Machimo a Zaka Makumi asanu ndi atatu Akhululukidwa, sawabu za Zaka Makumi asanu ndi atatu Zilembedwa Kupyolera mu Kubwereza Durood Makumi asanu ndi atatu tsiku Lachisanu

عن أبي هريرة رضي الله عنه قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: الصلاة علي نور على الصراط ومن صلى علي يوم الجمعة ثمانين مرة غفرت له ذنوب ثمانين عاماً أخرجه ابن شاهين في الأفراد وغيرها وابن بشكوال من طريقه وأبو الشيخ والضياء من طريق الدارقطني في الأفراد أيضاً والديلمي في مسند الفردوس وأبو نعيم وسنده ضعيف وهو عند الأزدي في الضعفاء من حديث أبي هريرة أيضاً لكنه من وجه آخر ضعيف أيضاً وأخرجه أبو سعيد في شرف المصطفى من حديث أنس والله أعلم (القول البديع صـ 398)

Hazrat Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akufotokoza kuti Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) adati “kundiwerengera Duruud kudzakhala kuwala pa Mlatho (Paul-Siraat) ndipo amene adzandiwerengere Duruud tsiku lachisanu kokwana makumi asanu ndi atatu (80), adzakhululukidwa zaka makumi asanu ndi atatu za machimo ake.”

Nkhani ya Abu Imraan Waastwii (rahimahullah)

Abu Imraan Waastwii (rahimahullah) akulongosora kuti:

Tsiku lina ndinali pa ulendo wopita ku Madina Tayyibah, ndili m’njira ndinamva ludzu ladzaoneni moti ndinkaopa kumwalira. Poopa kuti imfa yatsala pang’ono kundipeza, ndinakhala pansi pa mtengo waminga.

Mwadzidzidzi munthu wina anabwera ali pa kavalo wagilini, wokhala ndi zingwe zagilini ndi chichalonso chagilini. M’manja mwake munali galasi lagilini lokhala ndi chakumwa chagilini. Ndinamwa katatu ndipo palibe ngakhale dontho lomwe linapunguka. Kenako adandifunsa komwe ndikupita, ndipo ndidayankha kuti ndikupita ku Madina Munawwarah kuti ndikapereke Salaam yanga kwa Nabii (swallallahu alaih wasallam) ndi anzake awiri Abu Bakr ndi Umar (radhwiyallahu anhuma).

Kenako adayankha: “Ukakafika ku Madinah Munawwarah ndikuwalonjera, ukafikitsenso Salaam yanga kwa Nabiy (swallallahu alaih wasallam) ndi anzake awiri. Ukamuuze kuti Ridhwaan akupeleka Salaamu. (Ridwaan ndi mngelo yemwe ndi mlonda wa ku Paradiso).”

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …