Hazrat Abu Bakr Siddeeq (Radhwiyallahu ‘anhu) ali m’phanga la Thaur

Ali kuphangako paulendo wa Hijrah, zikunenedwa kuti Hazrat Abu Bakr Siddeeq (radhwiyallahu anhu) adali ndi nkhawa kuti palibe cholengedwa chomwe chingatuluke mu dzenje lililonse la mphangamo ndi kuvulaza Hazrat Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam). Choncho, anayamba kutseka mabowo onse a m’phangamo ndi zidutswa za malaya ake apansi. Komabe, padali mabowo awiri omwe sadathe kutseka (chifukwa chosowa zovala), choncho Hazrat Abu Bakr Siddeeq (Radhwiyallahu ‘anhu) adayika mapazi ake onse m’mabowomo. Pambuyo pake, Hazrat Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adayika mabaarak mutu wake pantchafu za Hazrat Abu Bakr Siddeeq (Radhiyallahu ‘anhu) ndipo anagona.

Pamene Hazrat Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adali mtulo, Hazrat Abu Bakr Siddeeq (Radhiyallahu anhu) adamva kulumidwa phazi lake ndi njoka m’dzenjemo. Posafuna kusokoneza tulo ta Hazrat Rasulullah (Swallallaahu ‘alaih wasallam) ngakhale pang’ono. Hazrat Abu Bakr Siddeeq (Radhwiyallahu ‘anhu) anapirira ululuwo ndipo sanasunthe ngakhale inchi imodzi. Komabe, chifukwa cha ululu waukulu komanso kulephera kupirira zotsatira zake, misozi inayamba kutsika mosatonthozeka pankhope ya Hazrat Abu Bakr Siddeeq (radhwiyallahu ‘anhu) ndi kugwera pa mubarak nkhope ya Hazrat Rasulullah (Swallallaahu alaih wasallam).

Hazrat Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adadzuka mwadzidzidzi nafunsa kuti: “Kodi chachitika ndi chiyani ee iwe Abu Bakr?” Hazrat Abu Bakr Siddeeq (Radhwiyallaahu ‘anhu) adayankha: “Ndalumidwa, makolo anga aperekedwe nsembe chifukwa cha inu oh Mtumiki (Swallallaahu alaih wasallam)!” Kenako Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adayika malovu ake pa malo okhudzidwawo, ndipo nthawi yomweyo ululuwo udatha.

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …