Qiyaam

10. Mukangoiyamba swalah yanu werengani Duaa-ul Istiftaa chamuntima.

وَجَّهْتُ وَجْهِيَ لِلَّذِيْ فَطَرَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ حَنِيْفًا مُسْلِمًا وَمَا أَنَا مِنَ الْمُشْرِكِيْنَ إِنَّ صَلَاتِيْ وَنُسُكِيْ وَمَحْيَايَ وَمَمَاتِيْ لِلّٰهِ رَبِّ الْعَالِمِيْنَ لَا شَرِيْكَ لَهُ وَبِذلِكَ أُمِرْتُ وَأَنَا مِنَ الْمُسْلِمِيْنَ

Ndikuyang’ana nkhope yanga kwa Yemwe adalenga thambo ndi nthaka, ndikukhala panjira yoongoka popanda kusokonekera, mogonjera kotheratu, ndipo ine sindine mmodzi wa ophatikiza Allah ndi Ndithu zina, Swalaah yanga, miyambo yanga, moyo wanga pamodzi ndi kumwalira kwanga ndi za Allah, Mbuye wa zolengedwa. Iye alibe wothandizana naye, ndipo izi ndi zomwe ndalamulidwa, ndipo ine ndiri mwa ogonjera kwa Allah.

11. Muwerengenso Ta’awwudh. Ta’awwudh ndikuwerenga motere:

أَعُوذُ بِاللَّهِ مِنَ الشَّيْطَانِ الرَّحِيمِ

Ndikudzitchinjiriza mwa Allah kuchokera kwa Satana wotembereredwa.

Dziwani: Dua-ul Istiftaah ndi Ta’awwudh idzawerengedwa ndi munfarid (omwe akuswali payekhapayekha) komanso Imaam ndi muqtadi (otsatira Imaam).

Check Also

Rakaah Yachiwiri

1. Mukamanyamuka pa sajdah, choyamba nyamulani chipumi ndi mphuno, kenako zikhato ndikumalizira mawondo. 2. Pamene …