Tafseer Ya Surah Ma’un

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ

أَرَأَيْتَ الَّذِي يُكَذِّبُ بِالدِّينِ ‎﴿١﴾‏ فَذَٰلِكَ الَّذِي يَدُعُّ الْيَتِيمَ ‎﴿٢﴾‏ وَلَا يَحُضُّ عَلَىٰ طَعَامِ الْمِسْكِينِ ‎﴿٣﴾‏ فَوَيْلٌ لِّلْمُصَلِّينَ ‎﴿٤﴾‏ الَّذِينَ هُمْ عَن صَلَاتِهِمْ سَاهُونَ ‎﴿٥﴾‏ الَّذِينَ هُمْ يُرَاءُونَ ‎﴿٦﴾‏ وَيَمْنَعُونَ الْمَاعُونَ ‎﴿٧﴾‏

Kodi mwamuona amene akukana (za tsiku la) Chiweruzo? iye ndi Yemwe akukankha (ndi kutsekereza) wa masiye, ndipo salimbikitsa Kudyetsa osauka. Mavuto akulu ali kwa amene akuswali, amene akunyalanyaza Swalah yawo. Iwo amene (amachita zabwino) podzionetsera, ndipo amakana kupereka (kapena kubwereketsa) ziwiya zawo ngakhale zinthu zazing’ono (zomwe anthu akuzifuna).

أَرَأَيْتَ الَّذِي يُكَذِّبُ بِالدِّينِ ‎﴿١﴾‏ فَذَٰلِكَ الَّذِي يَدُعُّ الْيَتِيمَ ‎﴿٢﴾‏ وَلَا يَحُضُّ عَلَىٰ طَعَامِ الْمِسْكِينِ ‎﴿٣﴾‏

Kodi wamuona amene akutsutsa za Chiweruzo? Iye ndi Yemwe akubweza (ndi kutsekereza) wa masiye, ndipo salimbikitsa Kudyetsa osauka.

Mawu oti ‘Deen’ ali ndi matanthauzo osiyanasiyana. Tanthauzo limodzi ndi Deen ya chisilamu. Tanthauzo lachiwiri ndi chiweruzo. Choncho Aayah iyi ikhoza kutanthauza kuti munthu wosakhulupirira amene wakana chipembedzo cha Chisilamu kapena tsiku lachiweruzo. Malinga ndi malipoti ena, aya zoyambilira zidavumbulutsidwa ponena za kafiri otchedwa Aas bun Waa’il yemwe adali wodziwika kuti adali woipa. Komabe surayi siili kwa iye yekha ndipo uthenga wa surayi ndi wamba komanso ukukhudzanso Asilamu. Choncho, nawonso Asilamu atengepo phunziro m’sura imeneyi ndi kusiya kuchita zoipa monga kunyoza ana amasiye kapena kusiya kudyetsa masikini (anthu osauka.

Kusiyana kwakukulu pakati pa wokhulupirira ndi wosakhulupirira ndiko kukhulupirira tsiku lachiweruzo ndi kuopa kuyankha mlandu pa tsiku lomaliza. Kafiri sakhulupirira za tsiku lachiweruzo, choncho saopa kuyankha mlandu pa tsiku lomaliza. Komabe, pankhani ya wokhulupirira woona, ndiye kuti nthawi iliyonse amakhala akuzindikira kuti Allah Ta’ala akumuyang’ana ndipo adzayenera kuwerengedwa zochita zake zonse posayang’ana kuchepa kapena kukula kwake pa tsiku la Qiyaamah.

Popeza kafiri sakhulupirira mwa Allah Taala ndipo saopa kuwerengedwa pa tsiku la Qiyaamah, amaziona kuti ali ndi mphamvu. Iye sadera nkhawa za ana amasiye ndi masikini ndi anthu osauka ndipo akupitirizabe kutengeka ndi chuma ndi mphamvu zomwe ali nazo, kuiwala kuti zinthu zingasinthe mtsogolo mwake, ndipo Allah Taala akhoza kuwadalitsa ndi chuma ndi kuwachotsera chuma chomwe ali nachocho. M’mawu ena, olemera angakhale osauka mawa, ndipo osauka angakhale olemera mawa.

Choncho, m’ma aya awa Allah Ta’la waipanga kukhala tcheru ku zinthu zoipazi zokanira tsiku lachiweruzo, kunyozera mwana wamasiye ndi kusiya kudyetsa masikini, ndipo akuwalimbikitsa okhulupirira kuti achitire chifundo amasiye, masikini ndi amphawi.

فَوَيْلٌ لِّلْمُصَلِّينَ ‎﴿٤﴾‏ الَّذِينَ هُمْ عَن صَلَاتِهِمْ سَاهُونَ ‎﴿٥﴾‏ الَّذِينَ هُمْ يُرَاءُونَ ‎﴿٦﴾‏ وَيَمْنَعُونَ الْمَاعُونَ ‎﴿٧﴾

Chionongeko chili kwa amene akuswali, amene akunyalanyaza Swalah yawo. Iwo amene (amachita zabwino) modzionetsera, ndipo amakana kupereka (kapena kubwereketsa) ziwiya zawo ngakhale titakhala tinthu ting’onoting’ono (zomwe anthu akuzifuna).

