Answaari wina agwetsa nyumba pansi

Tsiku liina Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) ankadutsa mumsewu wa Madinah Munawwarah pamene adawona nyumba yomwe inali ndi dome. Adafunsa kwa Swahaabah. “Ichi ndi chiyani?” Anamuuza kuti inali nyumba yatsopano yomangidwa ndi mmodzi wa ma Ansaar. Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) anakhala chete.

Tsiku lina, Answaari amene adamanga nyumbayo adadza kwa Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) ndikumulonjera ndi salaam. Komabe, Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) adatembenuka kumbali. Adabwerezanso Salamu, koma Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) sadayankhenso. Sahaabia uyu adali ndi nkhawa kwambiri chifukwa Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) samayankha salaamu zake.

Pamene adafunsa kwa ma Swahaabah ena, adauzidwa kuti Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) anadutsa pafupi ndi nyumba yatsopano imene anamanga n’kuifunsa. Iye nthawi yomweyo anapita ndikugwetsa nyumba yatsopanoyo pansi, ndipo sanadziwitse Mtumiki (swallallahu alaih wasallam).

Patapita nthawi, Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) anadutsanso njira imeneyo. Iye anafunsa kuti, “Ili kuti nyumba imene ili ndi dome imene ndikumkumbukira kuti tinaiona nthawi mmbuyomu imene tinadutsa pafupi ndi malowa? Swahaabah adamudziwitsa za Answari uja kuti adaigwetsa poona kuti ichi ndi chifukwa chakuipidwa kwa Mtumiki (Swallallahu alaih wasallam). Pa nthawiyi Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) anati, “Chomanga chilichonse (nyumba iliyonse yomangidwa popanda chifukwa chenicheni) idzakhala yolemetsa kwa mwiniwakeyo, kupatula nyumba yomwe ili yofunikira kwambiri.”

Khalidwe la Sahaabi ameneyu linasonyeza chikondi chenicheni ndi kudzipereka. Sahaabayu sadathe kupirira kuipidwa kwa Hazrat Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) ndipo atangoona kuipidwa kwa Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) adachisiya nthawi yomweyo kuchita chilichonse.

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …