Palibe malo mu Chisilamu kwa amene a kunyoza ma Swahaabah (Radhiyallahu anhum)

Tsiku linalake Munthu wina anafika kwa Zainul Aabidiin, Aliy bin Husain rahimahullah ndipo adafunsa:

Oh chidzukulu cha Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) maganizo anu ndi otani pa nkhani ya Uthmaan (radhwiyallahu anhu)?

Atazindikira za nkwiyo wa munthuyu pa Uthmaan (radhwiyallahu anhu, Olemekeza Zainul Aabidiin (rahimahullah)adamulongosolera munthuyo kuti:

Oh m’bale wanga okondeka! Onse pamodzi pali magulu atatu a asilamu omwe atchuridwa mu Qur’an (ma Muhajirina, ma Answaar komanso omwe adabwera pambuyo pa ma Muhajirina ndi Answari mu ntchito zawo zabwino), kenako adafunsa kuti: m’bale wanga! Kodi uli mgulu loyambiliralo? (la ma Muhajirina)omwe Allah akuyankhula mu Qur’an za iwowo.

Allah akuti:

 لِلْفُقَرَآءِ ٱلْمُهَٰجِرِينَ ٱلَّذِينَ أُخْرِجُوا۟ مِن دِيَٰرِهِمْ وَأَمْوَٰلِهِمْ يَبْتَغُونَ فَضْلًا مِّنَ ٱللَّهِ وَرِضْوَٰنًا وَيَنصُرُونَ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥٓ أُو۟لَٰٓئِكَ هُمُ ٱلصَّٰدِقُونَ ‎﴿٨﴾

(muli gawo la chuma) la anthu osaukitsitsa omwe ndi ma Muhajirina omwe adapitikitsidwa mnyumba zawo ndi katundu wawo. (omwe adasamukira ku Madinah Munawwarah ndicholinga chofuna kusakasaka ntendere wa Allah ndi Mtumiki wake komanso Kuthandiza Dini ya Allah. Amenewa ndi omwe ali pa chilungamo”.

Munthu uja adayankha nati: Ayi sindiri mgulu la ma Muhajirina, Olemekezeka Zainul Aabidiin anati: ngati siuli mgulu loyamba lomwe latchuridwa mu Qur’an ndiye kuti uli mgulu lachiwiri la (ma Answaar) omwe Allah akuyankhula zowachemelera iwo mu Qur’an:

Allah akuti:

وَٱلَّذِينَ تَبَوَّءُو ٱلدَّارَ وَٱلْإِيمَٰنَ مِن قَبْلِهِمْ يُحِبُّونَ مَنْ هَاجَرَ إِلَيْهِمْ وَلَا يَجِدُونَ فِى صُدُورِهِمْ حَاجَةً مِّمَّآ أُوتُوا۟ وَيُؤْثِرُونَ عَلَىٰٓ أَنفُسِهِمْ وَلَوْ كَانَ بِهِمْ خَصَاصَةٌ وَمَن يُوقَ شُحَّ نَفْسِهِۦ فَأُو۟لَٰٓئِكَ هُمُ ٱلْمُفْلِحُونَ ‎﴿٩﴾

(mulinso gawo la chuma la) amene adakhala kale mumzinda Uwu (wa Madina) ndi kukhulupirira, Akuwakonda amene adasamukira kwa iwo. Ndipo sakupeza vuto m’mitima mwawo Pazimene anzawo apatsidwa, ndipo Akutsogoza zofuna za anzawo pazawo, Ngakhale iwo akuzifunitsitsa. Amene Atetezedwa (ndi Mulungu) kuumbombo Wa mitima yawo, amenewo ndiwo Opambana.

Munthu uja adayankha nati”. Ayi! Sindilinso mgulu la ma Answaar ”

Zainul Aabidiin adati kwa iye:” ndikulumbira mwa Allah ngati siuli mgulu lachitatuli lomwe Allah akuyankhula mu Qur’an yolemekezeka kuti, ndiye kuti zivute zitani upezeka kunja kwa chisilamu popeza siupezeka mgulu lina lirilonse mmagulu achisilamu atatuwa, gulu lachitatu ndi lomwe Allah akunena kuti;

‏ وَٱلَّذِينَ جَآءُو مِنۢ بَعْدِهِمْ يَقُولُونَ رَبَّنَا ٱغْفِرْ لَنَا وَلِإِخْوَٰنِنَا ٱلَّذِينَ سَبَقُونَا بِٱلْإِيمَٰنِ وَلَا تَجْعَلْ فِى قُلُوبِنَا غِلًّا لِّلَّذِينَ ءَامَنُوا۟ رَبَّنَآ إِنَّكَ رَءُوفٌ رَّحِيمٌ ‎﴿١٠﴾

Ndipo (okhulupirira) amene adadza Pambuyo (pa Amuhajirina ndi Ansari) Akunena kuti: ‘Mbuye wathu Tikhululukireni ndi anzathu amene Adatitsogolera pa chikhulupiriro, ndipo Musaike m’mitima mwathu njiru ndi Chidani kwa amene adakhulupirira. 0, Mbuye wathu! lnu ndinu Wodekha Wachisoni.’

Mukunena kwina titha kunena kuti Olemekezeka Zainul Aabidiin adamulongosolera munthuyu kuti ngati Sali mgulu la ma Muhajirina ndi Answari ndiye kuti akhale nsilamu weniweni akuyenera kuwakonda ma Muhajirina ndi ma Answaar pa nkhani ya Dini.

Check Also

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Awonetsa ku Ummah Udindo olemekezeka wa Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Awonetsa ku Ummah Udindo olemekezeka wa Abu Ubaidah …