Olemekezeka Abu Bakr (Radhwiyallahu anhu) Kupereka Chuma Chake Kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)

Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallah alayhi wasallam) adati: “Palibe chuma cha munthu chomwe chidandipindulira monga chuma cha Abu Bakr (radhiyallahu anhu), atamva izi olemekezeka Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) adayamba kulira nati: “Chuma changa ndi zonse ndi zanu.

Pali nkhani ya olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) m’buku lotchedwa Musnad Ahmed, Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adati: “Palibe chuma (cha munthu) chomwe chidandipindulira monga chuma cha Abu Bakr (radhiyallahu anhu), Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) atamva izi anayamba kulira ndipo adati katatu: “Oh, Mtumiki wa Allah (swallallahu alaih wasallam)! Ndithudi, kupyolera mwa inu Allah wandidalitsa ine ndi chilichonse.”

Check Also

Kudziwa Kwambiri Dini kwa Muaaz bin Jabal (radhwiyallahu ‘anhu)

Abu Muslim Khowlaani (rahimahullah) akufotokoza kuti: “Ndinalowa mumzikiti wa Hims ndipo ndinaona gulu la anthu. …