira kuti watulukamo.

Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adamuuza Ali (radhiyallahu anhu) kuti makafiri sakwanitsa kumupha ndipo kuti Allah amuteteza.

Pamenepa Ali (radhiyallahu anhu) ngakhale ankadziwa kuti ali pa chiopsyezo adatsatirabe langizo la Mtumiki (swallallahu alaih wasallam).

Mmenemu ndimmene Ali (radhiyallahu anhu) adadzipelekera umoyo wake pofuna kukwaniritsa langizo la Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) ndicholinga chofuna Kuteteza moyo wake.

Pa chifukwa chimenechi olemekezeka Ali radhwiyallahu anhu ankawerenga ndakatulo iyi:

وقيت بنفسي خير من وطئ الثرى ومن طاف بالبيت العتيق وبالحجر
رسول اله خاف أن يمكروا به فنجاه ذو الطول الإله من المكر
وبات رسول الله في الغار آمنا موقى وفي حفظ الإله وفي ستر
وبتّ أراعيهم وما يتهمونني وقد وطنت نفسي على القتل والأسر

Ndidapeleka moyo pofuna Kuteteza moyo wa munthu olemekezeka kwambiri pa dziko lonse lapansi komanso yemwe adapangaTawaaf pa nyumba yolemekezeka kwambiri ya ka’bah pa Hajar Aswad.

Dzina limeneli silawinanso koma la Mthenga wa Allah madaritso ndi mtendere zipite kwa iye amene adaopa ndale za adani ake, kotero Allah amene ndi tsinde la chisomo chonse adamteteza ku ndale zawo zoipa.

Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adakhala Kuphanga usiku onse mwantendere komanso motetezeka kusangalala mnchitetezo cha namalenga ndimobisala.

Usiku onse ndidakhala ndikuwayang’ana adaniwa omwe sankayembekezera kuti munthu yemwe ali m’nyumbamu ndi ineyo (ndagona malo ake) ndidakonzekera zophedwa kapena kugwidwa.

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …