Chikondi chopanda malire cha maswahabah pa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam)

Munthu wina adabwera kwa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) nati, Oh Mtumiki wa Allah (swallallahu alaih wasallam) chikondi changa pa inu chili ponena kuti ndikangokuganizani ndimazadzidwa ndi chikondi chopanda malire, ndipo mtima wanga siumakhala mmalo pokhapokha ndikuoneni, Oh Mthenga wa Allah, maganizo amandifika kuti ngati Allah anganditenge ndikukandilowetsa ku Jannah zidzakhala zovuta kwa ine kuti ndidzakuoneni popeza inu mudzakhala Jannah ya pamwamba kwambiri yomwe ine sindingakwanitse kuifika.

Mtumiki swallallahu alaih wasallam adamukhazikitsa mtima pansi pomuwerengera Ayah iyi:

وَمَن يُطِعِ ٱللَّهَ وَٱلرَّسُولَ فَأُو۟لَٰٓئِكَ مَعَ ٱلَّذِينَ أَنْعَمَ ٱللَّهُ عَلَيْهِم مِّنَ ٱلنَّبِيِّنَ وَٱلصِّدِّيقِينَ وَٱلشُّهَدَآءِ وَٱلصَّٰلِحِينَ ۚ وَحَسُنَ أُو۟لَٰٓئِكَ رَفِيقًا ‎﴿٦٩﴾‏

Onse amene amatsatira malamulo a Allah ndikutsatira sunnah ya Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) ali limodzi ndi anthu omwe ali mchisomo cha Allah monga Atumiki, ma Siddiiqiin, anthu ofera ku nkhondo komanso anthu olungama. 

Check Also

Abu Zar (radhiyallahu ‘anhu) Apereka Uphungu kwa Mtsogoleri wa Asilikali Kuti Atsatire Chilungamo

Imaam Bayhaqi (rahimahullah) akunena kuti: Yazid bin Abi Sufyaan (radhiyallahu ‘anhu) pamene adali bwanamkubwa wa …