عن أبي وائل قال : ما شهد عبد الله مجمعا ولا مأدبة فيقوم حتى يحمد الله ويصلي على النبي صلى الله عليه وسلم وإن كان مما يتبع أغفل مكان في السوق فيجلس فيه فيحمد الله ويصلي على النبي صلى الله عليه وسلم (المصنف لابن أبي شيبة، الرقم: 30429، ورواته ثقات)
Hazrat Abu Waail radhwiyallahu anhu anatchulapo kuti: “Sindinamuone Abdullah bun Masuud ali pa msonkhano uliwonse kapena nkumano, koma kuti ankatamanda ndi kulemekeza Allah ndi kumuwerengera Duruud Rasulullah swallallahu alaih wasallam, ndipo ankati akapita ku nsika komwe anthu amanyalanyaza kumkumbukira Allah, amatamanda Allah ndi kukawerenga Durood m’malo amenewo.”
Hazrat Bilaal (radhiyallahu anhu) abwelera kupita ku Madinah Tayyibah
Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) atamwalira zidali zovuta kwambiri kwa Bilaal (radhiyallahu anhu) kuti akhalebe ku Madinah Tayyibah, izi zidali chonchi chifukwa cha chikondi chimene adali nacho pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kukhala ku Madinah zinkamupangitsa kuti azimukumbukira Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) nthawi ina iliyonse.
Kotero adasamuka ku Madinah ndi kuganiza zoyenda mmjira ya Allah moyo wake onse.
Ulendo wina adalota Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) akumuuza kuti “Oh Bilaal! Bwanji kunditalikira chotero (udasiya kundiyendera)? Nthawi yomweyo adauyamba ulendo opita ku Madinah Tayyibah.
Atafika kumeneko, Hassan ndi Husain zidzukulu za Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamupempha kuti apange Adhaan. Sadathe kuwakanira popeza adali okondedwa kwa iye.
Chongopanga Adhaan anthu aku Madinah Tayyibah adalira chifukwa chokumbukira nthawi ya Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Bilaal (radhiyallahu anhu) adanyamukanso patadutsa masiku ochepa ndipo adamwalilira ku Damascus mchaka cha 20 A. H.