M’ndime izi Allah Ta’ala akunena za anthu okhulupirira amene amanyalanyaza Swalah yawo ndi kuwachitira zoipa anthu. Akaimirira kuti aswali, saswali ndi mtima wodzipereka. Koma iwo amaswali basi ndi cholinga chofuna kuti anthu awaone ngati Asilamu oopa Mulungu. Choncho, akakhala kuti sali pamaso pa anthu, ndiye kuti saswali Swalah yawo, kapena amaswali Swalaah yawo pambuyo pa nthawi ya Qadha, kapena saswali momwe ikuyenera kukhalira ndi kaimidwe koyenera, nthawi yolondola, ndi jamaat mu musjid ndi zina zotero. Choncho, zoona zake n’zakuti alibe chikondi chenicheni ndi kukhudzika pa nkhani ya Swalah m’mitima mwawo.

Mofananamo, iwo ndi oipa ndipo amakana kupereka anthu ngakhale zinthu zofunika, zazing’ono zomwe anthu akufunikira. Mawu oyambirira amene anagwiritsidwa ntchito m’ndime imeneyi ndi “maa’uun”. kutanthauza ‘zinthu zazing’ono ndi zotchipa’, monga mbiya, mchere, shuga, ndi zina zotero.

Mawu oti maa’uon athanso kunena za zakaat. Mu kuyankhula kwina, anthu amenewa amakana kupereka zakaat yawo yokakamizidwa. Izi zanenedwa kuchokera kwa Hazrat Ali (Radhiyallahu anhu) yemwe wanena kuti liwu loti maa’uon m’ndime iyi likunena za zakaat, chifukwa imalipidwa pang’ono poyerekezera ndi chuma chonse cha munthu.

Momwemonso, ayenera kukhudzidwa ndi kukwaniritsa maufulu omwe ali nawo kwa anthu ndi kuchitira chifundo banja lake, anansi, abwenzi, ana amasiye, osowa ndi osauka. Ngati munthu achita zoipa ndiye kuti sangakwaniritse zoyenera za Allah Ta’ala m’chuma chake popereka zakaat, ndiponso sadzakwaniritsa zoyenera zomwe ali nazo akapolo a Allah Ta’ala pokwaniritsa maufulu omwe ali nawo kwa osauka ake. achibale, anansi, etc.

Nthawi ina Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adali paulendo ndipo adalangiza kuti amene ali ndi chokwera choonjezera athandize amene alibe.

Hazrat Abu Said (Radhiya Allaahu ‘anhu) adati: “Nthawi ina tidali paulendo ndi Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) ndipo mwadzidzidzi munthu wina adakwera m’chombocho adadza kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam). Munthuyo anali m’mabvuto ndipo ankayang’ana kumanja ndi kumanzere kuti awone ngati pali amene angamuthandize kukwaniritsa zosowa zake. Pa nthawiyi Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adawalimbikitsa ma Swahaabah (Radhiyallahu ‘anhum) kuti: “Amene ali ndi chokwera choonjezera athandize amene alibe. Amene ali ndi chakudya athandizw yemwe alibe. Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adapitiliza kutchula chuma chamitundumitundu (chomwe munthu angapereke pa sadaqah), ndikuwalimbikitsa ma Swahaabah (Radhiya Allahu ‘anhum) kuti apereke mpaka tinkamuona ngati amene ali nacho chilichonse chopyolera zosoŵa zake alibe ufulu wosunga (mmalo mwake, azigawira osowa). (Saheeh Muslim #1728)

Kuchokera mu Hadith iyi, tikumvetsa kuti khalidwe la okhulupirira ndi loti asakhale wodzikonda komanso wodzitukumula, komanso kudera nkhawa za kupita patsogolo kwakuthupi kwa iye ndi banja lake. M’malo mwake, iye amada nkhaŵa ndi Asilamu onse ndipo amafunafuna mipata yothandizira anthu. Chifukwa chake, munthu wotero amakhala wokonzeka nthawi zonse kuthandiza anthu omwe amakhala pafupi naye ndipo amamukomera mtima onse, kaya akhale achibale, oyandikana nawo, abwenzi ngakhalenso osauka ndi osowa.

Check Also

Tafseer ya Surah Ikhlaas

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ قُلْ هُوَ اللَّهُ أَحَدٌ ‎﴿١﴾‏ اللَّهُ الصَّمَدُ ‎﴿٢﴾‏ لَمْ يَلِدْ وَلَمْ يُولَدْ ‎﴿٣﴾‏ وَلَمْ يَكُن لَّهُ كُفُوًا …