عن أنس عن النبي صلى الله عليه وسلم قال: ما من عبدين متحابين في الله يستقبل أحدهما صاحبه فيصافحه ويصليان على النبي صلى الله عليه وسلم إلا لم يفترقا حتى تغفر ذنوبهما ما تقدم منهما وما تأخر (مسند أبي يعلى الموصلي، الرقم: 2960، وفيه درست بن حمزة وهو ضعيف كما في مجمع الزوائد، الرقم: 17987)
Hazrat Anas bun Maalik (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Hazrat Mtumiki (swallallahu alaih wasallam ) adati: “Pamene Asilamu awiri okondana wina ndi mzake (pachifukwa cha Allah) akumana ndi kumuwerengera malonje Mtumiki (Durood) asanasiyane wina ndi mzake, machimo awo a m’mbuyo ndi mtsogolo amakhululukidwa.
Nkhani ya Abu Imraan Waastwii (rahimahullah)
Abu Imraan Waastwii (rahimahullah) akulongosora kuti:
Tsiku lina ndinali pa ulendo wopita ku Madina Tayyibah, ndili m’njira ndinamva ludzu ladzaoneni moti ndinkaopa kumwalira. Poopa kuti imfa yatsala pang’ono kundipeza, ndinakhala pansi pa mtengo waminga.
Mwadzidzidzi munthu wina anabwera ali pa kavalo wagilini, wokhala ndi zingwe zagilini ndi chichalonso chagilini. M’manja mwake munali galasi lagilini lokhala ndi chakumwa chagilini. Ndinamwa katatu ndipo palibe ngakhale dontho lomwe linapunguka. Kenako adandifunsa komwe ndikupita, ndipo ndidayankha kuti ndikupita ku Madina Munawwarah kuti ndikapereke Salaam yanga kwa Nabii (swallallahu alaih wasallam) ndi anzake awiri Abu Bakr ndi Umar (radhwiyallahu anhuma).
Kenako adayankha: “Ukakafika ku Madinah Munawwarah ndikuwalonjera, ukafikitsenso Salaam yanga kwa Nabiy (swallallahu alaih wasallam) ndi anzake awiri. Ukamuuze kuti Ridhwaan akupeleka Salaamu. (Ridwaan ndi mngelo yemwe ndi mlonda wa ku Paradiso).”